Anthu a Yehova “Aleke Kucita Zosalungama”
“Aliyense wochula dzina la Yehova aleke kucita zosalungama.”—2 TIM. 2:19.
1. N’ciani cofunika kwambili pa kulambila kwathu?
KODI munalionapo dzina la Yehova litalembedwa pa zipupa za nyumba kapena pa zinthu m’nyumba zosungilamo zinthu zakale? Mwacionekele, zimenezo zinakukondweletsani. Pokhala Mboni za Yehova, dzina la Mulungu n’lofunika kwambili pa kulambila kwathu. Padziko lonse lapansi palibe gulu limene limagwilitsila nchito kwambili dzina la Mulungu monga mmene ifeyo timacitila. Komabe, timadziŵa kuti mwai wodziŵika ndi dzina la Mulungu limeneli umafuna kucita zoonjezeleka.
2. Mwai wathu wochedwa ndi dzina la Mulungu umafuna kuti tizicita zinthu zoonjezeleka ziti?
2 Kugwilitsila nchito dzina la Mulungu kokha sikungatiyanjanitse ndi Yehova. Timafunikila kutsatila miyezo yake ya makhalidwe abwino. Ndiye cifukwa cake Baibulo limatikumbutsa kuti, anthu a Yehova afunika ‘kupatuka pa zinthu zoipa.’ (Sal. 34:14) Mtumwi Paulo mosapita m’mbali anaonetsa mfundo imeneyi pamene analemba kuti: “Aliyense wochula dzina la Yehova aleke kucita zosalungama.” (Ŵelengani 2 Timoteyo 2:19.) Monga Mboni zake, timadziŵika kuti timalemekeza dzina la Yehova. Koma kodi tingaleke bwanji kucita zosalungama?
“PATUKANI” PA ZINTHU ZOIPA
3, 4. Ndi lemba liti limene limacititsa cidwi akatswili a Baibulo? Nanga n’cifukwa ciani?
3 Ganizilani cimene cinacititsa kuti Paulo alembe mau a pa 2 Timoteyo 2:19. Lembali limanena za “maziko olimba a Mulungu,” ndiyeno limachulanso za mauthenga aŵili ozokotedwa pamenepo. Uthenga woyamba ndi wakuti “Yehova amadziŵa anthu ake.” Ndipo mwacionekele, Paulo anagwila mau a pa lemba la Numeri 16:5. (Onani nkhani yapita.) Waciŵili ndi wakuti, “Aliyense wochula dzina la Yehova aleke kucita zosalungama.” Mauthenga amenewa amawacititsa cidwi akatswili a Baibulo. Nanga n’cifukwa ciani?
4 Mau a Paulo aonetsa kuti iye anagwila mau a malemba ena. Komabe, m’Malemba Aciheberi mulibe mau ogwilizana ndi amene Paulo anagwila. Conco, kodi mtumwi Paulo anali kukamba ciani pamene anati: “Aliyense wochula dzina la Yehova aleke kucita zosalungama”? Atanena mau amenewa, Paulo anagwila mau a pa Numeri caputala 16, onena za kupanduka kwa Korah. Kodi uthenga waciŵili ndi wogwilizananso ndi kupanduka kumeneko?
5-7. Ndi zocitika ziti za m’nthawi ya Mose zimene zimagwilizana ndi zimene Paulo analemba pa 2 Timoteyo 2:19? (Onani cithunzi cili kuciyambi kwa nkhani ino.)
5 Baibulo limanena kuti ana a Eliyabu, Datani ndi Abiramu, anagwilizana ndi Kora monga atsogoleli kuti aukile Mose ndi Aroni. (Num. 16:1-5) Iwo mosabisa anatsutsa Mose ndi kukanilatu utsogoleli wake wopatsidwa ndi Mulungu. Apandu amenewa anapitilizabe kukhala pakati pa anthu a Yehova ndi kuononga ubwenzi wa anthuwo ndi Mulungu. Pamene nthawi inafika, Yehova anapeleka malangizo omveka kuti asiyanitse alambili okhulupilika ndi apandu.
6 Lembali limati: “Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: ‘Uza khamulo kuti, “Cokani kumahema a Kora, Datani ndi Abiramu!”’ Kenako Mose ananyamuka n’kupita kwa Datani ndi Abiramu, ndipo akulu a Isiraeli anapita naye limodzi. Atafika anauza khamulo kuti: ‘Conde, cokani kumahema a anthu oipawa, ndipo musakhudze cinthu cao ciliconse, kuti musaphedwe nao limodzi cifukwa ca kucimwa kwao.’ Nthawi yomweyo anthuwo anacoka kumbali zonse za mahema a Kora, Datani ndi Abiramu. Zitatelo, Datani ndi Abiramu anatuluka n’kuima pamakomo a mahema ao, limodzi ndi akazi ao, ana ao.” (Num. 16:23-27) Ndiyeno, Yehova anapha apandu onse. Koma alambili okhulupilika amene anapatuka pa zinthu zoipa ndi kuleka kucita zosalungama anapulumuka.
7 Yehova amaona mitima, ndipo amadziŵa kukhulupilika kwa anthu ake. Komabe, anthu ake anafunikila kucitapo kanthu mwa kupatukana ndi anthu osakhulupilikawo. Conco, n’zomveka kuti Paulo anali kukamba za nkhani ya pa Numeri 16:5, 23-27 pamene analemba kuti: “Aliyense wochula dzina la Yehova aleke kucita zosalungama.” Izi zigwilizana ndi mau a Paulo akuti: “Yehova amadziŵa anthu ake.”—2 Tim. 2:19.
“UZIKANA MAFUNSO OPUSA NDI OPANDA NZELU”
8. N’cifukwa ciani kugwilitsila nchito dzina la Yehova kapena kukhala mbali ya mpingo sikokwanila?
8 Pochula zocitika za m’nthawi ya Mose, Paulo anali kukumbutsa Timoteyo kufunika kocitapo kanthu kuti ateteze ubwenzi wake wamtengo wapatali ndi Yehova. Kungokhala mbali ya mpingo sikunali kokwanila monga mmene kungochula dzina la Yehova sikunali kokwanila m’nthawi ya Mose. Mosazengeleza alambili okhulupilika anayenela ‘kuleka kucita zosalungama.’ Kodi zimenezi zinam’khudza bwanji Timoteyo? Nanga masiku ano anthu a Yehova aphunzilapo ciani pa uphungu wouzilidwa wa Paulo?
9. “Mafunso opusa ndi opanda nzelu” anaukhudza bwanji mpingo wacikristu woyambilila?
9 Baibulo lili ndi malangizo acindunji okhudza zosalungama zimene Akristu ayenela kuleka kapena kukana. Mwacitsanzo, m’mau ake a patsogolo pa lemba la 2 Timoteyo 2:19, Paulo anauza Timoteyo kuti “asamakangane pa mau” ndi kuti “azipewa nkhani zopeka.” (Ŵelengani 2 Timoteyo 2:14, 16, 23.) Anthu ena mumpingo anali kulimbikitsa ziphunzitso zampatuko. Ndipo ena anali kuyambitsa maganizo opotoka. Ngakhale kuti anthuwo sanali kutsutsa malemba mwacindunji, io anali kucititsa magaŵano. Anacititsa kuti anthu mumpingo ayambe kukangana pa mau ndipo mumpingo munaloŵa mzimu woipa. Ndiye cifukwa cake Paulo anawagogomezela kuti ‘azikana mafunso opusa ndi opanda nzelu.’
10. Tiyenela kucitanji tikakumana ndi ampatuko?
10 Masiku ano, anthu a Yehova sakumana ndi ampatuko mumpingo. Komabe, tisazengeleze kukaniza ziphunzitso zilizonse zosagwilizana ndi malemba. Ndi kupanda nzelu kukangana ndi ampatuko kaya pamaso m’pamaso, pa webusaiti yao, kapena mwanjila ina iliyonse. Ngakhale pamene colinga ndico kuthandiza winawake, kukambitsilana kwa conco n’kosafunika malinga n’zimene tangokambitsilana. M’malo mwake, monga anthu a Yehova tiyenela kupewelatu ampatuko.
11. N’ciani cingayambitse ‘mafunso opanda nzelu’? Nanga akulu mu mpingo angaonetse bwanji citsanzo cabwino?
11 Kupatulapo mpatuko, pali zinthu zina zimene zingaononge mtendele wa mpingo. Mwacitsanzo, nkhani yosankha zosangulutsa ingayambitse “mafunso opusa ndi opanda nzelu.”Ngati ena mumpingo akonda zosangulutsa zosagwilizana ndi miyezo ya makhalidwe a Yehova, akulu sayenela kulekelela makhalidwe amenewo pofuna kupewa mikangano. (Sal. 11:5; Aef. 5:3-5) Komabe, ayenela kusamala kuti asazilimbikitsa maganizo ao. Iwo ayenela kutsatila uphungu wa oyang’anila acikristu wakuti: “Wetani gulu la nkhosa za Mulungu lomwe analisiya m’manja mwanu, . . . Osati mocita ufumu pa anthu amene ali coloŵa cocokela kwa Mulungu, koma mukhale zitsanzo kwa gulu la nkhosa.”—1 Pet. 5:2, 3; ŵelengani 2 Akorinto 1:24.
12, 13. (a) Kodi Mboni za Yehova zimati bwanji pankhani yosankha zosangulutsa? Nanga ndi mfundo ziti za m’Baibulo zimene tingatsatile? (b) N’cifukwa ciani mfundo zili mu ndime 12 zingagwilenso nchito pankhani zina zaumwini?
12 Pankhani ya zosangulutsa, gulu lathu silichula mafilimu, maseŵela a pavidiyo, mabuku kapena nyimbo zimene tiyenela kupewa. N’cifukwa ciani silimatelo? Cifukwa cakuti Baibulo limalimbikitsa aliyense wa ife ‘kugwilitsa nchito mphamvu zake za kuzindikila, . . . kusiyanitsa coyenela ndi cosayenela.’ (Aheb. 5:14) Malemba ali ndi mfundo zimene zingatithandize posankha zosangulutsa. Pa umoyo wathu wonse, ‘nthawi zonse tizitsimikiza kuti covomelezeka kwa Ambuye n’citi.’ (Aef. 5:10) Baibulo limakamba kuti mitu ya banja ili ndi udindo m’banja. Conco, mutu wa banja ungaone zosangulutsa zosayenelela banja lake.a—1 Akor. 11:3; Aef. 6:1-4.
13 Mfundo za m’Baibulo zimene takambilana sizigwila cabe nchito pankhani yokhudza zosangulutsa. Kusiyana maganizo pankhani ya kavalidwe ndi maonekedwe, thanzi, zakudya, ndi nkhani zina zaumwini, kungayambitsenso mikangano. Komabe, ngati palibe mfundo za m’Baibulo zimene zanyalanyazidwa, anthu a Yehova amapewa kukangana ndi ena pankhani zimenezi. Iwo amadziŵa kuti “kapolo wa Ambuye sayenela kukangana ndi anthu, koma ayenela kukhala wodekha kwa onse.”—2 Tim. 2:24.
PEWANI KUGWILIZANA NDI ANTHU OIPA
14. Kodi Paulo anagwilitsila nchito fanizo lotani kuonetsa kuti sitifunika kugwilizana ndi anthu oipa?
14 Kodi anthu amene ‘amachula dzina la Yehova aleka kucita zosalungama’ m’njila zina ziti? Amapewa kugwilizana ndi anthu amene amacita zosalungama. Ndiye cifukwa cake Paulo ananena fanizo lina pambuyo ponena fanizo la kukhala ndi “maziko olimba a Mulungu.” Iye analemba za “m’nyumba yaikulu” mmene simumakhala “ziwiya zagolide ndi zasiliva zokha ai, koma mumakhalanso zamtengo ndi zadothi. Ziwiya zina zimakhala za nchito yolemekezeka koma zina zimakhala za nchito yonyozeka.” (2 Tim. 2:20, 21) Ndiyeno, Paulo analimbikitsa Akristu ‘kupewa’ kapena kuzipatula ku ziwiya za ‘nchito yonyozeka.’
15, 16. Tiphunzilapo ciani pa fanizo la ‘nyumba yaikulu’?
15 Kodi fanizo limeneli litanthauza ciani? Paulo anayelekezela mpingo wacikristu ndi ‘nyumba yaikulu,’ ndipo anayelekezela anthu a mumpingo ndi “ziwiya,” kapena kuti zinthu za m’nyumba. Nthawi zina ziwiya za m’nyumba zingaipitsidwe ndi mankhwala akupha kapena zingakhale ndi uve. Ndipo mwininyumba sangaike ziwiya za conco pamodzi ndi ziwiya zaukhondo, monga ziwiya zophikila.
16 Mofananamo, anthu a Yehova masiku ano pofuna kukhala a aukhondo, amapewa kugwilizana ndi anthu a mumpingo amene amanyalanyaza malamulo a Yehova. (Ŵelengani 1 Akorinto 15:33.) Conco, ngati tingapewe anthu a mu mpingo, bwanji ponena za ‘kupatukana’ ndi anthu akunja amene ambili a io ndi ‘okonda ndalama, osamvela makolo, osakhulupilika, odyelekeza, owopsa, osakonda zabwino, aciwembu, okonda zosangalatsa, m’malo mokonda Mulungu?’—2 Tim. 3:1-5.
YEHOVA ADZATIDALITSA NGATI SITIZENGELEZA
17. Kodi Aisiraeli okhulupilika anaonetsa bwanji kuti anakanilatu kucita zosalungama?
17 Baibulo limanena mosapita mbali kuti Aisiraeli sanazengeleze pamene anauzidwa kuti ‘acoke kumahema a Kora, Datani, ndi Abiramu.’ Nkhaniyo imati, “nthawi yomweyo anthuwo anacoka.” (Num. 16:24, 27) Iwo sanazengeleze kapena kuwayawaya. Lemba limenelo limanenanso kuti anatsatila mosamalitsa zimene anauzidwa. Anthu okhulupilikawo “anacoka kumbali zonse,” ndipo sanafune kuika moyo wao pa ngozi. Iwo sanamvele ndi mitima iŵili, koma anaonetsa kuti anali kumbali ya Yehova ndipo anakanilatu kucita zosalungama. Kodi tiphunzilepo ciani pa citsanzo cao?
18. N’cifukwa ciani Paulo anauza Timoteyo kuti “thaŵa zilakolako zaunyamata”?
18 Kuti titeteze ubwenzi wathu ndi Yehova, tiyenela kucitapo kanthu mwamsanga ndi mosazengeleza. Cifukwa ca zimenezi Paulo analimbikitsa Timoteyo kuti, “thaŵa zilakolako zaunyamata.” (2 Tim. 2:22) Panthawi imeneyo, Timoteyo anali wamkulu kale, mwina anali ndi zaka za m’ma 30. Komabe, zaka sizingacititse kuti munthu apewe “zilakolako zaunyamata” zoipa. Kuti Timoteyo apewe zilakolako zimenezi, anafunikila ‘kuzithaŵa.’ M’mau ena tingakambe kuti iye anafunikila ‘kuleka kucita zosalungama.’ Yesu anatiuza kucita zofanana ndi zimenezi pamene anakamba kuti: “Ngati diso lako limakupunthwitsa ulikolowole n’kulitaya.” (Mat. 18:9) Masiku ano, Akristu amene amatsatila malangizo amenewa ndi mtima wonse, sazengeleza kucitapo kanthu pa zinthu zimene zingawavulaze mwa kuuzimu.
19. Kodi ena masiku ano amacita ciani mosazengeleza kuti aziteteze mwa kuuzimu?
19 Ena amene anali kumwa moŵa kwambili asanakhale Mboni, anasankha kulekelatu kumwa moŵa. Ena amapewa zosangulutsa zimene sizolakwika koma zimene zingawacititse kukhala ndi zilakolako zoipa. (Sal. 101:3) Mwacitsanzo, M’bale wina asanakhale Mboni anali kukonda kupita kumaphwando kumene kunali kukhala mavinidwe oipa. Koma pamene anakhala mboni analekelatu kuvina ngakhale pa maphwando a Mboni, poopela kuti anagayambenso kuganizila zakale. Akristu sangafunike kulekelatu kumwa moŵa, kuvina kapena kulekelatu kucita zinthu zina zimene sizolakwika. Komabe, aliyense wa ife ayenela kucitapo kanthu mosazengeleza kuti aleke kucita ciliconse cimene cingam’vulaze mwa kuuzimu.
20. Ngakhale kuti n’zovuta ‘kuleka kucita zosalungama,’ n’ciani cimatithandiza kuleka kucita zimenezo?
20 Mwai wodziŵika ndi dzina la Mulungu umafuna kucita zambili. Tiyenela ‘kuleka kucita zosalungama’ ndi ‘kupatuka pa zinthu zoipa.’ (Sal. 34:14) N’zoona kuti kucita zimenezi sikopepuka nthawi zonse. Komabe, n’zolimbikitsa kudziŵa kuti Yehova adzapitilizabe kukonda “anthu ake” amene amatsatila njila zake zolungama.—2 Tim. 2:19; ŵelengani 2 Mbiri 16:9a.
a Onani nkhani yakuti “Kodi Muli ndi Lamulo Loletsa Mavidiyo Ena, Mabuku Ena Ndiponso Nyimbo Zina? pa jw.org, pa kamutu kakuti, ZOKHUDZA IFEYO > MAFUNSO OFUNSIDWA KAŴILIKAŴILI.