UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Muziimba Mosangalala Nyimbo Zotamanda Yehova
Paulo na Sila anaimba nyimbo zotamanda Yehova pamene anali m’ndende. (Mac. 16:25) Mosakayikila kuimba kunawathandiza kuti apilile. Nanga bwanji ise masiku ano? Nyimbo zimene timaimba polambila, komanso nyimbo zathu zina, zimatitsitsimula na kutithandiza kukhalabe okhulupilika pokumana na mayeselo. Koposa zonse, nyimbozo zimatamanda Yehova. (Sal. 28:7) Timalimbikitsidwa kuti tiziikako pa mtima mawu a nyimbo zina. Kodi munayesapo kucita zimenezi? Pa kulambila kwa pabanja tikhoza kumaimbako nyimbo kuti tidziŵe mawu ake.
TAMBITSANI VIDIYO YAKUTI ANA ATAMANDA YEHOVA M’NYIMBO
, PAMBUYO PAKE, YANKHANI MAFUNSO OTSATILA:
Kodi kuimba nyimbo za Ufumu kumatikhudza bwanji?
Kodi Dipatimenti ya Audio/Video imakonzekela bwanji nyimbo zokajambula?
Kodi makolo na ana awo amakonzekela bwanji nyimbo zokajambula?
Kodi mumakonda nyimbo ziti? Nanga n’cifukwa ciani mumazikonda?