Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Thandizani Ophunzila Kukhala ndi Cizolowezi Cabwino Cophunzila Baibulo
Cifukwa Cake Kuli Kofunika: Kuti ophunzila Baibulo akule mwa kuuzimu, afunika kuphunzila mfundo zozama osati cabe mfundo zoyambilila za m’Mau a Mulungu. (Aheb. 5:12–6:1) Kuphunzila kumafuna khama. Kumaphatikizapo kugwilizanitsa zimene tikuphunzila ndi zimene tikudziŵa, komanso kuona mmene tingazigwilitsile nchito. (Miy. 2:1-6) Ngati ophunzila Baibulo amafufuza zinthu paokha, amaphunzila kuyankha mafunso a m’Baibulo pogwilitsila nchito zofalitsa zathu. Kuyesetsa kwao kugwilitsila nchito zimene akuphunzila, kudzawathandiza kulimbana ndi ziyeso zimene angakumane nazo monga Akristu.—Luka 6: 47, 48.
Yesani Kucita Izi Mwezi Uno:
Mukatsiliza kuphunzila nkhani iliyonse kapena kamutu kalikonse, funsani wophunzila Baibulo wanu kuti afotokoze mwacidule zimene waphunzila. Ngati mulibe phunzilo, yesezani kufotokoza mwacidule zimene inu mwaŵelenga m’Baibulo kapena ndime ya mu Nsanja ya Mlonda kuti muone ngati mwamvetsa zimene mwaŵelenga.