LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb19 June tsa. 7
  • Sankhani Zosangalatsa Mwanzelu

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Sankhani Zosangalatsa Mwanzelu
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2019
  • Nkhani Zofanana
  • Sankhani Zosangalatsa Zovomelezeka kwa Yehova
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Mmene Tingasankhile Zosangalatsa
    Mmene Tingakhalilebe mu Cikondi ca Mulungu
  • Mmene Mungasankhile Zosangulutsa Zabwino
    “Khalanibe m’Cikondi ca Mulungu”
  • Khalani Wodzipeleka kwa Yehova Yekha
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2019
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2019
mwb19 June tsa. 7

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Sankhani Zosangalatsa Mwanzelu

N’cifukwa ciani tifunika kusankha zosangalatsa mwanzelu? Cifukwa pamene tisankha filimu yotamba, nyimbo yomvetsela, webusaiti yoti tiloŵepo, buku loti tiŵelenge, kapena gemu ya pavidiyo kuti tichaye, timakhala tikusankha zinthu zoti zikhale m’maganizo mwathu. Conco, zimene timasankha zimakhudza khalidwe lathu. N’zomvetsa cisoni kuti, zosangalatsa zambili masiku ano n’zodzala na zinthu zimene Yehova amadana nazo. (Sal. 11:5; Agal. 5:19-21) N’cifukwa cake Baibo imatilangiza kuti sitifunika kuleka kuganizila zinthu zolemekeza Yehova.—Afil. 4:8.

TAMBITSANI VIDIYO YAKUTI KODI NIYENELA KUSANKHA ZOSANGALATSA ZABWANJI? PAMBUYO PAKE, YANKHANI MAFUNSO AYA:

  • Maseŵela omenyana a ku Roma

    Kodi maseŵela omenyana a ku Roma wakale afanana bwanji na zosangalatsa zina zamakono?

  • M’bale amene ni mpainiya ali mu ulaliki pamodzi na wacicepele wa mu mpingo mwawo

    Kodi abale na alongo mu mpingo angathandize bwanji acicepele kusankha zosangalatsa mwanzelu?

  • Msilikali

    Kodi lemba la Aroma 12:9 lingatithandize bwanji posankha zosangalatsa?

  • Mboni zacicepele zikuchaya bola

    Ni zosangalatsa zotani zabwino zimene zimacitika m’dela lanu?

ZOSANGALATSA ZIMENE MUCITAPO KANTHU, NA ZIMENE SIMUCITAPO KANTHU

Zosangalatsa zambili masiku ano zimalimbikitsa kungokhala, osacita kanthu. Mafilimu, mabuku, na mapulogilamu a pa TV amaonetsa anthu ena akucita zinthu zoonetsa nzelu zawo, osati zanu. Ngakhale kuti zilipo zina zosangalatsa zabwino zosalila kucitapo kanthu, ambili aona kuti zosangalatsa zofuna kucitapo kanthu zimakhala zopindulitsa kwambili. Mwacitsanzo, ena amakonda kuimba nyimbo pa cipangizo coimbila kapena kudilowing’a zithunzi. Ena amakonda kucita zosangalatsa monga kuchaya bola, kukwela phili, kapena kukaona malo akutali. Kaya tisankhe zosangalatsa zotani, tiyeni tizicita “zonse ku ulemelelo wa Mulungu.” —1 Akor. 10:31.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani