NASA Photo
KHALANI MASO!
Kodi Pali Boma Lodalilika Limene Lingalamulile Dziko Lapansi?—Kodi Baibo Ikambapo Ciyani?
Maboma padziko lonse lapansi akukumana ndi zovuta zambili. Ngakhale m’maiko amene akuoneka kuti zinthu zikuwayendela, maboma a kumeneko agwedezeka cifukwa ca malipoti okhudza zocita za andale, kuvuta kwa masankho, kukangana pakati pa zipani za ndale, komanso zipolowe.
Baibo imatiuza kuti pali boma limodzi lomwe ndi lodalilika. Mwina munavampo kale za boma limeneli. Bomali ndi lija limene Yesu anachula m’pemphelo la Ambuye.
“Koma inu muzipemphela motele: ‘Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeletsedwe. Ufumu wanu ubwele. Cifunilo canu cicitike, monga kumwamba cimodzimodzinso pansi pano.’”—Mateyo 6:9, 10.
Kodi Baibo imati ciyani ponena za Ufumu umenewu?
Ufumuwu ndi boma lodalilika
Ufumuwu ukulamulila kucokela kumwamba.
Yesu anachula boma limeneli kuti “Ufumu wakumwamba.” (Mateyo 4:17; 5:3, 10, 19, 20) Conco m’pomveka kuti iye anati: “Ufumu wanga si wam’dzikoli.”—Yohane 18:36.
Ufumuwu udzalowa m’malo maboma a anthu.
Baibo imakamba kuti: “Ufumu umenewu . . . udzaphwanya n’kuthetsa maufumu [a anthu] onsewa, ndipo ndi ufumu wokhawu umene udzakhalepo mpaka kalekale.”—Danieli 2:44.
Ufumuwu, umene ukulamulidwa ndi Yesu Khristu, sudzawonongedwa.
Baibo imakamba kuti: “Ulamulilo wake udzakhalapo mpaka kalekale ndipo sudzatha. Ufumu wake sudzawonongedwa.”—Danieli 7:13, 14.
Ufumuwu udzabweletsa mtendele komanso citetezo padziko lapansi.
Baibo imakamba kuti: “Aliyense adzakhala mwamtendele pansi pa mtengo wake wa mpesa ndi mtengo wake wa mkuyu palibe amene adzawacitisa mantha.”—Mika 4:4, Good News Translation.
Dziwani zambili zokhudza Ufumu umenewu
Yesu ali padziko lapansi, anathela nthawi yake yoculuka “kulalikila uthenga wabwino wa Ufumu.” (Mateyo 9:35) Iye anakambanso kuti:
“Uthenga wabwino uwu wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti udzakhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.”—Mateyo 24:14.
Masiku ano, uthenga wabwino wa Ufumu umenewu ukulalikidwa m’maiko okwana 240. Tikupemphani kuti muphunzile zambili za Ufumu umenewu komanso mmene mudzapindulila ndi ulamulilo wake.
Onelelani vidiyo yakuti Kodi Ufumu wa Mulungu N’ciani?