UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Khalani Wodzicepetsa Ena Akakutamandani
Nthawi zina, ena angatiyamikile kapena kutitamanda. Izi zingakhale zolimbikitsa ngati zimene anthuwo akamba n’zocokela pansi pa mtima komanso ngati ali na colinga cabwino. (Miy. 15:23; 31:10, 28) Koma tifunika kusamala kuti zimenezo zisatipangitse kudziona wapamwamba, na kuyamba kunyada.
TAMBITSANI VIDIYO YAKUTI KHALANI OKHULUPILIKA MONGA YESU—MUKATAMANDIDWA, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO OTSATILAWA:
Ni zinthu ziti zimene anthu angatitamande nazo?
Kodi abale anam’tamanda bwanji m’bale Seji?
Kodi kumutamanda kwawo kunapitilila bwanji pa mlingo woyenela?
Muphunzilapo ciani mukaona mmene m’bale Seji anawayankhila modzicepetsa?