CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 20-21
Yehova Amakwanilitsa Malonjezo Ake Nthawi Zonse
21:1-3, 5-7, 10-12, 14
Yehova anadalitsa Abulahamu na Sara cifukwa ca cikhulupililo cawo, powapatsa mwana wamwamuna. M’kupita kwa nthawi, pokhalabe omvela pokumana na mayeselo, anaonetsa cikhulupililo cawo m’malonjezo a Yehova akutsogolo.
Ngati nikhalabe womvela pokumana na mayeselo, kodi nimaonetsa bwanji kuti nimakhulupilila malonjezo a Yehova akutsogolo? Nanga ningalimbitse bwanji cikhulupililo canga?