Kupelekela Munthu Magazini Kumathandiza Kuyambitsa Maphunzilo a Baibo
1. N’cifukwa ciani gulu la Yehova lakhala likulimbikitsa ofalitsa kupanga makonzedwe opelekela anthu ena magazini?
1 Anthu ambili safuna kuti tiziphunzila nao Baibo, koma amafuna kuŵelenga magazini athu. Conco, gulu la Yehova lakhala likulimbikitsa ofalitsa kupanga makonzedwe opelekela anthu ena magazini. Kaŵili-kaŵili, anthu amene amaŵelenga magazini athu amalaka-laka Mau a Mulungu. (1 Pet. 2:2) Nthawi zina io angaŵelenge nkhani imene ingawasangalatse, ndipo angavomeleze kuphunzila Baibo.
2. Kodi tingakulitse bwanji cidwi ca anthu amene timapelekela magazini?
2 ‘Muzithilila’ Mbeu za Coonadi: M’malo mongosiila mwininyumba magazini, kambilanani naye ndipo yesetsani kuzoloŵelana naye. Kucita zimenezi kudzakuthandizani kudziŵa mmene umoyo wake ulili, zimene amakonda, ndi zikhulupililo zake, ndipo izi zidzakuthandizani kukambilana naye mosamala. (Miy. 16:23) Muzikonzekela ulendo wobwelelako uliwonse. Ngati n’kotheka, mwacidule chulani mfundo imene igwilizana ndi lemba limene lili m’magazini, kuti muthilile mbeu iliyonse ya coonadi mumtima mwake. (1 Akor. 3:6) Nthawi iliyonse mukapanga ulendo wobwelelako, muzilemba deti, cofalitsa cimene mwasiya, nkhani imene mwakambilana ndi malemba ake.
3. Kodi tizibwelelako kangati kwa anthu amene timapelekela magazini?
3 Kodi Tizibwelelako Kangati? Mwezi ulionse mufunikila kupanga ulendo wobwelelako umodzi kuti mupeleke magazini atsopano. Koma ngati mikhalidwe yanu ilola ndipo munthuyo ali ndi cidwi, mungapange maulendo obwelelako angapo. Mwacitsanzo, ngati papita mlungu umodzi kapena iŵili kucokela pamene munasiya magazini, mungabweleleko ndi kukamba kuti, “Ndafika pano kuti ndikuonetseni mwacidule mfundo yosangalatsa ili m’magazini amene ndinakusiilani.” Izi zidzacititsa munthuyo kukhala ndi cifuno coŵelenga nkhani ina. Ngati anaŵelenga kale, mungamupemphe kuti afotokoze mwacidule maganizo ake pa nkhaniyo ndi kukambilana naye mwacidule. Ndiponso ngati iye amakonda kuŵelenga mabuku athu, mungapange ulendo wobwelelako ndi kum’gaŵila kapepala ka uthenga, kabuku, kapena buku limene tigaŵila mweziwo.
4. Kodi tiyenela kupitiliza kucita ciani kuti tione ngati anthu amene timapelekela magazini angakonde kuphunzila Baibo?
4 M’malo moyembekeza kuti mwininyumba akupempheni phunzilo la Baibo, yambani ndinu. Ngakhale kuti anakana kuphunzila Baibo, mungakambilane naye mbali yakuti “Kuyankha Mafunso a m’Baibo” ya mu Nsanja ya Mlonda ndi kuona ngati angavomeleze makambilano. Mwina mungayambe kumatsogoza phunzilo lacidule. Koma ngati sitinakhazikitse phunzilo la Baibo, muyenela kupitilizabe kupeleka magazini kuti mukulitse cidwi cake.