LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • km 6/14 masa. 5-6
  • Mmene Tingathandizile Anthu Amene Amavutika Kuŵelenga

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mmene Tingathandizile Anthu Amene Amavutika Kuŵelenga
  • Utimiki Wathu wa Ufumu—2014
  • Nkhani Zofanana
  • Mmene Tingatsogozele Phunzilo la Baibo Lotsogolela Munthu ku Ubatizo—Gawo 1
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2020
  • Zimene Mungacite Kuti Muzipindula Kwambili Poŵelenga Baibo
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Mmene Tingatsogozele Phunzilo la Baibo Lotsogolela Munthu ku Ubatizo—Gawo 2
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2020
  • Monga Mpingo, Thandizani Maphunzilo a Baibo Kupita Patsogolo Kuti Akabatizike
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2021
Onaninso Zina
Utimiki Wathu wa Ufumu—2014
km 6/14 masa. 5-6

Mmene Tingathandizile Anthu Amene Amavutika Kuŵelenga

1. Kuphunzila Baibulo ndi anthu amene amavutika kuŵelenga kuli ndi vuto lanji?

1 Anthu amene amavutika kuŵelenga angakhale ndi cidwi ndi zinthu za kuuzimu, koma angamacite mantha akaona Baibulo ndi mabuku ena. Anthu otelo kuwagaŵila buku la Zimene Baibulo Imaphunzitsa paciyambi kungakhale kosathandiza kwenikweni. Conco, anthu otelo tingawathandize bwanji mwa kuuzimu? Tinafunsa ofalitsa ozoloŵelana kwambili ndi nchito imeneyi a m’maiko osiyanasiyana oposa 20, kuti afotokoze zimene amacita. Iwo anapeleka malingalilo otsatila.

2. Ndi zofalitsa ziti zimene tingagwilitsile nchito pothandiza munthu amene amavutika kuŵelenga?

2 Ngati wophunzila Baibulo amadziŵako pang’ono kapena sadziŵa n’komwe kuŵelenga, mungayambe ndi kabuku kakuti, Mvetselani kwa Mulungu kapena kakuti Mvetselani kwa Mulungu kuti Mukhale ndi Moyo Wamuyaya. M’bale wina amene ndi mpainiya ku United States, amaonetsa tumabuku tonse tuŵili kwa munthu amene akumulalikila kuti asankhepo kamene angakonde. Ofesi ya nthambi ku Kenya inanena kuti zida zimenezi zakhala zothandiza kwambili kumeneko cifukwa mu Africa, anthu mwamwambo amaphunzitsidwa mwa kungomvetsela nthano m’malo mwa kukambilana mafunso ndi mayankho. Ngakhale kuti munthu wophunzila amavomela mosavuta kuŵelenga ndi kukambilana mwa mafunso ndi mayankho, munthu amene sanaphunzile kwambili samakhala womasuka ndi njila imeneyi. Ngati wophunzila Baibulo amakwanitsako kuŵelenga, ofalitsa ambili amakonda kuyamba ndi tumabuku utu: Uthenga Wabwino Wocokela kwa Mulungu!, Naimwe Mungakhale Mnzake wa Mulungu!, kapena buku lakuti Buku langa la Nkhani za m’Baibo.

3. Ndi mfundo ziti zimene zingatithandize kuti ticite bwino pophunzitsa anthu amene sadziŵa kuŵelenga?

3 Ayamikileni: Anthu amene sadziŵa kuŵelenga amakhala a manyazi ndipo ambili amadziona ngati osafunika. Nthawi zambili cinthu coyamba cimene tifunika kucita ndi kuwathandiza kuti akhale omasuka tisanayambe kuwaphunzitsa coonadi. Anthu ambili amene sadziŵa kuŵelenga amakhala anzelu ndipo amatha kuphunzila. Tiyenela kuwalemekeza kwambili ndi kuwaona kukhala ofunika. (1 Pet. 3:15) Iwo adzalimbikitsidwa kwambili kupitilizabe kuphunzila ngati aona kuti kuyesayesa kwao n’kothandiza ndipo akupitilizabe kukula mwa kuuzimu. Conco tiyeni tiziwayamikila kwambili.

Anthu amene sadziŵa kuŵelenga amakhala amanyazi ndipo amadziona ngati osafunika. Nthawi zambili cinthu coyamba cimene tifunika kucita ndico kuwathandiza kuti akhale omasuka tisanayambe kuwaphunzitsa coonadi.

4. Tingawathandize bwanji kukonzekela phunzilo anthu amene sadziŵa bwinobwino kuŵelenga?

4 Ngakhale kuti wophunzila sadziŵa bwinobwino kuŵelenga, m’limbikitseni kuti azikonzekela phunzilo. Ofalitsa ena ku South Africa amalimbikitsa maphunzilo ao kuti azipempha wa wacibale wao kapena mnzao amene angawelenge bwino kuti awathandize. Wofalitsa wina ku Britain amalimbikitsa amene amaphunzila nao kukonzekela mwa kuwalola kugwilitsila nchito buku lake pa ndime zingapo pocita phunzilo n’colinga cakuti aone mmene zimakhalila zopepuka kupeza mayankho ngati io alemba mzela kunsi kwa mayankho. M’bale wina ku India amalimbikitsa amene aphunzila nao Baibulo kuti azionelatu zithunzi za m’phunzilo lotsatila ndi kusinkhasinkhapo mozama.

5. Tingaonetse bwanji kuleza mtima tikamatsogoza phunzilo?

5 Khalani Oleza Mtima: Mosasamala kanthu za cofalitsa cimene museŵenzetsa, gogomezelani mfundo zazikulu ndipo thandizani wophunzila kumvetsa bwino zimenezi. Kukambilana kwa mphindi 10 kapena 15 kungakhale kothandiza ngati mwangoyamba kumene phunzilo. Pa phunzilo lililonse musaziphunzila zinthu zoculuka, m’malo mwake muzingophunzila ndime zocepa cabe. Ngati wophunzila amaŵelenga pang’onopang’ono, khalani woleza mtima. N’kutheka kuti pamene cikondi cake pa Yehova cikula, adzalimbikitsidwa kukulitsa luso lake la kuŵelenga. Kuti wophunzilayo acite zimenezo, cimakhala bwino kumuitanila ku misonkhano mukangoyamba kuphunzila naye.

6. Tingathandize bwanji anthu kuti aphunzile kuŵelenga?

6 Ophunzila Baibulo akaphunzila kuŵelenga, amapita patsogolo mwamsanga mwakuuzimu. (Sal. 1:1-3) Ofalitsa ambili athandiza maphunzilo ao, mwa kugwilitsila nchito buku la Dzipelekeni pa Kuŵelenga ndi Kulemba. Buku limeneli amaliphunzila kwa mphindi zocepa akamaliza phunzilo lililonse. Ngati wophunzilayo akudziona kuti sangakwanitse, mwina mungam’limbikitse mwa kumuonetsa zinthu zina zimene anakwanitsa kuphunzila. Mutsimikizileni kuti Yehova adzadalitsa khama lake, ndipo mulimbikitseni kuti azipemphela kwa Yehova kuti amuthandize. (Miy. 16:3; 1 Yoh. 5:14, 15) Ofalitsa ena ku Britain amalimbikitsa maphunzilo ao kukhala ndi zolinga zoyenela zimene zingawathandize kupita patsogolo. Mwina kuphunzila zilembo za alifabeti coyamba, ndiyeno kupeza ndi kuŵelenga malemba osankhidwa, ndipo comalizila kuŵelenga zofalitsa zofotokoza Baibulo zosavuta. Kuthandiza anthu kuti adziŵe kuŵelenga, nthawi zambili kumafuna kuwalimbikitsa kuti akhale ndi cifuno coŵelenga osati cabe kuwaphunzitsa kuŵelenga.

7. N’cifukwa ciani sitifunika kuleka kuuza coonadi anthu amene amavutika kuŵelenga?

7 Yehova saona kuti anthu amene sanaphunzile kwambili ndi otsika. (Yobu 34:19) Iye amasanthula mtima wa munthu aliyense. (1 Mbiri 28:9) Conco musaleke kuwauza coonadi anthu amene amavutika kuŵelenga. Muli ndi zofalitsa zabwino kwambili zimene mungayambe nazo powathandiza. Pakapita nthawi, mungasinthe phunzilo lanu n’kuyamba kuphunzila m’buku la Zimene Baibo Imaphunzitsa ndipo mungawathandize kumvetsa bwino Malemba.

Ngati mwininyumba sadziŵa kuŵelenga, yesani izi:

  • Coyamba gwilitsilani nchito tumabuku utu, Mvetselani kwa Mulungu, kapena Mvetselani kwa Mulungu kuti Mukhale ndi Moyo Wamuyaya kapena mungagwilitsile nchito zofalitsa zina zoyenelela.

  • Mpatseni ulemu ndipo muyamikileni kwambili.

  • Muzikambilana mwacidule ndipo musaziphunzila zinthu zoculuka.

  • M’thandizeni kunola luso loŵelenga.

Akamaonetsa kukonda kwambili coonadi ndi kukhala wofunitsitsa kuphunzila zambili, mungasamutsile phunzilo lanu m’buku la Zimene Baibo Imaphunzitsa.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani