Maulaliki Acitsanzo
Kuyambitsa Maphunzilo a Baibulo pa Ciŵelu Coyamba mu March
“Tikucezela anzathu mwacidule kuwauza za mwambo umene udzakhalako pa April 14. Tsiku limeneli tidzakumbukila imfa ya Yesu. Ena adzakumbukila cocitika cimeneci cifukwa cakuti amaona imfa yake kukhala yofunika. Koma ena sadziŵa kufunika kwa imfa ya Yesu. Kodi muganiza kuti inu ndi ine tingapindule ndi imfa yake?” Yembekezani ayankhe. Muonetseni kucikuto ca kumapeto kwa Nsanja ya Mlonda ya March 1, ndi kukambitsilana naye nkhani ili pansi pa funso loyamba ndipo ŵelengani naye lemba limodzi kapena aŵili pa malembawo. Kenako m’gaŵileni magazini ndi kupangana naye kuti mukabwelenso kudzakambitsilana funso lotsatila.
Nsanja ya Mlonda March 1
“Anthu ambili amadzifunsa cifukwa cake Mulungu sacitapo kanthu kuthetsa kupanda cilungamo ndi mavuto m’dzikoli. Kodi muganiza kuti cingakhale cifukwa cakuti Mulungu sasamala za ife kapena kuti iye amangofuna kuti tizivutika? [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno ŵelengani Yohane 3:16.] Ngakhale kuti ambili amalidziŵa pamtima vesili loonetsa kuti Mulungu amasamala, io sadziŵa mmene imfa ya mwana wake ingawapindulitsile. Magazini iyi ifotokoza mmene imfa ya Yesu idzathandizila kuti kupanda cilungamo ndi mavuto zithe padziko.”
Galamukani! March
“Tafika pano kuti tikambitsilane mwacidule za vesi ili la m’Baibulo limene anthu ambili amalimva molakwa. [Ŵelengani Genesis 1:1.] Ena amakhulupilila zimene taŵelenga kuti dziko linacita kulengedwa koma ena amakana. Kaya inu muganiza bwanji? [Yembekezani ayankhe.] Ambili zimawavuta kukhulupilila kuti zinthu zinacita kulengedwa cifukwa abusa acipembedzo amaphunzitsa zosiyana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa. Magazini iyi ifotokoza mfundo za m’Baibulo zomveka ndi zodalilika za mmene cilengedwe cinayambila.”