Kudyetsa Anthu Ambili Mwa Kugwilitsila Nchito Anthu Ocepa
“[Yesu] ananyema-nyema mitanda ya mkate ija n’kupatsa ophunzilawo, ndipo ionso anagaŵila khamulo.”—MAT. 14:19.
KODI MUNGAYANKHE BWANJI?
Kodi ndi njila yotani imene Yesu anagwilitsila nchito kudyetsa makamu a anthu?
Kodi Yesu anawagwilitsila nchito bwanji atumwi ndi akulu ku Yerusalemu?
Kodi nthawi yoyenela yakuti Kristu akhazikitse njila yolinganizika yogaŵila cakudya ca kuuzimu inali iti?
1-3. Fotokozani mmene Yesu anadyetsela khamu lalikulu la anthu pafupi ndi Betsaida. (Onani cithunzi-thunzi cili kuciyambi kwa nkhani ino.)
GANIZILANI cocitika ici. (Ŵelengani Mateyu 14:14-21.) Mwambo wa Pasika wa mu 32 C.E. unali pafupi kucitika. Khamu la amuna pafupi-fupi 5,000, kupatulapo akazi ndi ana aang’ono, linali ndi Yesu ndi ophunzila ake ku malo opanda anthu. Malo amenewo anali kufupi ndi mudzi wa Betsaida umene unali kumpoto, m’mphepete mwa Nyanja ya Galileya.
2 Pamene Yesu anaona khamu la anthu amenewo, iye anawamvelela cisoni. Conco, anacilitsa odwala ao ndi kuwaphunzitsa zinthu zambili zokhudza Ufumu wa Mulungu. Pamene kunali pafupi kuda, ophunzila ake anamuza kuti awalole anthuwo kupita ku midzi yapafupi kuti akagule cakudya. Koma Yesu anauza ophunzila ake kuti: “Inuyo muwapatse cakudya.” Mwacionekele, io anadabwa nao mau ake cifukwa cakuti cakudya cimene anali naco cinali cocepa kwambili. Panali cabe mitanda ya mkate isanu ndi tunsomba tuŵili.
3 Pogwidwa ndi cifundo, Yesu anacita cozizwitsa. Ndipo cimeneco ndi cozizwitsa cokha cimene cinalembedwa ndi alembi onse anai a Mauthenga Abwino. (Maliko 6:35-44; Luka 9:10-17; Yoh. 6:1-13) Yesu anauza ophunzila ake kuti auze anthuwo kukhala m’magulu, ena anthu 50 ndi ena 100 pa udzu wobiliwila. Pambuyo popempha dalitso, iye anayamba kunyema-nyema mkateyo ndi kudula-dula nsombazo. Ndiyeno, m’malo mwakuti iye mwini apeleke cakudyaco, Yesu anapeleka ‘kwa ophunzila ake kuti io acipeleke kwa anthuwo.’ Mwanjila yozizwitsa, panapezeka cakudya coculuka cakuti aliyense anadya ndipo cinatsalako. Tangoganizilani! Yesu anadyetsa anthu ambili mwa kugwilitsila nchito anthu ocepa. Anthu ocepa amenewo anali ophunzila ake.a
4. (a) Kodi Yesu anali kudela nkhawa kwambili ponena za kugaŵila cakudya cotani? Ndipo n’cifukwa ciani? (b) Kodi m’nkhani ino ndi yotsatila tidzakambilana ciani?
4 Koma Yesu anali kudela nkhawa kwambili ponena za kugaŵila otsatila ake cakudya ca kuuzimu. Iye anali kudziŵa kuti kudya cakudya ca kuuzimu, kapena kuti coonadi ca m’Mau a Mulungu, kumatsogolela ku moyo wosatha. (Yoh. 6:26, 27; 17:3) Cifukwa ca cifundo cimodzi-modzi cimene cinam’pangitsa kuti agaŵile makamu a anthu mkate ndi nsomba, Yesu anagwilitsila nchito maola ambili kuphunzitsa otsatila ake. (Maliko 6:34) Koma iye anali kudziŵa kuti adzakhala nthawi yocepa padziko lapansi ndipo pambuyo pake adzabwelela kumwamba. (Mat. 16:21; Yoh. 14:12) Kodi zikanatheka bwanji kuti Yesu asamalile otsatila ake pamene iye ali kumwamba? Ndi mwa kutsatila njila yofanana ndi imene anagwilitsila nchito podyetsa makamu. Njila imeneyo ndi yogwilitsila nchito anthu ocepa kudyetsa anthu ambili. Kodi anthu ocepa amenewo anali ndani? Tiyeni tione mmene Yesu anagwilitsila nchito anthu ocepa kudyetsa otsatila ake odzozedwa ambili m’nthawi ya atumwi. Ndiyeno, m’nkhani yotsatila tidzakambitsilana funso lofunika kwambili kwa aliyense wa ife lakuti: Kodi anthu ocepa amene Kristu akuwagwilitsila nchito kutidyetsa masiku ano tingawadziŵe bwanji?
YESU ASANKHA ANTHU OCEPA
5, 6. (a) Kodi ndi cosankha cacikulu citi cimene Yesu anapanga kuti otsatila ake adzadyetsedwe bwino mwa kuuzimu iye akadzafa? (b) Kodi Yesu anawakonzekeletsa bwanji atumwi ake kuti adzagwile nchito yofunika kwambili pambuyo pakuti iye wafa?
5 Tate wabwino amakonza zinthu kuti banja lake lisakavutike iye akadzamwalila. Mofananamo, Yesu amene anali kudzakhala Mutu wa mpingo wacikristu, anakonza zinthu kuti otsatila ake akasamalidwe mwa kuuzimu iye akadzamwalila. (Aef. 1:22) Mwacitsanzo, zaka pafupi-fupi ziŵili Yesu asanaphedwe, anapanga cosankha cacikulu kwambili. Iye anasankha anthu ocepa amene mtsogolo anali kudzawagwilitsila nchito kudyetsa anthu ambili. Taganizilani zimene zinacitika.
6 Pambuyo popemphela usiku wonse, Yesu anasonkhanitsa ophunzila ake ndipo anasankha atumwi 12 pakati pao. (Luka 6:12-16) Kwa zaka ziŵili zotsatila, iye anali kukonda kwambili atumwi 12 amenewo, ndipo anali kuwaphunzitsa mwa mau ndi citsanzo. Iye anadziŵa kuti panali zambili zimene io anafunika kuphunzila, ndipo io anapitiliza kuchedwa kuti “ophunzila.” (Mat. 11:1; 20:17) Anawapatsa uphungu wothandiza ndi kuwaphunzitsa zinthu zambili zokhudza ulaliki. (Mat. 10:1-42; 20:20-23; Luka 8:1; 9:52-55) N’zoonekelatu kuti Yesu anali kuwakonzekeletsa kaamba ka nchito yofunika kwambili imene io anali kufunika kucita pambuyo pakuti iye wafa ndi kupita kumwamba.
7. Kodi Yesu anaonetsa bwanji cimene cinayenela kukhala cofunika kwambili kwa atumwi?
7 Kodi ndi udindo wotani umene atumwi anali kudzakhala nao? Pamene mwambo wa Pentekosite wa mu 33 C.E. unayandikila, zinali zoonekelatu kuti atumwi adzakhala ndi ‘udindo woyang’anila.’ (Mac. 1:20) Koma kodi n’ciani cimene atumwi anayenela kuona kukhala cofunika kwambili? Pamene Yesu anaukitsidwa, iye anauza mtumwi Petulo zinthu zimene zimatithandiza kudziŵa yankho la funso limeneli. (Ŵelengani Yohane 21:1, 2, 15-17.) Pamaso pa atumwi ena, Yesu anauza Petulo kuti: “Dyetsa ana a nkhosa anga.” Motelo, Yesu anaonetsa kuti atumwi ake adzakhala ena mwa anthu ocepa amene iye adzagwilitsila nchito kudyetsa anthu ambili cakudya ca kuuzimu. Zimenezi ndi zolimbikitsa kwambili ndipo zitionetsa kuti Yesu amasamalila “ana a nkhosa” ake.b
KUDYETSA ANTHU AMBILI KUYAMBILA PA PENTEKOSITE MPAKA MTSOGOLO
8. Pa Pentekosite, kodi okhulupilila atsopano anaonetsa bwanji kuti anali kudziŵa bwino njila imene Kristu anali kugwilitsila nchito?
8 Kuyambila pa Pentekosite mu 33 C.E., Kristu amene anali ataukitsidwa, anagwilitsila nchito atumwi monga njila yogaŵila cakudya ca kuuzimu kwa ophunzila ena odzozedwa. (Ŵelengani Machitidwe 2:41, 42.) Njila imeneyo inali yodziŵika bwino kwa Ayuda ndi kwa anthu oloŵa Ciyuda amene anakhala Akristu odzozedwa ndi mzimu patsikulo. Mosazengeleza, io “anapitiliza kulabadila zimene atumwiwo anali kuphunzitsa.” Malinga ndi katswili wina, liu la Cigiriki limene analitembenuza kuti “anapitiliza kulabadila,” lingatanthauze kukhala “okhulupilika nthawi zonse ndi wa maganizo osumika pa cinthu cimodzi pocita zinthu.” Okhulupilila atsopano amenewo anali ndi njala yaikulu ya cakudya ca kuuzimu, ndipo anali kudziŵa bwino kumene angacipeze. Mokhulupilika, io anali kudalila atumwi kuti awafotokozele tanthauzo la mau ndi zocita za Yesu. Anali kuwadalilanso kuti awathandize kumvetsetsa mfundo zina za m’malemba zimene zimanena za iye.c—Mac. 2:22-36.
9. Kodi atumwi anaonetsa bwanji kuti anali kuona udindo wao wodyetsa nkhosa za Yesu kukhala wofunika kwambili?
9 Atumwi anaona udindo wao wodyetsa nkhosa za Yesu kukhala wofunika kwambili. Mwacitsanzo, onani mmene anathetsela nkhani imene inabuka mumpingo watsopano umenewo, imene inali yovuta ndipo ikanabweletsa magaŵano. Nkhani imeneyo inali yokhudza cakudya cakuthupi. Akazi amasiye olankhula Cigiriki anali kunyalanyazidwa pa kagaŵidwe ka cakudya ca tsiku ndi tsiku, koma akazi amasiye olankhula Ciheberi anali kupatsidwa. Kodi atumwi anaithetsa bwanji nkhani yovuta imeneyi? “Atumwi 12 aja” anaika abale 7 oyenelela kuti akhale oyang’anila nchito yogaŵila cakudya imene inali ‘nchito yofunika.’ Ambili mwa atumwiwo anagwilako nchito yogaŵila khamu la anthu cakudya cimene Yesu anawapatsa mwa njila yozizwitsa. Koma io anaona kuti cofunika kwambili cinali nchito yopeleka cakudya ca kuuzimu. Conco, anadzipeleka pa “utumiki wokhudza mau a Mulungu.”—Mac. 6:1-6.
10. Kodi Kristu anagwilitsila nchito bwanji atumwi ndi akulu ku Yerusalemu?
10 Pofika mu 49 C.E., akulu ena oyenelela anagwilizana ndi atumwi amene anali akali moyo kuti azigwilila nchito pamodzi. (Ŵelengani Machitidwe 15:1, 2.) “Atumwi ndi akulu ku Yerusalemu” anali kutumikila monga bungwe lolamulila. Monga Mutu wa mpingo, Kristu anagwilitsila nchito gulu locepa limenelo la amuna oyenelela kuti athetse mikangano yokhudza ziphunzitso, ndi kuti aziyang’anila ndi kutsogolela nchito yolalikila ndi kuphunzitsa uthenga wabwino wa Ufumu.—Mac. 15:6-29; 21:17-19; Akol. 1:18.
11, 12. (a) Kodi n’ciani cimene cimaonetsa kuti Yehova anadalitsa njila imene Mwana wake anagwilitsila nchito kupeleka cakudya ca kuuzimu ku mipingo ya m’nthawi ya atumwi? (b) Kodi njila imene Kristu anali kugwilitsila nchito kupeleka cakudya ca kuuzimu inali kudziŵika bwino motani?
11 Kodi Yehova anadalitsa njila imene Mwana wake anali kugwilitsila nchito kudyetsa Akristu m’mipingo ya m’nthawi ya atumwi? Inde anatelo. Kodi tingatsimikizile bwanji zimenezo? Buku la Machitidwe limatiuza kuti: “Popitiliza ulendo wao [mtumwi Paulo ndi anzake] m’mizinda, anali kupatsa okhulupilila a kumeneko malamulo oyenela kuwatsatila, malinga ndi zimene atumwi ndi akulu ku Yerusalemu anagamula. Conco mipingo inapitiliza kulimba m’cikhulupililo ndipo ciŵelengelo cinapitiliza kuonjezeka tsiku ndi tsiku.” (Mac. 16:4, 5) Onani kuti mipingo imeneyo inakula ndi kulimba cifukwa cogwilizana mokhulupilika ndi bungwe lolamulila ku Yerusalemu. Kodi umenewu si umboni wakuti Yehova anadalitsa njila imene Mwana wake anali kugwilitsila nchito kudyetsa Akristu m’mipingo? Tiyenela kukumbukila kuti mipingo imakula ndi kulimba kokha cifukwa ca dalitso la Yehova.—Miy. 10:22; 1 Akor. 3:6, 7.
12 Conco, taona kuti Yesu anali kugwilitsila nchito njila ina yake kuti adyetse otsatila ake cakudya ca kuuzimu. Njila imeneyo inali ya kugwilitsila nchito anthu ocepa kudyetsa anthu ambili. Ndipo njilayo inali yodziŵika bwino kwambili. Atumwi amene anali mamembala oyambilila a bungwe lolamulila, anapeleka umboni wooneka bwino wakuti anali kutsogoleledwa ndi Mulungu. Lemba la Machitidwe 5:12 limati: “Atumwiwo anapitiliza kucita zizindikilo ndi zodabwitsa zambili pakati pa anthu.”d Conco, panthawiyo panalibe cifukwa cakuti anthu amene anakhala Akristu adzifunse kuti, ‘Kodi ndani kweni-kweni amene Kristu akugwilitsila nchito kudyetsa nkhosa zake?’ Koma ca kumapeto kwa nthawi ya atumwi, zinthu zinasintha.
PAMENE NAMSONGOLE ANALI WOCULUKA KUPOSA TILIGU
13, 14. (a) Kodi Yesu anapeleka cenjezo lotani lokhudza kuukilidwa kwa mpingo? Ndipo mau ake anayamba kukwanilitsidwa liti? (b) Kodi mpingo unaukilidwa kucokela ku mbali ziŵili ziti? (Onani mau akumapeto.)
13 Yesu analosela kuti mpingo wacikristu udzaukilidwa. Kumbukilani kuti m’fanizo lake la ulosi lonena za tiligu ndi namsongole, Yesu anapeleka cenjezo lakuti namsongole (Akristu onama) adzafesedwa m’munda wa tiligu (Akristu odzozedwa). Iye anakamba kuti mbeu za mitundu iŵili zimenezo adzazileka kuti zikulile pamodzi mpaka nthawi yokolola, imene idzacitika pa “mapeto a nthawi ino.” (Mat. 13:24-30, 36-43) Sipanapite nthawi yaitali kuti mau a Yesu amenewo ayambe kukwanilitsidwa.e
14 Ampatuko anayamba kuonekela m’nthawi ya atumwi, koma atumwi a Yesu okhulupilika anali ngati “coletsa” kuti mpingo usaipitsidwe ndi ziphunzitso zabodza. (2 Ates. 2:3, 6, 7) Komabe, pamene mtumwi womaliza anafa, ampatuko anazika mizu ndi kuculuka kwambili. Zimenezo zinacitika kwa zaka zambili. Ndipo panthawi imeneyo namsongole anaculuka kuposa tiligu. Panalibe njila yodalilika ndi yolinganizika yogaŵila cakudya ca kuuzimu. Koma zimenezo zinali kudzasintha m’kupita kwa nthawi. Kodi zimenezo zinali kudzacitika liti?
KODI NDANI ADZADYETSA ANTHU PA NTHAWI YOKOLOLA?
15, 16. Kodi khama lophunzila Malemba la Ophunzila Baibo linali ndi zotsatilapo zotani? Nanga pakubuka funso lotani?
15 Cakumapeto kwa nyengo ya kukula kwa tiligu ndi namsongole, anthu ena anayamba kukhala ndi cidwi cacikulu cofuna kudziŵa coonadi ca m’Baibo. Kumbukilani kuti m’zaka za m’ma 1870, anthu ocepa amene anali kufunitsitsa kudziŵa coonadi anayamba kukumana kuti aphunzile Baibo. Iwo sanali kukumana pamodzi ndi anthu okhala ngati namsongole kapena kuti Akristu onama a m’Machalichi Acikristu. Ophunzila Baibo oona mtima amenewo anali ndi mitima yodzicepetsa ndi maganizo oyenela, ndipo mwapemphelo anali kufufuza Malemba mosamalitsa.—Mat. 11:25.
16 Khama lophunzila Malemba la Ophunzila Baibo amenewo, linali ndi zotsatilapo zabwino kwambili. Amuna ndi akazi okhulupilika amenewo anavumbula ziphunzitso zabodza, ndipo analalikila coonadi ca m’Baibo mwa kusindikiza ndi kugaŵila mabuku ofotokoza Baibo kumadela osiyana-siyana ndi akutali. Nchito yao inakopa ndi kukhutilitsa anthu ambili amene anali ndi njala ndi ludzu la coonadi ca m’Baibo. Pamenepa pangabuke funso locititsa cidwi lakuti, Kodi Ophunzila Baibo amene analiko 1914 isanafike, anali njila imene Kristu anali kugwilitsila nchito kudyetsa nkhosa zake? Iyai. Iwo anali akali m’nyengo ya kukula, ndipo nchito yokonza njila yopelekela cakudya ca kuuzimu inali ikali mkati. Nthawi inali isanakwane yakuti Akristu onama amene anali monga namsongole awacotse pakati pa Akristu oona amene anali monga tiligu.
17. Kodi ndi zocitika zofunika ziti zimene zinayamba kucitika mu 1914?
17 Monga mmene tinaphunzilila m’nkhani yapita, nthawi yokolola inayamba mu 1914. M’caka cimeneco, zinthu zingapo zofunika zinayamba kucitika. Yesu anaikidwa kukhala Mfumu, ndipo masiku otsiliza anayamba. (Chiv. 11:15) Kuyambila mu 1914 mpaka kuciyambi kwa 1919, Yesu anabwela pamodzi ndi Atate ake kudzagwila nchito yofunika kwambili yoyendela ndi yoyeletsa kacisi wa kuuzimu.f (Mal. 3:1-4) Ndiyeno kuyambila mu 1919, nthawi inakwana yakuti nchito yokolola tiligu iyambe. Kodi imeneyo inali nthawi yakuti Kristu akhazikitse njila yolinganizika yogaŵila cakudya ca kuuzimu? Inde.
18. Kodi Yesu ananenelatu kuti adzakhazikitsa ciani? Pamene masiku otsiliza anangoyamba, kodi panabuka funso lofunika liti?
18 Mu ulosi wake wonena za masiku otsiliza, Yesu ananena kuti adzakhazikitsa njila imene adzagwilitsila nchito kugaŵila ‘cakudya ca kuuzimu pa nthawi yoyenela.’ (Mat. 24:45-47) Kodi anali kudzagwilitsila nchito njila iti? Monga mmene anacitila m’nthawi ya atumwi, Yesu anali kudzagwilitsilanso nchito anthu ocepa kudyetsa anthu ambili. Koma pamene masiku otsiliza anangoyamba, funso lofunika linali lakuti, Kodi anthu ocepa amenewo adzakhala ndani? Tidzakambilana funso limenelo kuphatikizapo mafunso ena okhudza ulosi wa Yesu umenewu m’nkhani yotsatila.
MAU AKUMAPETO: (Mau awa aŵelengedwe monga mau a munsi poŵelenga ndime zake.)
[Mau apansi]
a Ndime 3: Pa nthawi ina pamene Yesu mozizwitsa anadyetsa amuna okwana 4,000 kupatulapo akazi ndi ana, anapelekanso cakudya kwa “ophunzilawo ndipo io anagaŵila khamu la anthulo.”—Mat. 15:32-38.
b Ndime 7: M’nthawi ya Petulo, anthu onse a ‘m’kagulu ka nkhosa’ amene anali kudyetsedwa anali ndi ciyembekezo ca kumwamba.
c Ndime 8: Mfundo yakuti okhulupilila atsopano “anapitiliza kulabadila zimene atumwiwo anali kuphunzitsa,” imatanthauza kuti atumwi anali kuphunzitsa nthawi zonse. Zinthu zina zimene atumwi anali kuphunzitsa zinalembedwa m’mabuku ouzilidwa amene pa nthawi ino ndi mbali ya Malemba Acigiriki Acikristu.
d Ndime 12: Anthu ena amene sanali atumwi naonso analandila mphatso zozizwitsa za mzimu. Koma nthawi zambili io anali kulandila mphatso zimenezo mwacindunji kudzela mwa atumwi kapena pamaso pa atumwi.—Mac. 8:14-18; 10:44, 45.
e Ndime13: Mau a mtumwi Paulo pa Machitidwe 20:29, 30, amaonetsa kuti mpingo udzaukilidwa kucokela ku mbali ziŵili. Mbali yoyamba, Akristu onama (“namsongole”) ‘adzafika pakati’ pa Akristu oona. Mbali yaciŵili, “pakati” pa Akristu oona padzakhala ampatuko amene adzalankhula “zinthu zopotoka.”
f Ndime 17: Onani nkhani yakuti “Dziŵani Kuti Ine Ndili Pamodzi ndi Inu Masiku Onse,” m’magazini ino, tsamba 11, ndime 6.
[Cithunzi papeji 23]
Anthu ambili anadyetsedwa mwa kugwilitsila nchito anthu ocepa
(Onani ndime 4)
[Cithunzi papeji 25]
M’nthawi ya atumwi, zinali zosavuta kudziŵa anthu amene Yesu anali kugwilitsila nchito kudyetsa mpingo
(Onani ndime 12)