LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • wp16 na. 1 tsa. 16
  • Kuyankha Mafunso A M’baibulo

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kuyankha Mafunso A M’baibulo
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2016
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • Kodi akufa adzakhalanso ndi moyo?
  • Kuyankha Mafunso a M’baibo
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2013
  • Kuyankha Mafunso a M’baibo
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2013
  • Akufa Adzauka Ndithu!
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
  • Kodi Ciukitso N’ciyani?
    Kuyankha Mafunso Okhudza Baibo
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2016
wp16 na. 1 tsa. 16

Kuyankha Mafunso A M’baibulo

Kodi akufa adzakhalanso ndi moyo?

Anthu akulandila oukitsidwa m’Paladaiso

Kukamba zoona, Mlengi wa moyo adzaukitsadi akufa

Yehova Mulungu ndiye Kasupe wa moyo. (Salimo 36:9) Ndiye cifukwa cake m’pomveka kuti iye adzaukitsa akufa. Baibulo limatitsimikizila kuti Mulungu adzacitadi zimenezi mtsogolo. (Ŵelengani Machitidwe 24:15) Nanga n’cifukwa ciani adzaukitsa akufa?

Colinga ca Mlengi wathu poyamba cinali cakuti anthu akhale ndi moyo wosatha padziko lapansi. (Genesis 1:31; 2:15-17) Colinga cake cimeneci sicinasinthe. Iye zimam’pweteka kwambili akaona kuti anthufe tikukumana ndi mavuto osiyanasiyana, komanso kuti tili ndi moyo waufupi.—Ŵelengani Yobu 14:1, 14, 15.

Kodi amene adzaukitsidwa adzakhala kuti?

Kodi Mulungu analenga anthu kuti azikhala kumwamba? Iyai. Mulungu analenga angelo kuti azikhala kumwamba. Koma anthu anawalenga kuti azikhala padziko lapansi. (Genesis 1:28; Yobu 38:4, 7) Mwacitsanzo, ganizilani anthu amene Yesu anaukitsa. Iwo ataukitsidwa, anakhalanso ndi moyo padziko lapansi. Conco, anthu ambili amene adzaukitsidwa adzakhalanso ndi moyo padziko lapansi.—Ŵelengani Yohane 5:28, 29; 11:44.

Komabe, Mulungu anasankha anthu ocepa kuti adzakhale kumwamba ndipo adzapatsidwa matupi auzimu. (Luka 12:32; 1 Akorinto 15:49, 50) Anthu amene adzaukitsidwila kumwamba adzalamulila dziko lapansi limodzi ndi Yesu.—Ŵelengani Chivumbulutso 5:9, 10.

Kuti mudziŵe zambili, onani nkhani 7 m’buku ili, Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova

Mungatenge buku limeneli pa www.jw.org

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani