LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w13 10/1 tsa. 8
  • “Yehova Anakukhululukilani ndi Mtima Wonse”

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • “Yehova Anakukhululukilani ndi Mtima Wonse”
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2013
  • Nkhani Zofanana
  • Yehova Ni Wokonzeka Kukhululuka
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2022
  • Khalani Wokhululuka
    ‘Imbani Mokweza ndi Mosangalala’ kwa Yehova
  • Muzikhululuka
    Imbirani Yehova
  • Muzikhulupirira Kuti Yehova Anakukhululukirani
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2013
w13 10/1 tsa. 8

YANDIKILANI MULUNGU

“Yehova Anakukhululukilani ndi Mtima Wonse”

Katswili wa mbili yakale wa ku Britain wa m’zaka za m’ma 1600 wochedwa Edward Herbert, anati: “Munthu amene sakhululukila ena amatsekeleza mwai wakuti ena amukhululukile.” Mau amenewa amaonetsa cifukwa cimodzi cimene tifunikila kukhululukila anzathu. Cifukwa cake ndi cakuti nthawi zina, ifenso tingapemphe anzathu kuti atikhululukile. (Mateyu 7:12) Koma pali cifukwa cina cacikulu kwambili cimene tifunikila kukhululukila ena. Onani mau a mtumwi Paulo a pa Akolose 3:13.—Ŵelengani.

Kaamba kakuti tonse ndife opanda ungwilo, nthawi zina tingakhumudwitse anzathu kapena kuwalakwila, ndipo nawonso angatilakwile. (Aroma 3:23) Kodi tingasunge bwanji mtendele ndi anzathu opanda ungwilo? Mouzilidwa ndi Mulungu, Paulo anapeleka malangizo akuti tiyenela kukhala osakwiya msanga ndi okhululukila ena. Malangizo amenewa amathandiza masiku ano monga mmene analili pamene analembedwa zaka pafupi-fupi 2000 zapitazo. Tsopano tiyeni tipende mosamalitsa mau a Paulo amenewa.

“Pitilizani kulolelana.” Liu la Cigiriki limene analitembenuza kuti “pitilizani kulolelana,” limatanthauza kusakwiya msanga. Buku lina limakamba kuti Mkristu amasonyeza khalidwe limeneli mwa “kuleza mtima ndi munthu amene ali ndi zizoloŵezi zoipa zimene zimamukhumudwitsa.” Liu lakuti “kulolelana” limaonetsa kuti aliyense afunika kulolela zolakwa za mnzake. Izi zitanthauza kuti tiyenela kuzindikila kuti nafenso tili ndi makhalidwe ena amene amakhumudwitsa anzathu. Tikatelo, sitidzalola kuti zimene ena angatilakwile zisokoneze mtendele wathu ndi io. Koma bwanji ngati ena atilakwila?

“Pitilizani . . . kukhululukilana ndi mtima wonse.” Malinga ndi katswili wina, liu la Cigiriki limene linatembenuzidwa kuti “kukhululukilana ndi mtima wonse” “ndi liu lapadela limene limatanthauza kukhululukila . . ndipo limagogomeza za kukhululukila mocokela pansi pa mtima.” Buku lina limanena kuti liu limeneli lingatanthauze “kucitila munthu cabwino, kumukomela mtima kapena kumuthandiza.” Timaonetsa kuti ndife okoma mtima kwa ena mwa kulolela kuwakhululukila ndi mtima wonse ngati tili ndi ‘cifukwa codandaulila za io.’ Koma kodi n’cifukwa ciani tiyenela kuwakomela mtima mwa njila imeneyo? Cifukwa cimodzi n’cakuti nthawi zina ifenso tingafune kuti mnzathu amene tamulakwila atikomele mtima mwa kutikhululukila ifeyo.

“Monga Yehova anakukhululukilani ndi mtima wonse, inunso teloni.” Cifukwa cacikulu cimene tifunikila kukhululukila ena ndi cakuti Yehova Mulungu amatikhululukila ndi mtima wonse. (Mika 7:18) Ganizilani cifundo cacikulu cimene Yehova amaonetsa kwa anthu ocimwa amene alapa. Mosiyana ndi ife, Yehova sacita chimo. Conco, sangafunikile kuti anthu ocimwa amusonyeze cifundo mwa kumukhululukila. Komabe, iye amakhululukila ndi mtima wonse anthu ocimwa amene alapa. Indedi, Yehova ndi citsanzo cabwino kwambili ca kukhululukila ndi mtima wonse anthu olapa.

Cifundo ca Yehova cimatilimbikitsa kumuyandikila ndi kutengela citsanzo cake. (Aefeso 4:325:1) Tingacite bwino kudzifunsa kuti, ‘Popeza kuti Yehova amandikomela mtima mwa kundikhululukila, kodi inenso sindiyenela kukhululukila anthu anzanga opanda ungwilo amene andilakwila ndipo alapa moona mtima?’—Luka 17:3,4.

Mavesi amene mungaŵelenge

Agalatiya 1-6; Aefeso 1-6; Afilipi 1-4; Akolose 1-4; Kalata Yoyamba kwa Atesalonika 1-5; Kalata Yachiwiri kwa Atesalonika 1-3; Kalata Yoyamba kwa Timoteyo 1-6 mpaka Kalata Yachiwiri kwa Timoteyo 1-4

[Mau okopa papeji 8]

Yehova ndi citsanzo cabwino kwambili ca kukhululukila ndi mtima wonse anthu olapa

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani