Maulaliki Acitsanzo
Kuyambitsa Maphunzilo a Baibo pa Ciŵelu Coyamba mu October
“Tikuceza mwacidule ndi maneba athu lelo. Ambili amene talankhula nao akamba kuti vuto losautsa kwambili limene akumanapo nalo ndi imfa ya wokondedwa wao. Kodi inu muona bwanji? [Yembekezani yankho.] Zimene zili m’magazini iye ndi zolimbikitsa kwambili.” Muonetseni nkhani ili kucikhuto cothela ca Nsanja ya Mlonda ya October 1. Ndiyeno kambilanani naye ndime yoyamba ndi lemba lake losagwidwa mau. Kenako, m’gaŵileni magazini ndi kupangana naye kuti mukabwelenso kudzakambilana funso lotsatila.
Nsanja ya Mlonda October 1
“Tikuceza ndi anthu kukambilana nao za kufunika koŵelenga Baibo. Tidziŵa kuti anthu ena amacita cidwi ndi zimene Baibo limanena koma ena ai. Nanga bwanji inuyo? [Yembekezani yankho.] Baibo limanena mau awa mosapita m’mbali. [Ŵelengani 1 Atesalonika 2:13.] Ndidziŵa kuti mudzavomeleza kuti ngati n’zoona kuti Baibo ndi buku locokela kwa Mulungu, ndiye kuti tifunikila kuiŵelenga. Mwacidule magazini iyi ifotokoza zimene Baibo imanena ndiponso cifukwa cake iyenela kuticititsa cidwi.”
Galamukani! October
“Kodi mungakambepo bwanji pa funso ili: Kodi n’zotheka kukhala wokhutila ngati uli ndi katundu wocepa? [Yembekezani yankho.] Onani zimene Baibo imakamba. [Ŵelengani 1 Timoteyo 6:8.] Magazini iyi ionetsa maganizo oyenela amene tiyenela kukhala nao pankhani ya katundu ndipo ifotokozanso zinthu zofunika zitatu zimene ndalama ingagule.”