Maulaliki Acitsanzo
Kuyambitsa Maphunzilo a Baibulo pa Ciŵelu Coyamba mu September
“Kodi muganiza kuti Mulungu amaona bwanji mapemphelo athu? Kodi muganiza kuti amawaona kuti ndi ofunika kapena amangowavomeleza?” Yembekezelani ayankhe. Muonetseni nkhani ili pa cikuto cothela ca Nsanja ya Mlonda ya July-August ndipo kambitsilanani mfundo zimene zili pa funso loyamba ndi lemba limodzi losagwidwa mau. Kenako m’gaŵileni magazini ndi kupangana naye kuti mudzakambitsilane funso lotsatila.
Nsanja ya Mlonda July–August
“Popeza Mulungu ndi Wamphamvuyonse, kodi muganiza kuti ayenela kuimbidwa mlandu cifukwa ca zinthu zoipa zonse zimene zicitika padziko? [Yembekezelani ayankhe. Ndiyeno ŵelengani Yakobo 1:13.] Magazini iyi ifotokoza cifukwa cake zinthu zoipa zimacitika ndiponso zimene Mulungu adzacita pothetsa zinthu zoipa ndi kuvutika.”
Galamukani! September
“Anthu ambili amaona kuti amapatsidwa nchito zambili ndi abwana ao ndipo amaona kuti palibe cimene angacite kuti athetse zimenezi. Akatswili amanena kuti kuculuka kwa nchito kungacititse munthu kumakhala wotopa nthawi zonse, zimene zingayambitse matenda ena ndi kulephela kuganiza bwino. Kodi muganiza kuti n’ciani cimene cingathandize munthu kukhala ndi umoyo wosalila zambili? [Yembekezani yankho.] Vesi la m’Baibulo ili lingathandize munthu kuganizilapo mwakuya pa nkhaniyi. [Ŵelengani Mlaliki 4:6.] Magazini iyi ifotokoza njila zinai zimene zingatithandize kuti ticepetseko zocita zathu ndi kuti tisamakhale wotopa nthawi zonse.”