LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • km 12/14 tsa. 7
  • Nyimbo Zatsopano Zogwilitsila Nchito Polambila

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Nyimbo Zatsopano Zogwilitsila Nchito Polambila
  • Utimiki Wathu wa Ufumu—2014
  • Nkhani Zofanana
  • Muziimba Mosangalala Nyimbo Zotamanda Yehova
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2018
  • Mfundo Yothandiza pa Kuŵelenga Kwanu
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
  • Nyimbo za Ufumu Zimathandiza Kukhala Wolimba Mtima
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano —2017
  • Nyimbo Zimene Zimatiyandikizitsa kwa Mulungu
    Mmene Zopeleka Zanu Zimagwilila Nchito
Onaninso Zina
Utimiki Wathu wa Ufumu—2014
km 12/14 tsa. 7

Nyimbo Zatsopano Zogwilitsila Nchito Polambila

1 Pa msonkhano wapacaka wa Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania umene unacitika pa October 4, 2014, panalengezedwa za kukonzedwanso kwa buku lathu la nyimbo. Kunena zoona, cimeneci cinali cilengezo cokondweletsa kwambili! Onse amene anapezekapo anakumbutsidwa za kufunika kwa nyimbo zathu za Ufumu pa kulambila kwathu.—Sal. 96:2.

2 Mwina mungafunse kuti, ‘N’cifukwa ciani buku la nyimbo linafunika kukonzedwanso?’ Pali zifukwa zingapo. Coyamba, kamvedwe kathu ka Malemba kakupitilizabe kusintha, ndipo ici cacititsa kuti mau a nyimbo zathu akhudzidwe. (Miy. 4:18) Cifukwa cina ndi ici: Mau ambili amene anali kugwilitsidwa nchito m’buku lathu la nyimbo anacotsedwa mu Baibulo la Dziko Latsopano lakale la Cingelezi. Conco mau a m’nyimbo zimenezi asinthidwa kuti agwilizane ndi mau amene ali mu Baibulo lokonzedwanso la Cingelezi. Popeza kuti panafunika kucitika nchito yaikulu kuti mau a m’nyimbo akonzedwe bwino, anaona kuti m’pofunika kuonjezela nyimbo zocepa zatsopano m’buku lathu.

3 Kodi tidzayembekezela mpaka pamene buku la nyimbo latsopano litasindikizidwa kuti tiyambe kugwilitsila nchito nyimbo zatsopano? Ai. Ndife okondwa kukudziŵitsani kuti m’miyezi ikubwelayi, zina mwa nyimbo zimenezi zidzaikidwa pa Webusaiti yathu ya jw.org. Ndipo nyimbo zimenezi zikadzatulutsidwa, zizidzaikidwa ku mapeto a ndandanda ya Msonkhano wa Nchito ndipo zizidzalembedwa kuti “nyimbo yatsopano.”

4 Mmene Tingaphunzilile Nyimbo Zatsopano: Kuphunzila nyimbo zatsopano kungakhale kovuta. Monga wamasalimo, ifenso tifunika kuimba nyimbo pa misonkhano ya mpingo ‘osati kukhala cete.’ (Sal. 30:12) Kuti muphunzile nyimbo yatsopano, tsatilani njila zosavuta izi:

  • Mvetselani mobwelezabweleza nyimbo yamalimba, imene idzaikidwa pa Webusaiti yathu. Mukamamvetsela kwambili nyimboyi, kudzakhala kosavuta kuikumbukila.

  • Lowezani mau a nyimbo imeneyi ndipo yesani kumaiimba pamtima.

  • Imbani nyimbo imeneyi motsagana ndi mau ake. Citani zimenezi mpaka mutaidziŵa bwino nyimboyi.

  • Yesezani nyimbozi pa nthawi ya Kulambila kwa pa Banja mpaka mutaona kuti banja lanu lazidziŵa bwino.

5 M’miyezi ya kutsogolo, ngati nyimbo yatsopano ndi imene idzaimbidwa pomaliza Msonkhano wa Nchito, coyamba mpingo uzimvetsela kamodzi nyimboyo. Pambuyo pake, gulu lizidzaimba pamodzi motsagana ndi nyimbo zamalimba, monga mmene timacitila ndi nyimbo zonse.

6 Mukaganizila nkhani imeneyi, mudzaona kuti kuimba nyimbo pa misonkhano yathu kumatipatsa cimwemwe cifukwa cotamanda Yehova mogwilizana. Conco pamene nyimbo iyamba, tisamakhale ndi cizoloŵezi cokonda kutuluka pabwalo popanda zifukwa.

7 Pali njila inanso imene tingaonetsele ciyamikilo cathu pa nyimbo zopatulika zimenezi. Pa misonkhano yadela ndi yacigawo, nyimbo zamalimba zimaimbidwa misonkhano isanayambe m’cigawo ciliconse. Kawili pa caka, abale ndi alongo odzipeleka ocokela m’maiko osiyanasiyana, amagwilitsila nchito ndalama zao kupita ku Patterson, mu mzinda wa New York, n’colinga coti akakonze nyimbo zosangalatsa zoti tizizigwilitsila nchito pa kulambila kwathu. Conco, pamene cheyamani watipempha kuti tikhale pansi ndi kumvetsela ku nyimbo zamalimba zimene gulu la oimba lakonza, tiyenela kucita zimenezo. Kucita zimenezi kudzatithandiza kukonzekeletsa mitima yathu pa nkhani zimene zidzatsatilapo.—Ezara 7:10.

8 Pa mapeto a msonkhano wa lelo, tidzaimba nyimbo yatsopano ya mutu wakuti: “Ufumu Ukulamulila, Ndipo Ubwele.” Nyimbo iyi ndi imene inaimbidwa pa msonkhano wapacaka, ndipo ionetsa kuti papita zaka 100 kucokela pamene Ufumu unakhazikitsidwa.

9 Mosakaikila, nyimbo zatsopano zimenezi ndi zinthu “zabwino” zocokela kwa Yehova. (Mat. 12:35a) Conco cikhale colinga cathu kuphunzila nyimbo zatsopano zimenezi ndi kuziimba kucokela pansi pa mtima wathu kuti tipeleke citamando coyenelela ndi ulemu kwa Mulungu wathu!—Sal. 147:1.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani