KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBULO
Kodi ndani kwenikweni akulamulila dzikoli?
Anthu ambili amakhulupilila kuti Mulungu woona ndiye akulamulila dziko. Ngati zimenezi n’zoona, kodi m’dziko mukanakhala mavuto ambili conco? (Deuteronomo 32:4, 5) Baibulo limanena kuti pali wina wake woipa amene akulamulila dzikoli.—Ŵelengani 1 Yohane 5:19.
Kodi woipayo anayamba bwanji kulamulila anthu? Kuciyambi kwa mbili ya anthu, mngelo wina anapandukila Mulungu ndipo anacititsa kuti anthu aŵili oyambilila apandukilenso Mulungu. (Genesis 3:1-6) Anthuwo anasankha kumvela mngelo wochedwa Satana kuti aziwalamulila. Mulungu wamphamvu zonse ndi yekhayo woyenela kulamulila. Koma iye amafuna kuti anthu asankhe ulamulilo wake cifukwa com’konda. (Deuteronomo 6:6; 30:16, 19) Koma n’zacisoni kuti anthu ambili asoceletsedwa mofanana ndi anthu oyambilila.—Ŵelengani Chivumbulutso 12:9.
Kodi ndani adzathetsa mavuto a anthu?
Kodi Mulungu adzalola Satana kupitiliza kulamulila anthu? Iyai. Mulungu adzagwilitsila nchito Yesu kucotsapo zinthu zoipa zimene Satana wabweletsa.—Ŵelengani 1 Yohane 3:8.
Mulungu adzapatsa Yesu mphamvu zoononga Satana. (Aroma 16:20) Ndiyeno, Mulungu adzalamulila anthu ndi kubwezeletsa cimwemwe ndi mtendele monga mmene anafunila paciyambi.—Ŵelengani Chivumbulutso 21:3-5.