LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w15 11/1 tsa. 10
  • N’cifukwa Ciani Mulungu Amatilimbikitsa Kupemphela?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • N’cifukwa Ciani Mulungu Amatilimbikitsa Kupemphela?
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • Mulungu amatipempha kuti tikhale naye paubwenzi.
  • Mulungu amafuna kukuthandizani.
  • Anthu amafunika zinthu za kuuzimu.
  • Kodi Mulungu Amamva Mapemphelo Anu?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2021
  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • Mwayi Wa Pemphelo
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
  • Kodi Yehova Amamvetsela kwa Ife?
    Mvetselani kwa Mulungu Kuti Mukhale ndi Moyo Wamuyaya
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
w15 11/1 tsa. 10

N’cifukwa Ciani Mulungu Amatilimbikitsa Kupemphela?

Mulungu amatipempha kuti tikhale naye paubwenzi.

Anthu amene ali pa ubwenzi amalankhulana nthawi zonse kuti alimbitse ubwenzi wao. N’cimodzimodzinso ndi Mulungu, iye amatipempha kuti tizikamba naye n’colinga cakuti tikhale naye paubwenzi wabwino. Iye amati: “Mudzaitanila pa ine komanso mudzabwela ndi kupemphela kwa ine ndipo ine ndidzakumvetselani.” (Yeremiya 29:12) Ngati mumakamba ndi Mulungu, ‘mumamuyandikila ndipo iyenso amayandikila kwa inu.’ (Yakobo 4:8) Baibulo limatitsimikizila kuti: “Yehova ali pafupi ndi onse oitanila pa iye.” (Salimo 145:18) Conco, nthawi zonse tikamapemphela, ubwenzi wathu ndi Mulungu umalimba kwambili.

“Yehova ali pafupi ndi onse oitanila pa iye.”—Salimo 145:18

Mulungu amafuna kukuthandizani.

Yesu anati: “Ndani pakati panu amene mwana wake atamupempha mkate, iye angamupatse mwala? Kapena atamupempha nsomba, kodi angamupatse njoka? Cotelo ngati inuyo, . . . mumadziŵa kupeleka mphatso zabwino kwa ana anu, kuli bwanji Atate wanu wakumwamba? Ndithudi, iye adzapeleka zinthu zabwino kwa onse om’pempha!” (Mateyu 7:9-11) Zoonadi, Mulungu akukupemphani kupemphela kwa iye cifukwa “amakudelani nkhawa” ndipo amafuna kukuthandizani. (1 Petulo 5:7) Iye akukupemphaninso kuti muzimuuza mavuto anu. Baibulo limatiuza kuti: “Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa ciliconse, mwa pemphelo ndi pembedzelo, pamodzi ndi ciyamiko, zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu.”—Afilipi 4:6.

Anthu amafunika zinthu za kuuzimu.

Akatswili oona pa zaumoyo wa anthu, apeza kuti anthu mamililiyoni amaona kuti kupemphela n’kofunika. Ngakhale anthu amene sakhulupilila kuti kuli Mulungu, naonso amaona kufunika kopemphela.a Zimenezi zingoonetsa kuti anthu analengedwa kuti azikonda zinthu za kuuzimu. Yesu anati: “Odala ndi anthu amene amazindikila zosoŵa zao zauzimu.” (Mateyu 5:3) Conco, njila yabwino yokhutilitsila zosoŵa zimenezo ndi kukambilana ndi Mulungu nthawi zonse.

Tingapindule bwanji ngati tivomeleza ciitano ca Mulungu cakuti tizipemphela kwa iye?

a Mu 2012, bungwe lofufuza nkhani la Pew Research Center, linapeza kuti ku United States, 11 pelesenti ya anthu amene sakhulupilila kuti kuli Mulungu, amapemphela kamodzi pa mwezi.

Kodi Pemphelo Limaphatikizapo Zinthu Ziti?

Baibulo limatiuza kuti pemphelo limakhudza mbali zonse za umoyo wathu. Tingapemphele pa zinthu zotsatilazi:

  • Kuulula Macimo “Ndinaulula chimo langa kwa inu, ndipo sindinabise colakwa canga.”—Salimo 32:5.

  • Kuyamika “Ndi bwino kuyamika inu Yehova.”—Salimo 92:1.

  • Kutamanda “Ndidzatamanda Yehova nthawi zonse. Ndidzamutamanda ndi pakamwa panga mosalekeza.”—Salimo 34:1.

  • Kupempha Citsogozo “Ndiyendetseni m’njila ya malamulo anu, Pakuti ndikukondwela ndi njila imeneyi.”—Salimo 119:35.

  • Kupempha Mphamvu “Ndiceukileni ndi kundikomela mtima. Patsani mtumiki wanu mphamvu.”—Salimo 86:16.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani