LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • km 1/14 tsa. 4
  • Maulaliki Acitsanzo

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Maulaliki Acitsanzo
  • Utimiki Wathu wa Ufumu—2014
  • Nkhani Zofanana
  • Maulaliki Acitsanzo
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Maulaliki Acitsanzo
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2014
  • Maulaliki Acitsanzo
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Maulaliki Acitsanzo
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2013
Onaninso Zina
Utimiki Wathu wa Ufumu—2014
km 1/14 tsa. 4

Maulaliki Acitsanzo

Kuyambitsa Maphunzilo a Baibo pa Ciŵelu Coyamba mu February

“Anthu amaona Baibo mosiyana-siyana. Ena amati ndi Mau a Mulungu, koma ena amati ndi buku wamba. Kodi inu mumaliona bwanji?” Yembekezani ayankhe. Muonetseni nkhani ili patsamba lothela kucikuto kwa Nsanja ya Mlonda ya February 1, ndi kukambilana naye nkhani ili pansi pa funso loyamba ndipo ŵelengani naye lemba ngakhale limodzi pa malembawo. Kenako m’gaŵileni magazini ndi kupangana kuti mukabwelenso kudzakambilana naye funso lotsatila.

Nsanja ya Mlonda February 1

“Anthu amafuna kuona nkhondo itatha. Kodi muganiza kuti zingatheke kukhala ndi mtendele wa dziko lonse? [Yembekezani ayankhe] Onani lonjezo la m’Malemba ili. [Ŵelengani Salimo 46:9] Magazini iyi ifotokoza zocitika pa Nkhondo Yoyamba ya dziko lonse ndipo itithandiza kukhala ndi cidalilo cakuti posacedwapa Mulungu adzakwanilitsa ulosi wake wakuti adzathetselatu nkhondo.”

Galamukani! February

“Mwacidule tikambilana ndi anthu ponena za vuto limene lafala. Zioneka kuti timasoŵa nthawi yokwanila yakuti ticite zonse zimene afuna kucita. Kodi muganiza kuti timasoŵa nthawi cifukwa cokhala ndi zocita zambili kapena ndi cifukwa coononga nthawi yoculuka? [Yembekezani ayankhe.] Ambili sadziŵa kuti Baibo ili ndi malangizo amene angatithandize kugwilitsila nchito bwino nthawi. Lekani tione citsanzo pa mbali imeneyi. [Ŵelengani Afilipi 1:10a]. Magazini iyi ifotokoza zinthu zinai zimene zathandiza anthu ambili kugwilitsila nchito nthawi yao mwanzelu.”

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani