KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBO
Kodi colinga ca kubwelanso kwa Kristu n’ciani?
Yesu Kristu asanapite kumwamba m’caka ca 33 C.E., analonjeza kuti adzabwelanso. Iye anadziyelekezela ndi munthu wa m’banja lacifumu amene anapita ku dziko lakutali ndipo atabwelako anakhala mfumu. Colinga ca kubwelanso kwa Yesu ndi kubweletsa boma labwino kwa anthu.—Ŵelengani Luka 19:11, 12.
Kodi Kristu adzabwela ndi thupi lotani? Iye anaukitsidwa ndi thupi lauzimu limene silioneka. (1 Petulo 3:18) Ndiyeno, Yesu anapita kumwamba ndi kukakhala kudzanja lamanja la Mulungu. (Salimo 110:1) Patapita zaka, anamubweletsa pafupi ndi “Wamasiku Ambili,” Yehova Mulungu, amene anapatsa Yesu mphamvu zolamulila anthu onse. Conco Yesu adzabwelanso monga Mfumu yosaoneka osati monga munthu.—Ŵelengani Danieli 7:13, 14.
Kodi Yesu adzacita ciani akadzabwela?
Yesu akadzabwela mosaoneka ndi angelo ake, adzaweluza anthu. Iye adzaononga anthu oipa koma adzapeleka moyo wosatha kwa anthu onse amene amamuvomeleza monga Mfumu.—Ŵelengani Mateyu 25:31-33, 46.
Pamene Yesu adzalamulila dziko lapansi monga Mfumu, adzalisandutsa kukhala paradaiso. Iye adzaukitsa akufa n’colinga cakuti akasangalale ndi moyo m’Paradaiso padziko lapansi.—Ŵelengani Luka 23:42, 43.
Kuti mudziŵe zambili, onani tsamba 73 mpaka 85 m’buku ili, Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova
Mungatenge buku limeneli pa www.jw.org
[Cithunzi papeji 32]
Yesu adzabweletsa boma labwino kwa anthu