Kodi Mumayendela Limodzi ndi Gulu la Yehova?
“Maso a Yehova ali pa olungama.”—1 PET. 3:12.
1. Ndi gulu liti limene linaloŵa m’malo Aisiraeli ampatuko? (Onani cithunzi cili kuciyambi kwa nkhani ino.)
MASIKU ano, anthu a Yehova padziko lapansi amam’lambila m’njila imene imam’sangalatsa. M’nthawi zakale, Aisiraeli anali mtundu wosankhidwa wa Mulungu, koma io anakhala ampatuko. Conco, Yehova anapanga mtundu watsopano wa otsatila a Kristu. Iwo anakhala gulu limene linali kuimila Yehova. Ngakhale kuti Yerusalemu anaonongedwa mu 70 C.E., gulu limenelo silinaonongedwe. (Luka 21:20, 21) M’masiku ano otsiliza pali gulu latsopano limene limaimila Yehova. Gulu limeneli lidzapulumuka pamene dziko la Satana lidzaonongedwa. (2 Tim. 3:1) Kodi tingatsimikize bwanji zimenezi?
2. Kodi Yesu anati ciani ponena za “cisautso cacikulu?” Nanga cidzayamba bwanji?
2 Pofotokoza za kukhalapo kwake kosaoneka ndi mapeto a nthawi ino, Yesu anati: “Kudzakhala cisautso cacikulu cimene sicinacitikepo kucokela pa ciyambi ca dziko mpaka tsopano, ndipo sicidzacitikanso.” (Mat. 24:3, 21) Cisautso cimeneci cidzayamba Yehova akadzaononga “Babulo Wamkulu,” ufumu wapadziko lonse wacipembedzo conyenga. Mulungu adzagwilitsila nchito maboma a anthu kucita zimenezi. (Chiv. 17:3-5, 16) Kodi n’ciani cidzatsatilapo?
KUUKILA KWA SATANA KUDZAYAMBITSA ARAMAGEDO
3. Pambuyo pakuti cipembedzo conyenga caonongedwa, n’ciani cidzacitikila anthu a Yehova?
3 Pambuyo pakuti cipembedzo conyenga caonongedwa, Satana ndi magulu ake adzaukila atumiki a Yehova. Mwacitsanzo, ponena za “Gogi wa kudziko la Magogi,” Baibulo limati: “Iwe udzabwela m’dzikolo ngati mphepo yamkuntho. Iweyo, magulu ako onse a asilikali, pamodzi ndi anthu ambili a mitundu ina, mudzaphimba dzikolo ngati mitambo.” Zidzaoneka ngati kuti anthu a Yehova ndi osatetezeka, koma kuukila anthuwo kudzaputa mkwiyo wa Mulungu.—Ezek. 38:1, 2, 9-12.
4, 5. Kodi Yehova adzacita ciani pamene Satana adzafuna kuononga atumiki a Mulungu?
4 Kodi Mulungu adzacita ciani Satana akadzafuna kuononga anthu ake? Yehova adzaloŵelelapo kuti aonetse kuti iye ndi Wolamulila wa Cilengedwe Conse. Yehova adzaona kuti kuukila atumiki ake kuli ngati kuukila iye mwini. (Ŵelengani Zekariya 2:8.) Conco, Atate wathu wakumwamba adzacitapo kanthu kuti atipulumutse. Tikadzapulumutsidwa, dziko la Satana lidzaonongedwa pa Aramagedo, imene ndi nkhondo “ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse.”—Chiv. 16:14, 16.
5 Ponena za Aramagedo, ulosi wa m’Baibulo umati: “‘Yehova akufuna kuimba mlandu mitundu ya anthu. Iye mwini adzalimbana ndi anthu onse powaweluza. Anthu oipa adzawapha ndi lupanga,’ watelo Yehova. Yehova wa makamu wanena kuti, ‘Taonani! Tsoka likuyenda kucokela mu mtundu wina kupita mu mtundu wina, ndipo mkuntho wamphamvu udzafika kucokela kumalekezelo a dziko lapansi. Pa tsiku limenelo padzakhala anthu ophedwa ndi Yehova kucokela kumalekezelo a dziko lapansi kufikanso kumalekezelo ena a dziko lapansi. Sadzawalila malilo, kuwasonkhanitsa pamodzi, kapena kuwaika m’manda. Iwo adzakhala ngati manyowa panthaka.’” (Yer. 25:31-33) Aramagedo idzathetsa dongosolo loipali la zinthu. Dziko la Satana lidzaonongedwa, koma gulu la Yehova padziko lapansi lidzapulumuka.
CIFUKWA CAKE GULU LA YEHOVA LIKUPITABE PATSOGOLO
6, 7. (a) Kodi anthu amene apanga “khamu lalikulu” acokela kuti? (b) N’ciani cionetsa kuti Mulungu akuthandiza gulu lake kupita patsogolo?
6 Masiku ano, gulu la Mulungu padziko lapansi likupita patsogolo cifukwa lili ndi anthu oyanjidwa ndi Mulungu. Baibulo limatitsimikizila kuti: “Maso a Yehova ali pa olungama, ndipo makutu ake amamva pembedzelo lao.” (1 Pet. 3:12) Olungama amaphatikizapo “khamu lalikulu” limene ‘lidzatuluka m’cisautso cacikulu.’ (Chiv. 7:9, 14) Anthu amene adzapulumuka si “khamu” cabe koma ndi “khamu lalikulu,” anthu oculuka kwambili. Ganizilani mmene mudzamvelela mukadzapulumuka cisautso cacikulu monga mmodzi wa khamu lalikulu.
7 Kodi anthu amene apanga khamu lalikulu acokela kuti? Iwo akusonkhanitsidwa pamodzi, malinga ndi zimene Yesu ananena zokhudza cizindikilo ca kukhalapo kwake. Iye anati: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.” (Mat. 24:14) M’masiku ano otsiliza imeneyi ndiyo nchito yaikulu ya gulu la Mulungu. Cifukwa ca nchito yolalikila ndi kuphunzitsa imene Mboni za Yehova zimagwila padziko lonse, anthu ambili aphunzila kulambila Mulungu motsogoleledwa “ndi mzimu ndi coonadi.” (Yoh. 4:23, 24) Mwacitsanzo, kuyambila m’caka ca utumiki ca 2003 mpaka 2012, anthu oposa 2,707,000, anabatizika kuonetsa kudzipeleka kwao kwa Mulungu. Tsopano, padziko lonse pali Mboni zoposa 7,900,000, ndipo palinso anthu mamiliyoni amene amagwilizana nao makamaka pamwambo wa Cikumbutso caka ndi caka. Ndife osangalala kuti khamu lalikulu likukula mwamsanga, ndipo timadziŵa kuti Yehova akulikulitsa.—1 Akor. 3:5-7.
8. N’cifukwa ciani gulu la Yehova likukula kwambili masiku ano?
8 Cifukwa cakuti Yehova akuthandiza Mboni zake, ciŵelengelo cao cikukula kwambili. (Ŵelengani Yesaya 43:10-12.) Cionjezeko cimeneci n’cogwilizana ndi ulosi wakuti: “Wamng’ono adzasanduka anthu 1,000, ndipo wocepa adzasanduka mtundu wamphamvu. Ineyo Yehova ndidzafulumizitsa zimenezi pa nthawi yake.” (Yes. 60:22) Panthawi ina, otsalila odzozedwa anali “wamng’ono” koma ciŵelengelo cinakula pamene Aisiraeli ena a kuuzimu anawabweletsa m’gulu la Mulungu. (Agal. 6:16) Kwa zaka zambili, ciŵelengelo ca khamu lalikulu cakhala cikupita patsogolo cifukwa ca dalitso la Yehova.
ZIMENE YEHOVA AFUNA KUTI TIZICITA
9. Tingacite ciani kuti tikapindule ndi tsogolo labwino limene Mulungu watilonjeza?
9 Kaya ndife Akristu odzozedwa kapena a khamu lalikulu, Yehova watilonjeza tsogolo labwino. Koma zimenezi zingatheke ngati timvela malamulo ake. (Yes. 48:17, 18) Mwacitsanzo, Yehova anafuna kuti Aisiraeli azitsatila Cilamulo cake. Cilamulo cimeneco cinawateteza ku khalidwe loipa ndi kuwathandiza kukhala ndi mabanja acimwemwe ndi mabwenzi abwino. Cinawathandizanso kucita malonda moona mtima, ndi kukomela ena mtima. (Eks. 20:14; Lev. 19:18, 35-37; Deut. 6:6-9) Ngakhale masiku ano, malamulo a Mulungu amatiteteza ndi kutipindulitsa, ndipo ndi osavuta kutsatila. (Ŵelengani 1 Yohane 5:3.) Tikamatsatila malamulo amenewa timakhala acimwemwe, ndipo koposa zonse cikhulupililo cathu mwa Yehova cimalimba kwambili.—Tito 1:13.
10. N’cifukwa ciani tiyenela kupatula nthawi yophunzila Baibulo ndi kucita Kulambila kwa Pabanja mlungu uliwonse?
10 Gulu la Yehova padziko lapansi likupita patsogolo m’njila zambili. Limatithandiza kumvetsetsa coonadi ca m’Baibulo. Zimenezi n’zogwilizana ndi zimene Baibulo limanena. Baibulo limati: “Njila ya olungama ili ngati kuwala kwamphamvu kumene kumamka kuonjezeleka mpaka tsiku litakhazikika.” (Miy. 4:18) Koma tiyenela kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimayendela limodzi ndi gulu pakakhala kusintha kwa kamvedwe ka mfundo za m’Malemba? Kodi ndimaŵelenga Baibulo tsiku ndi tsiku? Kodi ndili ndi cidwi coŵelenga zofalitsa zatsopano? Kodi ndimapatula nthawi yocita Kulambila kwa Pabanja mlungu uliwonse?’ Ambili a ife tingavomeleze kuti kucita zimenezi n’kosavuta, ndipo kumangofuna kupatula nthawi. Ndiponso, kukulitsa cidziŵitso cathu ca m’Malemba, kucita zimene malemba amanena ndi kukula kuuzimu n’kofunika kwambili makamaka tsopano pamene cisautso cacikulu cikuyandikila.
11. Kodi zikondwelelo za m’nthawi yakale zinali zopindulitsa m’njila ziti? Nanga masiku ano timapindula bwanji ndi misonkhano?
11 Gulu la Yehova limatilimbikitsa kutsatila malangizo a Paulo akuti: “Tiyeni tiganizilane kuti tilimbikitsane pa cikondi ndi nchito zabwino. Tisaleke kusonkhana pamodzi, monga mmene ena acizolowezi cosafika pamisonkhano akucitila. Koma tiyeni tilimbikitsane, ndipo tionjezele kucita zimenezi, makamaka pamene mukuona kuti tsikulo likuyandikila.” (Aheb. 10:24, 25) Zikondwelelo za pacaka ndi misonkhano ina zinalimbitsa Aisiraeli mwa kuuzimu. Zocitika zina monga Cikondwelelo ca Misasa m’masiku a Nehemiya inali nthawi yosangalatsa. (Eks. 23:15; Neh. 8:9-18) Mofananamo, ifenso timapindula ndi misonkhano yampingo, yadela ndi yacigawo. Tiyeni tiziyesetsa kupezeka pamisonkhano yonse imeneyi kuti tikhale acimwemwe ndi olimba kuuzimu.—Tito 2:2.
12. Kodi tiyenela kuiona bwanji nchito yolalikila uthenga wa Ufumu?
12 Popeza timagwilizana ndi gulu la Mulungu, ndife osangalala kugwila nchito yopatulika yolengeza uthenga wabwino wa Mulungu. (Aroma 15:16) Kugwila “nchito yopatulikayi” kumaticititsa kukhala “anchito anzake” a Yehova, Mulungu “Woyela.” (1 Akor. 3:9; 1 Pet. 1:15) Kulalikila uthenga wabwino kumathandiza kuti dzina loyela la Yehova liyeletsedwe. Kunena zoona, ndi mwai waukulu kwambili kutengako mbali pa nchito yolalikila “uthenga wabwino waulemelelo wocokela kwa Mulungu wacimwemwe.”—1 Tim. 1:11.
13. N’ciani cimene tiyenela kucita kuti tikhale olimba kuuzimu ndi kukhalabe ndi moyo?
13 Mulungu afuna kuti tikhale olimba kuuzimu mwa kumamatila kwa iye ndi kucilikiza gulu lake mu nchito zosiyanasiyana. Mose anauza Aisiraeli kuti: “Ndaika moyo ndi imfa, dalitso ndi tembelelo pamaso panu. Kumwamba ndi dziko lapansi ndi mboni pa zocita zanu. Conco inuyo ndi mbadwa zanu musankhe moyo kuti mukhalebe ndi moyo. Musankhe moyo mwa kukonda Yehova Mulungu wanu, kumvela mau ake ndi kum’mamatila, cifukwa iye ndiye wokupatsani moyo ndi masiku ambili kuti mukhale panthaka imene Yehova analumbila kwa makolo anu, Abulahamu, Isaki ndi Yakobo kuti adzawapatsa.” (Deut. 30:19, 20) Kuti tikhalebe ndi moyo, tiyenela kucita cifunilo ca Yehova, kum’konda, kumvela mau ake ndi kumamatila kwa iye.
