CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | EZARA 6-10
Yehova Amafuna Anthu Omutumikila Mocita Kufuna Okha
Ezara anakonza zobwelela ku Yerusalemu
7:6, 22; 8:26, 27
Ezara aloledwa ndi Mfumu Aritasasta kubwelela ku Yerusalemu kuti akalimbikitsa anthu kuti azilambila Yehova
Mfumu ipatsa Ezara “zopempha zake zonse” zokamangila nyumba ya Yehova—golide, siliva, tiligu, vinyo, mafuta, ndi mcele, ndipo zonse zinakwana $100,000,000, madola a ku America, malinga ndi ndalama za masiku ano
Ezara anakhulupilila kuti Yehova adzateteza atumiki Ake
7:13; 8:21-23
Ulendo wobwelela ku Yerusalemu unali wovuta
Ulendo unali makilomita pafupifupi 1,600 ndipo njilayo inali kudutsa m’madela oopsa
Ulendowo unatenga miyezi inai
Aisiraeli amene anabwelela anafunika kukhala ndi cikhulupililo colimba, acangu pa kulambila koona, ndi olimba mtima
EZARA ANANYAMULA . . .
Golide ndi siliva wolema kuposa matalente 750, monga kulema kwa njovu zazikulu pafupifupi zitatu
ZOPINGA ZIMENE ANAKUMANA NAZO POBWELELA . . .
Magulu acifwamba, cipululu coopsa, nyama zoopsa