Yehova ndi Mulungu Wadongosolo
“Mulungu si Mulungu wacisokonezo, koma wamtendele.”—1 AKOR. 14:33.
1, 2. (a) Kodi Mulungu analenga ndani poyamba? Nanga Yehova anam’gwilitsila nchito bwanji? (b) N’ciani cionetsa kuti angelo ndi adongosolo?
YEHOVA, Mlengi wa zinthu zonse, amacita zinthu mwadongosolo. Poyamba, Mulungu analenga Mwana wake wobadwa yekha wauzimu amene ndi Yesu. Mwanayu amachedwa “Mau” cifukwa anali wolankhulila wa Mulungu wamkulu. Yesu watumikila Yehova kwa zaka zambili. Baibulo limanena kuti: “Pa ciyambi, panali wina wochedwa Mau, ndipo Mauyo anali ndi Mulungu.” Limanenanso kuti: “Zinthu zonse zinakhalako kudzela mwa iye, ndipo palibe cinthu ngakhale cimodzi cimene cinakhalapo popanda iyeyo.” Zaka zoposa 2,000 zapita, Mulungu anatuma Yesu Kristu padziko lapansi. Monga munthu wangwilo, iye anacita cifunilo ca Atate wake mokhulupilika.—Yoh. 1:1-3, 14.
2 Asanabwele padziko lapansi, Mwana wa Mulungu anatumikila mokhulupilika monga “mmisili waluso.” (Miy. 8:30) Kupyolela mwa iye, Yehova analenga zolengedwa zina zauzimu mamiliyoni ambili kumwamba. (Akol. 1:16) Ponena za angelo amenewa, Baibulo limati: “Panali atumiki okwana miliyoni imodzi amene anali kum’tumikila [Yehova] nthawi zonse, ndi atumiki enanso mamiliyoni 100 amene anali kuimilila pamaso pake nthawi zonse.” (Dan. 7:10) Zolengedwa zauzimu za Mulungu zimachedwa kuti “makamu” a Yehova ndipo ndi zadongosolo.—Sal. 103:21.
3. Kodi nyenyezi ndi mapulaneti ndi zoculuka motani? Nanga zinalengedwa bwanji mwadongosolo?
3 Bwanji ponena za zinthu zakumwamba monga nyenyezi ndi mapulaneti? Ponena za nyenyezi, nyuzipepala ina ya ku Houston, m’cigawo ca Texas, inafotokoza kuti kafukufuku waposacedwapa anaonetsa kuti pali nyenyezi zokwanila “300 sekisitiliyoni, kapena kuti kuwilikiza katatu kuyelekezela ndi ciŵelengelo cimene asayansi anapeza m’mbuyomu.” Nyuzipepalayi inafotokozanso kuti ciŵelengelo cimeneci ndi “3 lotsatilidwa ndi mazilo 23 kapena kuti 3 tililiyoni kuwilikiza nthawi 100 biliyoni.” Nyenyezi zimenezi zinaikidwa m’milalang’amba mwadongosolo ndipo mlalang’amba uliwonse uli ndi mabiliyoni kapena matililiyoni a nyenyezi ndi mapulaneti ambili. Ndipo milalang’amba yambili ili m’magulu akuluakulu.—Chronicle.
4. N’ciani cimaonetsa kuti Yehova wakhazikitsa atumiki ake padziko lapansi?
4 Mofanana ndi zolengedwa zauzimu zolungama kumwamba, nyenyezi zinalengedwa mocititsa cidwi kwambili. (Yes. 40:26) Popeza kuti Yehova ndi wa dongosolo, iye wakhazikitsa atumiki ake padziko lapansi, ndipo afuna kuti naonso azicita zinthu mwadongosolo. Zimenezi n’zofunika kuti akwanilitse nchito yao yaikulu. Kwa zaka zambili, Yehova wakhala ndi gulu limene limam’tumikila mokhulupilika. Pali zitsanzo zambili zimene zimaonetsa kuti Mulungu wakhala akucilikiza gulu lake ndipo zimenezi zionetsa kuti iye “si Mulungu wacisokonezo, koma wamtendele.”—Ŵelengani 1 Akorinto 14:33, 40.
MULUNGU ANAKHAZIKITSA ATUMIKI AKE M’NTHAWI ZAKALE
5. Kodi colinga ca Mulungu cakuti anthu adzaze dziko lapansi cinasokonezeka bwanji?
5 Yehova atalenga anthu oyamba, iye anawauza kuti: “Mubelekane, muculuke, mudzaze dziko lapansi, ndipo muliyang’anile. Muyang’anilenso nsomba za m’nyanja ndi zolengedwa zouluka m’mlengalenga, komanso colengedwa ciliconse cokwawa padziko lapansi.” (Gen. 1:28) Yehova sanalenge anthu mamiliyoni panthawi imodzi. Adamu ndi Hava anafunika kubeleka ana ndipo naonso ana ao anafunika kubeleka ana mpaka kudzaza dziko lapansi. Mulungu anafuna kuti anthu oyambilila akonze dziko lonse kukhala paladaiso. Colinga ca Mulungu cimeneci cinasokonezeka kwa kanthawi pamene Adamu ndi Hava sanamvele Mulungu. (Gen. 3:1-6) M’kupita kwa nthawi, “Yehova anaona kuti kuipa kwa anthu kwaculuka padziko lapansi, ndipo malingalilo onse a m’mitima ya anthu anali oipa okhaokha nthawi zonse.” Zimenezi zinacititsa kuti ‘dziko lapansi liipe pamaso pa Mulungu woona, ndi kudzaza ndi ciwawa.’ Conco, Mulungu anali kudzabweletsa cigumula padziko lapansi cimene cinali kudzaononga anthu oipa.—Gen. 6:5, 11-13, 17.
6, 7. (a) N’cifukwa ciani Nowa anayanjidwa ndi Yehova? (Onani cithunzi cili kuciyambi kwa nkhani ino.) (b) N’ciani cinacitikila anthu onse opanda cikhulupililo m’nthawi ya Nowa?
6 Komabe, “Nowa anayanjidwa ndi Yehova” cifukwa cakuti “anali munthu wolungama.” Iye “anali wopanda colakwa pakati pa anthu a m’nthawi yake.” Popeza “Nowa anayenda ndi Mulungu woona,” Yehova anam’patsa malangizo akuti apange cingalawa cacikulu. (Gen. 6:8, 9, 14-16) Cingalawaci cinapangidwa m’njila yakuti ciziyandama pamadzi kuti anthu ndi nyama apulumuke. Nowa ndi banja lake anacita zonse zimene Yehova anawauza. Atamaliza kuloŵetsa nyama m’cingalawa, “Yehova anatseka citseko.”—Gen. 7:5, 16.
7 Cigumula citayamba mu 2370 B.C.E., Yehova “anaseselatu camoyo ciliconse cimene cinali padziko lapansi,” koma anasunga Nowa ndi banja lake. (Gen. 7:23) Masiku ano, munthu aliyense padziko lapansi ndi mbadwa ya Nowa, ana ake ndi akazi ao. Koma anthu onse opanda cikhulupililo anaonongedwa, cifukwa cakuti sanamvele Nowa “mlaliki wa cilungamo.”—2 Pet. 2:5.
8. Kodi Aisiraeli anacita ciani pamene Mulungu anawauza kuti aloŵe m’Dziko Lolonjezedwa?
8 Patapita zaka zoposa 800 pambuyo pa Cigumula, Mulungu anapanga Aisiraeli kukhala mtundu. Anthuwo anafunikila kumacita zinthu mwadongosolo paumoyo wao makamaka polambila. Mwacitsanzo, kuonjezela pa ansembe ambili ndi Alevi aciisiraeli, panalinso “akazi otumikila, amene anali kutumikila mwadongosolo pacipata ca cihema cokumanako.” (Eks. 38:8) Yehova anauza Aisiraeli kuti aloŵe m’dziko la Kanani. Koma Aisiraeli ambili anacita mantha ndipo anakana. Conco, Mulungu anawauza kuti: “Inu simudzaloŵa m’dziko limene ndinacita kukweza dzanja langa polumbila kuti ndidzakhala nanu mmenemo, kupatula Kalebe mwana wa Yefune, ndi Yoswa mwana wa Nuni.” Yoswa ndi Kalebe ndiwo okha amene anabweletsa lipoti labwino pambuyo pozonda Dziko Lolonjezedwa. (Num. 14:30, 37, 38) Cifukwa cotsatila malangizo a Mulungu, Mose anaika Yoswa kukhala wom’loŵa m’malo. (Num. 27:18-23) Yoswa atatsala pang’ono kutsogolela Aisiraeli kuloŵa m’dziko la Kanani, Mulungu anamuuza kuti: “Ukhale wolimba mtima ndipo ucite zinthu mwamphamvu. Usacite mantha kapena kuopa, pakuti Yehova Mulungu wako ali nawe kulikonse kumene upiteko.”—Yos. 1:9.
9. Kodi Rahabi anamuona bwanji Yehova ndi anthu ake?
9 Yehova Mulungu anathandizadi Yoswa pa zilizonse zimene anali kucita. Mwacitsanzo, ganizilani zimene zinacitika pamene Aisireli anazungulila Yeriko, mzinda wa Akanani. Mu 1473 B.C.E., Yoswa anatuma azondi aŵili kuti akazonde Yeriko, ndipo kumeneko anapeza mkazi wina wochedwa Rahabi amene anali hule. Anthu a mumzindawo anafuna kuti agwile azondiwo, koma Rahabi anawabisa padenga la nyumba yake. Iye anauza azondi aciisiraeli kuti: “Ndikudziŵa kuti Yehova akupatsani ndithu dziko lino . . . . Tinamva za mmene Yehova anaphwetsela madzi a Nyanja Yofiila pamaso panu . . . Tinamvanso za mmene munaphela mafumu aŵili a Aamori.” Iye ananenanso kuti: “Yehova Mulungu wanu ndiye Mulungu wa kumwamba ndi padziko lapansi.” (Yos. 2:9-11) Cifukwa cakuti Rahabi anagwilizana ndi gulu la Yehova panthawiyo, iye ndi banja lake anapulumutsidwa pamene Aisiraeli anagonjetsa Yeriko. (Yos. 6:25) Rahabi anali ndi cikhulupililo, ndipo iye anaopa Yehova ndi kulemekeza anthu ake.
GULU LA AKRISTU LINAKHAZIKITSIDWA M’NTHAWI YA ATUMWI
10. Kodi Yesu anawauza ciani atsogoleli acipembedzo aciyuda a m’nthawi yake? Nanga n’cifukwa ciani anawauza zimenezo?
10 Motsogoleledwa ndi Yoswa, Aisiraeli anagonjetsa mzinda uliwonse ndipo anakakhala m’dziko la Kanani. Koma kodi Aisiraeli anacita ciani patapita nthawi? Mobwelezabweleza, io anaphwanya malamulo a Mulungu. Pamene Yesu anabwela padziko lapansi, Aisiraeli anapitilizabe kusamvela Yehova ndi aneneli ake cakuti Yesu anacha Yerusalemu kuti “wakupha aneneli.” (Ŵelengani Mateyu 23:37, 38.) Mulungu anakana atsogoleli acipembedzo aciyuda cifukwa cakuti anali osakhulupilika. Conco, Yesu anawauza kuti: “Ufumu wa Mulungu udzacotsedwa kwa inu n’kupelekedwa kwa mtundu wobala zipatso zake.”—Mat. 21:43.
11, 12. (a) M’nthawi ya atumwi, n’ciani cionetsa kuti Yehova anakana mtundu waciyuda ndi kuyamba kuyanja gulu lina? (b) Kodi ndani anali m’gulu latsopano loyanjidwa ndi Mulungu?
11 M’nthawi ya atumwi, Mulungu anakana mtundu wosakhulupilika wa Aisiraeli. Komabe, zimenezo sizinatanthauze kuti Mulungu sadzakhala ndi gulu la atumiki ake okhulupilika padziko lapansi. Yehova anasiya Aisiraeli ndipo anayamba kuyanja gulu latsopano limene linayamba pa Pentekosite mu 33 C.E. Nthawi imeneyo panali ophunzila okwanila 120 amene anasonkhana ku Yerusalemu, ndipo “mwadzidzidzi kumwamba kunamveka mkokomo ngati wa mphepo yamphamvu, ndipo unadzaza m’nyumba yonse.” Kenako “anaona malawi amoto ooneka ngati malilime, ndipo anagawanika ndi kukhala pa aliyense wa io limodzilimodzi. Ndiyeno onsewo anadzazidwa ndi mzimu woyela ndipo anayamba kulankhula zinenelo zosiyanasiyana, monga mmene mzimuwo unawacititsila kulankhula.” (Mac. 2:1-4) Cozizwitsa cimeneci cinapeleka umboni wosatsutsika wakuti Yehova anali kucilikiza gulu lake latsopano lopangidwa ndi ophunzila a Kristu.
12 Patsiku lapadela limenelo, ciŵelengelo ca ophunzilawo “cinaonjezeka ndi anthu pafupifupi 3,000.” Ndiponso “Yehova anapitiliza kuwaonjezela anthu amene anali kuwapulumutsa.” (Mac. 2:41, 47) Akristu a m’nthawi ya atumwi anagwila nchito yolalikila mwakhama cakuti “mau a Mulungu anapitiliza kufalikila ponseponse. Ciŵelengelo ca ophunzila cinali kuonjezeka kwambili mu Yerusalemu.” Ndipo “ansembe ambilimbili anakhala okhulupilila.” (Mac. 6:7) Anthu ambili analandila coonadi atalalikilidwa ndi gulu latsopano limenelo. Patapita nthawi, Yehova anaonetsanso kuti anali kucilikiza gulu lake pamene anayamba kucititsa “anthu a mitundu ina” kubwela mumpingo wacikristu.—Ŵelengani Machitidwe 10:44, 45.
13. Ndi nchito iti imene Mulungu anapatsa gulu lake latsopano?
13 Mosakaikila, otsatila a Kristu anali ndi nchito yopatsidwa ndi Mulungu. Yesu anapatsa ophunzila ake citsanzo pa nchitoyi. Atangobatizika, iye anayamba kulalikila za “ufumu wakumwamba.” (Mat. 4:17) Yesu anaphunzitsa ophunzila ake kugwila nchito imeneyi. Iye anawauza kuti: “Mudzakhala mboni zanga mu Yerusalemu, ku Yudeya konse ndi ku Samariya, mpaka kumalekezelo a dziko lapansi.” (Mac. 1:8) Mwacionekele, otsatila a Kristu oyambilila anadziŵa zimene anafunikila kucita. Mwacitsanzo, ku Antiokeya wa ku Pisidiya, Paulo ndi Baranaba molimba mtima anauza Ayuda otsutsa kuti: “Kunali koyenela kuti inu mukhale oyamba kuuzidwa mau a Mulungu. Koma popeza kuti mukuwatayila kumbali ndipo mukudziweluza nokha kukhala osayenela moyo wosatha, ifeyo tikutembenukila kwa anthu a mitundu ina. Ndipotu Yehova anatiikila lamulo lakuti, ‘Ndakuikani monga kuwala kwa anthu a mitundu ina, kuti mukhale cipulumutso mpaka kumalekezelo a dziko lapansi.’” (Mac. 13:14, 45-47) Kucokela m’nthawi ya atumwi, gulu la Mulungu lakhala likuuza anthu zimene Yehova wacita kuti apulumutse anthu.
ATUMIKI A MULUNGU ANAPULUMUKA
14. N’ciani cinacitikila Yerusalemu wakale? Nanga ndani anapulumuka?
14 Ayuda ambili sanalandile uthenga wabwino ndipo anakumana ndi mavuto. Yesu anacenjeza ophunzila ake kuti: “Mukadzaona magulu ankhondo atazungulila Yerusalemu, mudzadziŵe kuti cionongeko cake cayandikila. Pamenepo amene ali mu Yudeya adzayambe kuthaŵila kumapili, ndipo amene ali mkati mwa mzindawo adzatulukemo. Amene ali m’madela akumidzi asadzaloŵe mumzindawo.” (Luka 21:20, 21) Mogwilizana ndi ulosi wa Yesu, mzinda wa Yerusalemu unaonongedwadi. Ayuda anaukila ulamulilo wa Aroma, ndipo mu 66 C.E. asilikali a Roma anatsala pang’ono kuononga mzindawo. Mwadzidzidzi, asilikali a Roma anacoka ndipo zimenezi zinapatsa otsatila a Yesu mpata wakuti acoke mu Yerusalemu ndi mu Yudeya. Malinga ndi zimene wolemba mbili wina wochedwa Eusebius ananena, anthu ambili anadutsa Mtsinje wa Yorodani ndi kuthaŵila ku Pela mumzinda wa Pereya. Mu 70 C.E., asilikali aciroma motsogoleledwa ndi Kazembe Tito, anabwelela ndi kuononga Yerusalemu. Koma Akristu okhulupilika amene anamvela cenjezo la Yesu anapulumuka.
15. N’cifukwa ciani anthu ambili anakhala Akristu?
15 M’nthawi ya atumwi, Akristu anazunzidwa ndipo cikhulupililo cao cinayesedwa. Ngakhale zinali conco, anthu ambili anakhala Akristu. (Mac. 11:19-21; 19:1, 19, 20) Cifukwa ca dalitso la Mulungu, Akristu amenewo anapita patsogolo kuuzimu.—Miy. 10:22.
16. Kodi Mkristu aliyense anafunikila kucita ciani kuti akhale wolimba kuuzimu?
16 Mkristu aliyense anafunikila kucita khama kuti akhale wolimba kuuzimu. Kuphunzila Malemba mwakhama, kupezeka pamisonkhano nthawi zonse ndi kutengamo mbali m’nchito yolalikila zinali zofunika kwambili. Kucita zimenezi kunathandiza anthu a Yehova kukhala ogwilizana ndi olimba kuuzimu, ndipo umu ndi mmene zilili masiku ano. Anthu amene anagwilizana ndi mipingo imene inakhazikitsidwa m’nthawi ya atumwi, anapindula kwambili ndi khama ndi kudzipeleka kumene oyang’anila ndi atumiki othandiza anasonyeza. (Afil. 1:1; 1 Pet. 5:1-4) Mwacionekele, zimenezi zinasangalatsa kwambili oyang’anila oyendela monga Paulo, pamene anali kucezela mipingo. (Mac. 15:36, 40, 41) Mmene Akristu amacitila zinthu polambila masiku ano zimafanana ndi mmene Akristu a m’nthawi ya atumwi anali kucitila. Timayamikila kwambili kuti Yehova wakhazikitsa atumiki ake masiku ano monga mmene anacitila m’nthawi zakale.a
17. Kodi tidzakambilana ciani m’nkhani yotsatila?
17 Pamene mapeto a dziko la Satana akuyandikila, gulu la Yehova padziko lapansi likupita patsogolo kwambili. Kodi mukuyendela limodzi ndi gulu limeneli? Kodi mukupita patsogolo mwa kuuzimu? Nkhani yotsatila idzaonetsa mmene tingacitile zimenezi.
a Onani nkhani yakuti, “Akristu Amalambira Mumzimu ndi M’choonadi” ndi yakuti “Amayendabe M’choonadi” mu Nsanja ya Olonda ya July 15, 2002. Kuti mumve zambili zokhudza gulu la Mulungu padziko lapansi, onani buku lakuti Jehovah’s Witnesses—Proclaimers of God’s Kingdom.