14. Kodi m’bale wina anali kuliona bwanji gulu la Mulungu looneka?
14 M’bale Pryce Hughes amene anamamatila kwa Mulungu ndi kupitilizabe kuyendela limodzi ndi gulu lake anakamba kuti: “Ndikuthokoza kwambili kuti ndacita mogwilizana ndi cidziŵitso ca zifuno za Yehova kuyambila m’masiku oyambililawo 1914 asanafike pamene zonse zinali zosadziŵika bwino kwambili . . . kufikila lelo pamene coonadi cikuwala ngati dzuŵa lamasana. Ngati palinso cinthu cina cimene cakhala cofunika koposa kwa ine, ndico kumamatila ku gulu la Yehova looneka. Cokumana naco canga coyambilila cinandiphunzitsa mmene kudalila maganizo aumunthu kulili kopanda nzelu. Pamene maganizo anga anatsimikizila za mfundoyo, ndinatsimikiza za kumamatila ku gulu lokhulupilika. Kodi munthu angapezenso motani ciyanjo ca Yehova ndi dalitso lake?”
PITILIZANI KUYENDELA LIMODZI NDI GULU LA MULUNGU
15. Pelakani citsanzo ca m’Baibulo coonetsa zimene tiyenela kucita pakakhala kamvedwe katsopano ka mfundo za m’Malemba.
15 Ngati tifuna kuti Yehova atiyanje ndi kutidalitsa, tiyenela kucilikiza gulu lake ndi kutsatila kamvedwe katsopano ka mfundo za m’Malemba. Ganizilani izi: Pambuyo pa imfa ya Yesu, Akristu ambili amene anali Ayuda anali kutsatila Cilamulo kwambili ndipo anavutika kuti aleke kucitsatila. (Mac. 21:17-20) Koma Paulo anawaongolela ndi kuwathandiza kumvetsa mfundo yakuti macimo ao anakhululukidwa cifukwa ca nsembe ya Yesu osati nsembe ya nyama. (Aheb. 10:5-10) Ambili mwa Akristu amenewo analandila malangizo a Paulo ndi kusintha maganizo ao. Zimene Akristuwo anacita, zitiphunzitsa kufunika kophunzila Baibulo ndi zofalitsa zathu mosamala. Ndiponso, modzicepetsa tiyenela kuyendela limodzi ndi gulu la Yehova ngati pakhala kusintha kwa kamvedwe ka mfundo za m’Malemba.
16. (a) Ndi madalitso ati amene adzacititsa umoyo kukhala wosangalatsa m’dziko latsopano? (b) Ndi zinthu ziti zimene mukuyembekezela m’dziko latsopano?
16 Onse okhulupilika kwa Yehova ndi gulu lake adzalandila madalitso. Akristu odzozedwa adzakhala mafumu pamodzi ndi Yesu kumwamba. (Aroma 8:16, 17) Anthu amene adzakhala padziko lapansi akuyembekezela moyo wosatha. Atumiki onse a Yehova ali ndi mwai wapadela wouzako ena za ciyembekezo cimeneci. (2 Pet. 3:13) Lemba la Salimo 37:11 limati: “Anthu ofatsa adzalandila dziko lapansi ndipo adzasangalala ndi mtendele woculuka.” Anthu “adzamanga nyumba n’kukhalamo,” ndipo io “adzapindula mokwanila ndi nchito ya manja ao.” (Yes. 65:21, 22) Sikudzakhala kupondelezana, umphawi ndi njala. (Sal. 72:13-16) Babulo Wamkulu sadzasoceletsanso aliyense, iye sadzakhalaponso. (Chiv. 18:8, 21) Anthu akufa adzaukitsidwa ndi kupatsidwa mwai wokhala ndi moyo wosatha. (Yes. 25:8; Mac. 24:15) Kunena zoona, anthu odzipeleka kwa Yehova ali ndi ciyembekezo cosangalatsa kwambili. Ngati tifuna kuti tikapindule ndi madalitso amenewa, tiyenela kupitiliza kukula kuuzimu ndi kuyendela limodzi ndi gulu la Mulungu nthawi zonse.
17. Kodi tiyenela kumuona bwanji Yehova pamodzi ndi gulu lake?
17 Posacedwapa, dongosolo la Satana lidzatha. Kuti tikapulumuke, tiyenela kukhala ndi cikhulupililo colimba ndi kulambila Yehova mokhulupilika pamodzi ndi gulu lake. Timamva monga mmene Davide anamvelela, amene anati: “Cinthu cimodzi cimene ndapempha kwa Yehova, cimeneco ndi cimene ndimacikhumba, n’cakuti, ndikhale m’nyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga, kuti ndione ubwino wa Yehova, komanso kuti ndiyang’ane kacisi wake moyamikila.” (Sal. 27:4) Aliyense wa ife ayenela kumamatila kwa Yehova ndi kupitilizabe kuyendela limodzi ndi gulu lake.