LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb19 February tsa. 8
  • Pitilizani Kuyembekezela Mopilila

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Pitilizani Kuyembekezela Mopilila
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2019
  • Nkhani Zofanana
  • Musalole Ciliconse Kukumanitsani Mphoto
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2017
  • Khalanibe Pafupi na Gulu la Yehova
    Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova
  • Mafunso Ocokela Kwa Aŵelengi
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2017
  • Yehova Amatithandiza Kupilila Mayeso
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
Onaninso Zina
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2019
mwb19 February tsa. 8

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Pitilizani Kuyembekezela Mopilila

Kodi Ufumu wa Mulungu mwauyembekezela kwa nthawi yaitali bwanji? Kodi mumapilila moleza mtima olo kuti mumakumana na mavuto? (Aroma 8:25) Akhristu ena amazondedwa, kuzunzidwa, kuikidwa m’ndende, ngakhale kuphedwa kumene. Ndipo ena ambili amapilila matenda osacilitsika kapena ukalamba.

N’ciani cingatithandize kuyembekezela mwacidwi olo tikumane na mavuto? Tifunika kulimbitsa cikhulupililo cathu mwa kuŵelenga Baibo na kusinkha-sinkha. Tifunikanso kusumika maganizo athu pa ciyembekezo. (2 Akor. 4:16-18; Aheb. 12:2) Tifunika kupemphela mopembedzela kwa Yehova, na kum’pempha kuti atipatse mphamvu ya mzimu woyela. (Luka 11:10, 13; Aheb. 5:7) Atate wathu wacikondi adzatithandiza ‘kuti tithe kupilila zinthu zonse ndi kukhala oleza mtima ndiponso acimwemwe.’—Akol. 1:11.

TAMBITSANI VIDIYO YAKUTI TIFUNIKA ‘KUTHAMANGA MOPILILA’—KHALANI NA CIDALILO CAKUTI MUDZALANDILA MPHOTO, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AYA:

  • Jamie na mkazi wake ali mu ulaliki

    Ni “zinthu zosayembekezeleka” ziti zimene zingatigwele mu umoyo? (Mlal. 9:11)

  • Jamie ali na stroko, ndipo m’bale Carl akuŵelenga naye malemba

    Kodi pemphelo lingatithandize bwanji tikakumana na mayeselo?

  • Jamie na m’bale Carl akucita ulendo wa ubusa ku banja lina

    Ngati sitikwanitsa kucita zimene kale tinali kucita mu utumiki wa Yehova, n’cifukwa ciani tifunika kulunjika maganizo athu pa zimene tingakwanitse?

  • Jamie akuganizila mmene adzakhalila na thanzi labwino m’Paradaiso

    Yang’ananibe pa mphoto

    N’ciani cimakuthandizani kukhalabe na cidalilo cakuti mudzalandila mphoto?

Mungawathandize bwanji anthu amene akukumana na mavuto pamodzi na a m’banja mwawo?

  • Auzeni mawu olimbikitsa, ndipo pewani kuwayelekezela na ena

  • Khalani m’mvetseli wabwino

  • Muziwapemphelela, ndipo muzipemphela nawo pamodzi

  • Muziwaphikilako cakudya kapena kuwagwililako nchito zina za panyumba

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani