LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb22 March tsa. 7
  • Thandizani Maphunzilo a Baibo Kuleka Makhalidwe Odetsa

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Thandizani Maphunzilo a Baibo Kuleka Makhalidwe Odetsa
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2022
  • Nkhani Zofanana
  • Thandizani Maphunzilo a Baibo Kukhala pa Ubale Wolimba na Yehova
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2022
  • Landilani Thandizo la Yehova Kupitila M’pemphelo
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
  • Funsani Mafunso
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
  • Afikeni Pamtima Anthu
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
Onaninso Zina
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2022
mwb22 March tsa. 7

CITANI KHAMA PA ULALIKI | WONJEZELANI CIMWEMWE CANU MU ULALIKI

Thandizani Maphunzilo a Baibo Kuleka Makhalidwe Odetsa

Anthu okhawo amene ali na khalidwe loyela ndiwo angakhale pa ubale wabwino na Yehova. (1 Pet. 1:14-16) Ophunzila Baibo akaleka makhalidwe oipa amapindula cifukwa amakhala na banja lacimwemwe, thanzi labwino, ndiponso amapewa kuwononga ndalama.

Afotokozeleni momveka bwino ophunzila Baibo mfundo za Yehova za makhalidwe abwino, cifukwa cake anazikhazikitsa, ndiponso mapindu amene iwo angapeze akamazitsatila. Sumikani maganizo pa kuthandiza ophunzila anu kusintha kaganizidwe kawo. Akasintha kaganizidwe kawo, m’kupita kwa nthawi makhalidwe awo nawonso adzasintha. (Aef. 4:22-24) Atsimikizileni kuti na thandizo la Yehova angakwanitse kuleka khalidwe loipa limene linazika mizu mwa iwo. (Afil. 4:13) Auzeni kuti azipemphela kwa Yehova mocondelela akayamba kulakalaka kucita chimo. Athandizeni kuzindikila zinthu zimene zingawaike pa mayeselo na kuzipewa. Alimbikitseni kucita zinthu zimene zingawathandize, m’malo mocita makhalidwe odetsa. Timakondwela kuona ophunzila Baibo akupanga masinthidwe pa umoyo wawo mothandizidwa na Yehova.

ONELELANI VIDIYO YAKUTI THANDIZANI MAPHUNZILO ANU A BAIBO KULEKA MAKHALIDWE ODETSA, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AWA:

  • Cithunzi coonetsa zocitika za m’vidiyo yakuti “Thandizani Maphunzilo Anu a Baibo Kuleka Makhalidwe Odetsa.” Neeta na Rose akumana na akulu.

    Kodi akulu komanso Neeta anaonetsa bwanji kuti anali na cidalilo cakuti Rose angasinthe?

  • Cithunzi coonetsa zocitika za m’vidiyo yakuti “Thandizani Maphunzilo Anu a Baibo Kuleka Makhalidwe Odetsa.” Neeta akuphunzila na Rose.

    Kodi Neeta anapitiliza bwanji kum’thandiza Rose?

  • Cithunzi coonetsa zocitika za m’vidiyo yakuti “Thandizani Maphunzilo Anu a Baibo Kuleka Makhalidwe Odetsa.” Rose akupempha thandizo kwa Yehova.

    Kodi Rose anacita ciani kuti Yehova am’thandize?

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani