Gwilitsilani Nchito Webusaiti ya jw.org mu Utumiki
Webusaiti yathu ndi cida cothandiza kwambili pa nchito yofalitsa uthenga wabwino mpaka “kumalekezelo a dziko lapansi.” (Mac. 1:8) Anthu ambili sadziŵa kuti kuli Webusaiti ya jw.org. Iwo amadziŵa za Webusaiti imeneyi ngati ife tawauza.
Woyang’anila woyendela wina anaika pa foni yake kavidiyo ka pa jw.org kamutu wakuti N’cifukwa Ciani Tiyenela Kuphunzila Baibulo?, ndipo amaonetsa anthu kavidiyo kameneka akapeza mpata. Mwacitsanzo, akakhala mu ulaliki wa khomo ndi khomo, iye amakamba kuti: “Ndikucezela anthu mwacidule kuti ndiwathandize kupeza mayankho a mafunso atatu ofunika awa: N’cifukwa ciani padzikoli pali mavuto ambili? Kodi Mulungu adzawathetsa bwanji? Nanga n’ciani cingatithandize kupilila mavutowa? Kavidiyo kakafupi kameneka kakuyankha mafunso amenewa.” Kenako, woyang’anila woyendelayo amaonetsa kavidiyo kameneko kwa mwininyumba. Ndiyeno amaona ngati mwininyumbayo akusangalala ndi zimene akuonela kapena ai. Kavidiyo kameneka ndi kokopa cidwi kwambili cakuti anthu akangoyamba kukaonelela, amafuna mpaka akamalize. Kenako woyang’anila woyendelayo amauza mwininyumbayo kuti: “Monga mmene mwamvela, mungathe kupempha phunzilo la Baibulo pa Intaneti. Popeza ine ndafika kale pa khomo lanu, ndingakuonetseni mwacidule mmene timaphunzilila.” Mwininyumba akavomela, iye amamusonyeza mmene timaphunzilila Baibulo pogwilitsila nchito kabuku ka Uthenga Wabwino. Ngati mwininyumba ndi wotangwanika, iye amapangana naye kuti adzamusonyeze nthawi ina. Woyang’anila woyendelayo amacitanso cimodzimodzi akapita kokapuma. Iye amayambitsa nkhani yodzutsa cidwi kwa munthu amene wakhala naye pafupi. Kodi inuyo mumaigwilitsila nchito Webusaiti ya jw.org mu utumiki?