KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBULO
N’cifukwa ciani tiyenela kupemphela?
Yehova Mulungu nthawi zonse amafuna kuti tizimuuza zinthu zimene zikutivutitsa. (Luka 18:1-7) Amamvetsela mapemphelo athu cifukwa amatikonda. Monga Atate wathu wakumwamba, akutipempha mokoma mtima kuti tizipemphela kwa iye, kungakhale kupanda nzelu kulephela kucita zimenezi.—Ŵelengani Afilipi 4:6.
Pemphelo si njila yongofuna kupempha thandizo. Koma limatithandiza kuyandikila kwa Mulungu. (Salimo 8:3, 4) Ngati nthawi zonse timuuza Mulungu zakukhosi kwathu, timakhala naye paubwenzi wolimba kwambili.—Ŵelengani Yakobo 4:8.
Tizipemphela bwanji?
Tikamapemphela, Mulungu safuna kuti tizigwilitsila nchito mau odzionetsela kapena kumangobweleza mapemphelo oloweza. Safunanso kuti popemphela tizitsatila kakhalidwe ka thupi kapadela. Yehova amafuna kuti tizipemphela kucokela mumtima. (Mateyu 6:7) Mwacitsanzo, kale m’nthawi ya Isiraeli, Hana anapemphela kwa Mulungu za vuto linalake lokhudza banja lake. Patapita nthawi, mavuto ake anatha ndipo anakhala wokondwela. Hana anayamikila Mulungu mwa kupemphela mocokela pansi pamtima.—Ŵelengani 1 Samueli 1:10, 12, 13, 26, 27; 2:1.
Pemphelo ndi mwai wapadela kwambili! Tingamuuze Mlengi mavuto athu amene tili nao. Tingamutamande ndi kumuyamikilanso cifukwa ca zinthu zimene amaticitila. Ndithudi, sitiyenela kunyalanyaza mwai wapadela kwambili umenewu.—Ŵelengani Salimo 145:14-16.