Maulaliki Acitsanzo
Kuyambitsa Maphunzilo a Baibo pa Ciŵelu Coyamba mu February
“Anthu ambili amaona kuti Mdyelekezi ndiye amacititsa zinthu zoipa m’dziko. Koma amadzifunsa kuti: ‘Kodi Mdyelekezi anacokela kuti?’ Kodi Mulungu ndiye anamulenga? Nanga inu muganiza bwanji? [Yembekezani yankho.] Onani zimene magazini iyi ikamba.” Muonetseni nkhani ili patsamba lothela kucikuto ca Nsanja ya Olonda ya February 1. Ndiyeno kambilanani naye ndime yoyamba ndi lemba lake losagwidwa mau. Kenako, m’gaŵileni magazini ndi kupangana naye kuti mukabwelenso kudzakambilana funso lotsatila.
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova February 1
“Tifuna kumvako maganizo anu ponena za munthu amene Akristu, Ayuda, ndi Asilamu amamulemekeza kwambili. Munthu ameneyu ndi Mose. Mukamva dzina limeneli, kodi n’ciani cimene cimabwela msanga m’maganizo mwanu? [Yembekezani yankho.] Ngakhale kuti Mose anali ndi zophophonya, n’zosangalatsa kuona zimene Baibo imakamba ponena za iye. [Ŵelengani Deuteronomo 34:10-12.] Magazini iyi ifotokoza ena a makhalidwe ake abwino atatu ndi mmene tingatsatilile citsanzo cake.”
Galamukani! February
“Masiku ano, anthu ambili amakonda kusamukila kumaiko ena pofuna umoyo wabwino. Kodi muganiza kuti nthawi zonse amazipeza zimene amafuna-funa? [Yembekezani yankho.] Kusamukila kumaiko ena sikunayambe lelo. Onani citsanzo ici colembedwa m’buku loyamba la m’Baibo. [Ŵelengani Genesis 46:5, 6.] Magazini iyi iyankha mafunso awa.” Muonetseni mafunso ali kumapeto kwa tsamba 6.