Alalikila khomo na khomo ku Italy
Maulaliki a Citsanzo
NSANJA YA MLONDA
Funso: Kodi n’colinga ca Mulungu kuti tizifa?
Lemba: Chiv. 21:4
Cogaŵila: Nsanja ya Mlonda iyi ifotokoza zimene Baibo imakamba pa nkhani ya moyo na imfa.
PHUNZITSANI COONADI
Funso: N’cifukwa ciani padzikoli pali mavuto ambili?
Lemba: 1 Yoh. 5:19
Coonadi: Satana Mdyelekezi ndiye amalamulila dziko.
KODI PHUNZILO LA BAIBO LIMACITIKA BWANJI?
Cogaŵila: Mboni za Yehova zili na pulogilamu yophunzitsa anthu Baibo kwaulele imene imayankha mafunso monga akuti: N’cifukwa ciani padziko pali mavuto ambili? Ningacite ciani kuti banja langa likhale lacimwemwe? Kavidiyo kacidule aka kaonetsa mmene phunzilo la Baibo limacitikila. [M’tambitseni ka vidiyo kakuti Kodi Phunzilo la Baibulo Limacitika Bwanji?] Tingamaseŵenzetse bukuli pokambilana. [Muonetseni cofalitsa cophunzilila Baibo, ndipo ngati n’kotheka muonetseni mmene timacitila.]
KONZANI ULALIKI WANU
Funso:
Lemba:
Cogaŵila: