LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w23 November tsa. 32
  • Mfundo Yothandiza pa Kuŵelenga Kwanu

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mfundo Yothandiza pa Kuŵelenga Kwanu
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
  • Nkhani Zofanana
  • Muziimba Mosangalala Nyimbo Zotamanda Yehova
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2018
  • Nyimbo Zatsopano Zogwilitsila Nchito Polambila
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2014
  • Nyimbo Zimene Zimatiyandikizitsa kwa Mulungu
    Mmene Zopeleka Zanu Zimagwilila Nchito
  • Nyimbo za Ufumu Zimathandiza Kukhala Wolimba Mtima
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano —2017
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
w23 November tsa. 32

Mfundo Yothandiza pa Kuŵelenga Kwanu

Loŵezani pa mtima “Nyimbo Zauzimu”

Mlongo Lorraine wa ku America anati “Masiku ena ngati napsinjika maganizo kapena kudziona kukhala wacabe-cabe, Yehova amanilimbikitsa kupitila m’nyimbo za pa JW Broadcasting®.”

Kungoyambila kale-kale, “nyimbo zauzimu” ­zakhala mbali ya kulambila kwa Cikhristu. (Akol. 3:​16) Ngati munaloŵeza nyimbozi pa ­mtima, zingakulimbikitseni ngakhale pamene mulibe buku la nyimbo kapena cipangizo camakono. Yesani kucita zotsatilazi kuti mukwanitse kuloŵeza nyimbozi pa mtima.

● Ŵelengani mofatsa mawu a m’nyimbo kuti mumvetse tanthauzo lake. N’capafupi kukumbukila cinthu cimene timamvetsa tanthauzo lake. Mawu a nyimbo zathu zonse kuphatikizapo nyimbo zopekedwa koyamba komanso nyimbo za ana, zilipo pa jw.org. Loŵani pa danga lakuti Laibulale kenako dinizani pa Nyimbo.

● Lembani pa pepala mawu a m’nyimbo. ­Kucita zimenezi kudzakuthandizani kuloŵeza mawuwo pa mtima.​—Deut. 17:18.

● Muziyeseza mokweza mawu. Muziŵelenga kapena kuimba nyimbo mobweleza-bweleza.

● Yesani ngati mungathe kukumbukila zimene mwaloŵeza. Yesezani kuimba nyimbo yonse popanda kuona m’buku la nyimbo kapena mawu ake, kenako onani mmene mwacitila.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani