Maulaliki Acitsanzo
Nchito Yogaŵila Tumapepala Toitanila Anthu Ku Cikumbutso
“Tikuitanila anthu ku cocitika capadela kwambili. Pa April 3, anthu mamiliyoni pa dziko lonse lapansi adzakumana kuti akumbukile imfa ya Yesu Kristu ndi kumvetsela ku nkhani ya anthu onse imene idzafotokoza mmene timapindulila ndi imfa yake. Kapepala kaciitano aka kakuonetsa nthawi ndi malo kumene tidzacitila mwambo umenewu kuno kwathu.”
Nsanja ya Mlonda January-February
“Zikuoneka kuti ciphuphu ca m’boma cakhala vuto lalikulu. Muganiza n’cifukwa ciani zili conco? [Yembekezani ayankhe.] Ndaona kuti mfundo iyi ya m’Baibulo ndi yocititsa cidwi. [Ŵelengani Mlaliki 7:20.] Magazini iyi ikufotokoza njila ya Baibulo yothetsela ciphuphu. Tikupemphani kupatula nthawi yakuti muiŵelenge. Tengani iyi ndi yanu.”
Galamukani! March
“Tikucezela anzathu mwacidule kuti tiwaonetse nkhani yatsopano imene ili mu Galamukani! iyi. [Muonetseni pacikuto.] Anthu ali ndi maganizo osiyana pa funso ili lakuti: ‘Kodi Mulungu aliko?’ Kodi muona kuti ndani amene ali ndi tsogolo labwino, anthu amene amakhulupilila Mulungu kapena amene sam’khulupilila? [Yembekezani ayankhe.] M’Baibulo muli lonjezo locokela kwa Mulungu limene limapatsa anthu ambili ciyembekezo. [Ŵelengani Salimo 37:10, 11.] Magazini iyi ikufotokoza zifukwa zinai zotithandiza kudziŵa kuti Mulungu aliko.”