Maulaliki Acitsanzo
Ogwilitsila Nchito Poitanila Anthu ku Cikumbutso
“Tikupatsa anthu tumapepala towaitanila ku mwambo wofunika kwambili. Pa April 14, anthu mamiliyoni padziko lonse lapansi adzasonkhana kuti akumbukile imfa ya Yesu Kristu, ndipo adzamvetsela nkhani ya m’Baibulo yaulele imene idzafotokoza mapindu amene tingapeze cifukwa ca imfa yake. Pa kapepala aka pali malo ndi nthawi kumene kudzacitikila mwambo umenewu m’dela lathu.”
Nsanja ya Mlonda April 1
“Tikucezela anthu mwacidule kuti tikambitsilane nao zinthu zimene anthu ambili amacita. Pafupi-fupi munthu aliyense, kaya ndi wa m’cipembedzo cotani amapemphela. Kodi muganiza kuti Mulungu amayankha mapemphelo? Kapena kodi muganiza kuti mapemphelo amangocititsa wina kumva bwino ngati ali ndi mavuto? [Yembekezani ayankhe.] Onani zimene Baibulo limanena pa nkhani ya pemphelo. [Ŵelengani 1 Yohane 5:14.] Magazini iyi ifotokoza mmene pemphelo lingatipindulitsile.”
Galamukani! April
“Tabwela kuti tikambilane kumene tingapeze thandizo pa mavuto amene afala kwambili. Anthu ena atopa ndi mavuto a umoyo wao cakuti amangoganiza kuti kufa ndiko yankho. Tsopano munthu akakhala ndi mavuto, kodi muganiza kuti amafunadi kufa, kapena amangofuna thandizo pa mavuto ake? [Yembekezani kuti ayankhe.] Tiyeni tione lonjezo la m’Baibulo limene lathandiza anthu ambili kukhala ndi maganizo oyenela. [Ŵelengani Chivumbulutso 21:3, 4.] Magazini iyi ifotokoza zifukwa zitatu zomveka zothandiza munthu kukhalabe ndi moyo mosasamala kanthu za mavuto ake.”