LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w17 October masa. 17-20
  • Yosefe wa ku Arimateya Analimba Mtima

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Yosefe wa ku Arimateya Analimba Mtima
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2017
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • MEMBALA WA KHOTI LALIKULU LA AYUDA
  • WOPHUNZILA WA YESU WAMSELI
  • ANATHETSA MANTHA
  • YOSEFE AIKA YESU M’MANDA
  • MMENE NKHANI YA YOSEFE INATHELA
  • Abale Ake Amuzonda Yosefe
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Yehova Sanamuiŵale Yosefe
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • ‘Tamvelani Maloto Awa’
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • Kapolo Amene Anamvela Mulungu
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2017
w17 October masa. 17-20
Yosefe wa ku Arimateya akamba na Pontiyo Pilato

Yosefe wa ku Arimateya Analimba Mtima

YOSEFE WA KU ARIMATEYA anali kuona kuti sangakwanitse kukaonana ndi Pontiyo Pilato, bwanamkubwa waciroma. Pilato anali munthu wosamva za ena. Koma Yosefe anali kudziŵa kuti mtembo wa Yesu sungaikiwe m’manda mwaulemu ngati sipapezeka munthu wokapempha Pilato kuti apeleke cilolezo cocotsa mtembowo. Yosefe atapita kukaonana ndi Pilato, anadabwa kuona kuti anamvela zimene anamupempha. Pilato atatsimikizila kwa kapitawo wa asilikali kuti Yesu wafa, anamulola Yosefe kukacotsa mtembowo. Panthawiyo, Yosefe, akali na cisoni cacikulu anabwelela mwamsanga ku malo amene Yesu anaphedwela.—Maliko 15:42-45.

  • Kodi Yosefe wa ku Arimateya anali ndani?

  • Kodi panali ubale wanji pakati pa iye na Yesu?

  • Nanga nkhani yake itikhudza bwanji masiku ano?

MEMBALA WA KHOTI LALIKULU LA AYUDA

Buku la Uthenga Wabwino la Maliko limakamba kuti Yosefe anali “munthu wodziŵika wa m’Bungwe Lalikulu la Ayuda.” Bungwe Lalikulu la Ayuda limene likuchulidwa apa ni Sanihedirini, kapena kuti khoti lalikulu la Ayuda. (Maliko 15:1, 43) Conco Yosefe anali mmodzi wa atsogoleli a Ayuda. N’cifukwa cake anali na ufulu wokaonana ndi bwanamkubwa waciroma. Ndipo n’zosadabwitsa kuti Yosefe anali munthu wolemela.—Mat. 27:57.

Kodi ndinu wolimba mtima cakuti mungavomeleze kuti Yesu ndiye Mfumu yanu?

Khoti Lalikulu la Ayuda linali kumuzonda Yesu. Mamembala ake ni amene anakonza ciwembu cakuti aphedwe. Komabe, Baibo imakamba kuti Yosefe anali “munthu wabwino ndi wolungama.” (Luka 23:50) Mosiyana na anzake ambili a m’khotiyo, iye anali munthu woona mtima, wakhalidwe labwino, ndipo anali kuyesetsa kumvela malamulo a Mulungu. Komanso anali “kuyembekezela ufumu wa Mulungu.” Mwina n’cifukwa cake anakhala wophunzila wa Yesu. (Maliko 15:43; Mat. 27:57) Mwacionekele, Yosefe anakopeka na uthenga wa Yesu cifukwa cakuti anali kukonda coonadi ndi cilungamo.

WOPHUNZILA WA YESU WAMSELI

Lemba la Yohane 19:38 limati Yosefe “anali wophunzila wa Yesu koma wamseli cifukwa anali kuopa Ayuda.” N’cifukwa ciani Yosefe anali kuwaopa Ayuda? Cifukwa anali kudziŵa kuti Ayuda sanali kumulemekeza Yesu. Anali kudziŵanso zimene Ayudawo anapangana, zakuti munthu aliyense wovomeleza kuti amakhulupilila Yesu, adzamucotsa m’sunagoge. (Yoh. 7:45-49; 9:22) Munthu akacotsedwa m’sunagoge anali kunyozewa, kusankhiwa, ndi kukaniwa na Ayuda anzake. N’cifukwa cake Yosefe anali kuopa kudzidziŵikitsa kuti anali kukhulupilila Yesu. Anali kuopa kucotsedwa pa udindo ndi kudzicotsela ulemu.

Si Yosefe yekha amene anali na mantha. Pa Yohane 12:42 pamati, “ambili, ngakhalenso olamulila anamukhulupilila [Yesu], koma cifukwa ca Afarisi sanavomeleze poyela, poopa kuti angawacotse musunagoge.” Munthu wina amene anali na vuto laconco ndi Nikodemo. Iye analinso membala wa Khoti Lalikulu la Ayuda.—Yoh. 3:1-10; 7:50-52.

Koma Yosefe anali wophunzila wa Yesu ngakhale kuti anali kuopa kudzidziŵikitsa kuti anali wophunzila wake. Limeneli linali vuto lalikulu, maka-maka tikakumbukila mau a Yesu akuti: “Aliyense wovomeleza pamaso pa anthu kuti ali kumbali yanga, inenso ndidzavomeleza pamaso pa Atate wanga wakumwamba kuti ndili kumbali yake. Koma aliyense wondikana ine pamaso pa anthu, inenso ndidzamukana pamaso pa Atate wanga wakumwamba.” (Mat. 10:32, 33) Yosefe sanam’kane Yesu, koma anali kuopa kuvomeleza pamaso pa anthu kuti anali kum’khulupilila. Kodi inunso mumaopa?

Baibo imakamba zinthu zina zabwino zokhudza Yosefe. Imakamba kuti iye sanagwilizane ndi ciwembu cimene Khoti Lalikulu la Ayuda linakonzela Yesu. (Luka 23:51) Malinga n’zimene ena amakamba, n’kutheka kuti Yosefe kunalibe panthawi imene Yesu anali kuweluzidwa. Mulimonse mmene zinalili, Yosefe ayenela kuti anakhumudwa kwambili na kupanda cilungamo kwakukulu kumeneku. Koma palibe zimene akanacita.

ANATHETSA MANTHA

Pofika nthawi imene Yesu anafa, Yosefe ayenela kuti analibenso mantha ndipo anayamba kucilikiza ophunzila a Yesu. Umboni wa zimenezi ni mau a pa Maliko 15:43. Lembali limati: “[Yosefe] anapita kwa Pilato molimba mtima kukapempha mtembo wa Yesu.”

Cioneka kuti Yosefe analipo pamene Yesu anafa. Iye anadziŵa kuti Yesu wafa Pilato asanadziŵe. Conco, pamene Yosefe anapempha mtembo wa Yesu, Pilato anayamba ‘kukayikila ngati [Yesu] anali atamwalila kale, conco anaitanitsa kapitawo wa asilikali ndi kumufunsa ngati iye anali atamwalila kale.’ (Maliko 15:44) Ngati Yosefe analipo pamene Yesu anali kuvutika na ululu pa mtengo wozunzikilapo, mwina zimene anaonazo zinamukhudza kwambili cakuti anaona kuti afunika kudzidziŵikitsa kuti ni wophunzila wa Yesu. Inde, zinamulimbikitsa kucitapo kanthu. Iye anatsimikiza mtima kuti sadzadzibisanso kuti ni wophunzila wa Yesu.

YOSEFE AIKA YESU M’MANDA

Malamulo aciyuda anali akuti anthu amene aweluzidwa kuti aphedwe, akafa anafunika kuikidwa m’manda dzuŵa lisanaloŵe. (Deut. 21:22, 23) Koma kwa Aroma, anthu opalamula akaphedwa, mitembo yawo inali kusiyidwa pamtengo mpaka kuwola, ndipo nthawi zina anali kuitaya m’manda a anthu onse. Yosefe sanafune kuti zimenezi zicitikile mtembo wa Yesu. Yosefe anali na manda ogobedwa muthanthwe m’munda wina wa pafupi na pamene Yesu anaphedwela. Baibo imakamba kuti m’manda amenewo anali asanaikemo munthu cikhalile. Izi zionetsa kuti Yosefe anali atakukila ku Yerusalemu camanje-manje kucoka ku Arimateya,a ndipo m’mandamo anali kufuna kuti aziikamo anthu a m’banja lake. (Luka 23:53; Yoh. 19:41) Conco, Yosefe anaonetsa kuwoloŵa manja kwakukulu mwa kuika Yesu m’manda ake am’tsogolo. Zimenezo zinakwanilitsanso ulosi wa m’Baibo wakuti Mesiya adzaikiwa m’manda “limodzi ndi anthu olemela.”—Yes. 53:5, 8, 9.

Kodi pali ciliconse cimene mumaona kuti n’cofunika ngako kuposa ubwenzi wanu na Yehova?

Anthu akutsitsa mtembo wa Yesu pa mtengo wozunzikilapo

Mabuku onse anayi a Uthenga Wabwino amakamba kuti mtembo wa Yesu atautsitsa pamtengo wozunzikilapo, Yosefe anaukulunga munsalu yabwino kwambili na kukauika m’manda ake. (Mat. 27:59-61; Maliko 15:46, 47; Luka 23:53, 55; Yoh. 19:38-40) Nikodemo yekha na amene amachulidwako kuti anathandiza Yosefe. Iye anabweletsa zonukhilitsa mtembo. Popeza kuti amuna aŵiliwa anali olemekezeka kwambili, n’zokayikitsa kuti ananyamulako mtembowo. Iwo ayenela kuti analamula anchito awo kuti aunyamule na kukauika m’manda. Ngakhale ngati zinali conco, nchito imene Yosefe na Nikodemo anagwila siinali yocepa. Takamba conco cifukwa munthu aliyense amene wakhudza mtembo anali kukhala wodetsedwa kwa masiku 7, ndipo ciliconse cimene wakhudza cinali kukhalanso codetsedwa. (Num. 19:11; Hag. 2:13) Kukhala odetsedwa kukanacititsa kuti iwo asakhale na mwayi wopezeka pa mwambo wa Pasika, kuphatikizapo pa zikondwelelo na zocitika zina zokhudzana ndi mwambowu. (Num. 9:6) Komanso, zimene Yosefe anacita, zoika Yesu m’manda zikanacititsa kuti anzake asamam’lemekeze. Komabe, panthawiyi Yosefe anali wokonzeka kuika Yesu m’manda mwaulemu ndi kudzidziŵikitsa kuti anali wophunzila wa Khristu, mosasamala kanthu za mavuto amene akanakumana nawo cifukwa cocita zimenezo.

MMENE NKHANI YA YOSEFE INATHELA

Pambuyo pokamba za kuikiwa m’manda kwa Yesu, Baibo siikambakonso za Yosefe wa ku Arimateya. Izi zingaticititse kufunsa kuti: ‘N’ciani cinamucitikila pambuyo pake?’ Kukamba mwacidule, sitidziŵa. Koma malinga n’zimene takambilana, pali umboni wokwanila wakuti iye anayamba kudzidziŵikitsa kuti ni Mkhristu. Monga taonela, panthawi yovuta ndi ya ciyeso, m’pamene cikhulupililo na kulimba mtima kwake zinali kukulila-kulila. Ici cinali cizindikilo cakuti anapita patsogolo.

Nkhani ino ikubweletsa funso limene aliyense wa ise afunika kuliganizila mozama. Funso lake n’lakuti: Kodi pali ciliconse—kaya udindo, nchito, cuma, cibululu, kapena ufulu wathu—cimene timaona kuti n’cofunika ngako kuposa ubwenzi wathu na Yehova?

a Cioneka kuti Arimateya ni malo amodzi-modzi amene anali kuchedwa Rama, dela limene masiku ano amati Rentis (Rantis). Kumeneku ndiye kunali kwawo kwa mneneli Samueli. Delali linali pamtunda wa makilomita 35 kum’poto cakum’madzulo kwa Yerusalemu.—1 Sam. 1:19, 20.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani