Kodi Mukumbukila?
Kodi munaŵelenga na kumvetsa bwino-bwino magazini aposacedwa a Nsanja ya Mlonda? Cabwino, tiyeni tione ngati mungayankhe mafunso aya:
Ni chimo lanji limene Yesu anali kukamba pa Mateyu 18:15-17?
Analukamba za nkhani imene anthu angakambilane ndi kuithetsa pakati pawo kumbali. Koma chimo limenelo munthu akhoza kucotsedwa nalo mumpingo ngati nkhaniyo siinathetsedwe. Mwacitsanzo, chimolo lingakhale misece kapena cinyengo.—w16.05, peji 7.
Mungacite ciani kuti muzipindula kwambili poŵelenga Baibo?
Mungacite izi: Muziŵelenga na maganizo oyenela, muziona mfundo zimene mungaseŵenzetse; muzidzifunsa mafunso monga akuti ‘Kodi mfundo izi ningaziseŵenzetse bwanji pothandiza ena?’; ndipo muziseŵenzetsa zida zimene muli nazo kuti mufufuze mfundo zowonjezela pa zimene mwaŵelenga.—w16.05, mapeji 24-26.
Kodi n’kulakwa Mkhiristu kulila malilo na kumva cisoni cifukwa amakhulupilila kuti akufa adzauka?
Pokhulupilila za ciukililo sikuti Mkhiristu samvela cisoni cifukwa ca kutaikidwa munthu mu imfa. Ngakhale Abulahamu analila imfa ya Sara. (Gen. 23:2) M’kupita kwa nthawi, cisoni cimayamba kucepa.—wp16.3, peji 4.
M’masophenya a Ezekieli, kodi mwamuna amene anali ndi kacola ka mlembi, konyamulilamo inki na zolembela, ndiponso amuna 6 onyamula zida zophwanyila, amaimila ndani?
Iwo amaimila angelo amphamvu amene anawononga mzinda wa Yerusalemu, ndipo adzawononganso dzikoli loipa la Satana pa Aramagedo. Masiku ano, wonyamula kacola ka inkiyo akuimila Yesu Khiristu, amene akuika cizindikilo anthu amene adzapulumuka.—w16.06, mapeji 31-32.
Kodi Baibo inapulumuka ku zinthu ziti?
Inapulumuka (1) kuti isawole cifukwa ca zimene anali kulembapo, monga gumbwa na zikopa (zikumba) za nyama; (2) kwa anthu andale ndi acipembedzo amene anafuna kuiwononga; ndi (3) kwa anthu ofuna kusintha uthenga wake.—wp16.4, mapeji 4-7.
Kodi Mkhiristu angacite ciani kuti akhale na umoyo wosalila zambili?
Lembani zinthu zimene mufunikila. Pewani kugula zinthu zosafunika kweni-kweni. Lembani bajeti imene mudzakwanitsa kuitsatila. Mungagulitse, kupatsa ena, kapena kutaya zinthu zimene munaleka kuseŵenzetsa. Bwezani nkhongole zimene mungakhale nazo. Cepetsani maovataimu pa nchito. Onani zimene mungacite kuti muwonjezele utumiki wanu.—w16.07, peji 10.
Kodi Baibo imati n’ciani camtengo wapatali kuposa golide na siliva?
Yobu 28:12, 15 ionetsa kuti nzelu zocokela kwa Mulungu ni zamtengo wapatali kuposa golide na siliva. Pamene muzifuna-funa yesetsani kukhala odzicepetsa ndi olimba m’cikhulupililo.—w16.08, mapeji 18-19.
Kodi n’koyenela m’bale kusunga ndevu?
Kumaiko ena, kusunga ndevu zodulila bwino-bwino n’kololeka, ndipo sikulepheletsa anthu kumvela uthenga wa Ufumu. Koma ngakhale kumaiko amenewo, abale ena angasankhe kusasunga ndevu. (1 Akor. 8:9) Koma kumaiko ena, ndevu sizololeka kwa Akhiristu.—w16.09, peji 21.
N’cifukwa ciani nkhani ya m’Baibo ya Davide na Goliyati ni yoona?
Goliyati anangopitilila ndi masentimita 15 cabe kuposa munthu wamtali kwambili amene anadziŵikapo masiku ano. Ndipo Davide anali munthu weni-weni. Zolemba zakale zimene zinachulako za “nyumba ya Davide na zimene Yesu anakamba, zimatsimikizila zimenezi. Ndipo zolembazo zigwilizana ndi zeni-zeni zimene akatswili apeza.—wp16.5, peji 13.
Kodi cidziŵitso, kumvetsa zinthu, na nzelu zimasiyana bwanji?
Munthu amene waphunzila mfundo na kuzisunga timati ali na cidziŵitso. Munthu amene amatha kuona mmene mfundo imodzi imagwilizanila ndi inzake timati amamvetsa zinthu. Koma munthu amene amatha kuseŵenzetsa bwino cidziwitso ndi kumvetsa zinthu, ndiye timati ali ndi nzelu.—w16.10, peji 18.