UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Akhristu Oona Amadziŵika na Cikondi—Kondwelani na Coonadi
CIFUKWA CAKE N’KOFUNIKA: Potengela citsanzo ca Yesu, tifunika kucitila umboni coonadi cokamba za colinga ca Mulungu. (Yoh. 18:37) Tifunikanso kukondwela na coonadi, kumakamba zoona komanso kumaganizila zilizonse za zoona, olo kuti tikukhala m’dziko lodzala mabodza ndiponso limene limacita zosalungama.—1 Akor. 13:6; Afil. 4:8.
MMENE TINGACITILE:
Tsimikizani mtima kuti musamamvele kapena kufalitsa misece.—1 Ates. 4:11
Musamakondwele wina akamavutika
Muzikondwela na zinthu zabwino ndiponso zolimbikitsa
TAMBITSANI VIDIYO YAKUTI “MUZIKONDANA”—KONDWELANI NDI COONADI OSATI NDI ZOSALUNGAMA, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO OTSATILAWA:
Kodi mlongo Debbie “anakondwela ndi zosalungama” m’lingalilo lanji?
Nanga mlongo Alice anasintha bwanji makambilano awo na mlongo Debbie kuti akhale oyenela?
Ni zinthu zabwino ziti zimene tingakambilane?
Kondwelani na coonadi osati na zosalungama