LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb21 November tsa. 15
  • Phunzitsani Maphunzilo Anu a Baibo Kudzidyetsa Okha Mwauzimu

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Phunzitsani Maphunzilo Anu a Baibo Kudzidyetsa Okha Mwauzimu
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
  • Nkhani Zofanana
  • Thandizani Maphunzilo a Baibo Kukhala pa Ubale Wolimba na Yehova
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2022
  • Thandizani Maphunzilo a Baibo Kuleka Makhalidwe Odetsa
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2022
  • Funsani Mafunso
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
  • Afikeni Pamtima Anthu
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
Onaninso Zina
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
mwb21 November tsa. 15

CITANI KHAMA PA ULALIKI | WONJEZELANI CIMWEMWE CANU MU ULALIKI

Phunzitsani Maphunzilo Anu a Baibo Kudzidyetsa Okha Mwauzimu

Kuti ophunzila Baibo athetse njala yawo yauzimu na kupita patsogolo mwauzimu, ayenela kuphunzilanso zinthu zina kuwonjezela pa zimene timawaphunzitsa. (Mat. 5:3; Aheb. 5:12–6:2) Ayenelanso kuphunzila kudzidyetsa okha mwauzimu.

Mukangoyamba kuphunzila Baibo na munthu, muonetseni mmene angakonzekelele phunzilo la Baibo, ndipo m’limbikitseni kucita zimenezo. (mwb18.03 6) M’limbikitseni kuti azipemphela nthawi zonse asanayambe kukonzekela. Athandizeni ophunzila Baibo anu kupeza zida zophunzilila za pazipangizo, ndipo auzeni mmene angaziseŵenzetsele. Afotokozeleni mmene angapezele zofalitsa, mavidiyo, na zinthu zina zatsopano za pa jw.org na JW Broadcasting®. Mwapang’ono-pang’ono, aphunzitseni kuti aziŵelenga Baibo tsiku lililonse, kukonzekela misonkhano ya mpingo, na kudzifufuzila mayankho pa mafunso amene ali nawo. Alimbikitseni kuti azisinkhasinkha pa zimene amaphunzila.

ONELELANI VIDIYO YAKUTI THANDIZANI MAPHUNZILO ANU A BAIBO KUDZIDYETSA OKHA MWAUZIMU, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AWA:

  • Cithunzi coonetsa zocitika za mu vidiyo yakuti “Thandizani Maphunzilo Anu a Baibo Kudzidyetsa Okha Mwauzimu.” Rose akukamba kuti amakumbukila mfundo zimene zinam’fika pamtima.

    Kodi Neeta anam’thandiza bwanji Rose kuona kuti kuphunzila sikutanthauza kudziŵa cabe mayankho?

  • Cithunzi coonetsa zocitika za mu vidiyo yakuti “Thandizani Maphunzilo Anu a Baibo Kudzidyetsa Okha Mwauzimu.” Neeta akuthandiza Rose kupeza yankho pa lemba.

    N’ciani cinathandiza Rose kumvetsa kuti Yehova anacita bwino kuletsa khalidwe laciwelewele?

  • Cithunzi coonetsa zocitika za mu vidiyo yakuti “Thandizani Maphunzilo Anu a Baibo Kudzidyetsa Okha Mwauzimu.” Rose akusinkhasinkha pa lemba atakhala pafupi na cibwenzi cake.

    Thandizani ophunzila anu kudziŵa coonadi komanso mmene ayenela kucigwilitsila nchito

    Kodi Rose anazindikila ciani pa nkhani ya kusinkhasinkha?

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani