LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb22 January tsa. 9
  • Thandizani Maphunzilo Anu a Baibo Kumapezeka pa Misonkhano

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Thandizani Maphunzilo Anu a Baibo Kumapezeka pa Misonkhano
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2022
  • Nkhani Zofanana
  • Kodi Misonkhano ya Mboni za Yehova Ingakupindulileni Motani?
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Thandizani Maphunzilo a Baibo Kukhala pa Ubale Wolimba na Yehova
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2022
  • Thandizani Maphunzilo Anu a Baibo Kupewa Mayanjano Oipa
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2022
  • Thandizani Maphunzilo a Baibo Kuleka Makhalidwe Odetsa
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2022
Onaninso Zina
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2022
mwb22 January tsa. 9

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | WONJEZELANI CIMWEMWE CANU MU ULALIKI

Thandizani Maphunzilo Anu a Baibo Kumapezeka pa Misonkhano

Misonkhano ya mpingo ni mbali yofunika kwambili pa kulambila koona. (Sal. 22:22) Onse amene amasonkhana kuti alambile Yehova amapeza cimwemwe na madalitso. (Sal. 65:4) Nthawi zambili ophunzila Baibo amapita patsogolo mwamsanga akamapezeka pamisonkhano nthawi zonse.

Kodi mungaathandize bwanji maphunzilo anu a Baibo kuti azipezeka kumisonkhano? Pitilizani kuwaitanila kumisonkhano. Aonetseni vidiyo yakuti N’ciani Cimacitika ku Nyumba ya Ufumu? Afotokozeleni ubwino wa misonkhano. (lff phunzilo 10) Komanso, mungawafotokozeleko mfundo inayake imene munaphunzila pamsonkhano, kapena mungawauzeko zimene mudzaphunzila pamsonkhano wotsatila. Apatseni zofalitsa zimene zidzagwilitsidwa nchito pamsonkhano. Ndiponso athandizeni pa zinthu zina zofunikila. Mwina afunika thandizo la mayendedwe. Ophunzila anu akadzapezeka pamisonkhano kwa nthawi yoyamba, mudzaona kuti khama lanu silinapite pacabe.—1 Akor. 14:24, 25.

ONELELANI VIDIYO YAKUTI THANDIZANI MAPHUNZILO ANU A BAIBO KUMAPEZEKA PA MISONKHANO, KENAKO YANKHANI MAFUNSO AWA:

  • Cithunzi coonetsa zocitika za mu vidiyo yakuti “Thandizani Maphunzilo Anu a Baibo Kumapezeka pa Misonkhano.” Neeta akuitanila Rose ku msonkhano wa mpingo.

    Kodi Neeta anaseŵenzetsa mpata wotani poitanila Rose kumsonkhano wa mpingo?

  • Cithunzi coonetsa zocitika za mu vidiyo yakuti “Thandizani Maphunzilo Anu a Baibo Kumapezeka pa Misonkhano.” Neeta akumwetulila pamene Rose wabwela ku msonkhano wa mpingo n’kukhala naye pafupi.

    N’cifukwa ciani timakondwela wophunzila Baibo akapezeka kumisonkhano?

  • Cithunzi coonetsa zocitika za mu vidiyo yakuti “Thandizani Maphunzilo Anu a Baibo Kumapezeka pa Misonkhano.” Alongo mwacikondi akum’patsa moni Rose pambuyo pa msonkhano wa mpingo.

    “Zoonadi Mulungu Ali Pakati Panu”

    N’ciani cinacitika nthawi yoyamba pamene Rose anapezeka kumisonkhano?

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani