UMOYO WATHU WACIKHIRISTU
Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Limbikitsani Anthu Acidwi Kupezeka pa Misonkhano
CIFUKWA CAKE KULI KOFUNIKA: Misonkhano imatipatsa mwayi ‘woimba’ ndi ‘kutamanda’ Yehova. (Sal. 149:1) Pa misonkhano, timaphunzitsidwa kucita cifunilo ca Mulungu. (Sal. 143:10) Anthu acidwi ndiponso amene timaphunzila nawo Baibulo amapita patsogolo mwamsanga akayamba kupezeka pa misonkhano.
MMENE TINGACITILE:
Itanilani munthu wacidwi ku misonkhano mwamsanga. Musayembekezele kuti mukhazikitse phunzilo la Baibulo.—Chiv. 22:17
Fotokozelani munthu wacidwi zimene zimacitika ku misonkhano ndi zimene tidzaphunzila pa msonkhano wotsatila. Mungaseŵenzetse zinthu zotsatilazi: Kapepala koitanila ku misonkhano, vidiyo yakuti N’ciani Cimacitika ku Nyumba ya Ufumu?, ndi kabuku ka Cifunilo ca Yehova, phunzilo 5 ndi 7
M’thandizeni. Kodi munthuyo afunika kukamutenga kapena kumuthandiza kusankha zovala zoyenelela? Khalani naye pafupi pa misonkhano, ndipo muzionela pamodzi mabuku amene mukuseŵenzetsa. Mudziŵikitseni kwa ena