CITANI KHAMA PA ULALIKI | WONJEZELANI CIMWEMWE CANU MU ULALIKI
Thandizani Maphunzilo Anu a Baibo Kupewa Mayanjano Oipa
Kuti ophunzila Baibo akhale pa ubwenzi na Yehova, ayenela kusankha mabwenzi abwino. (Sal. 15:1, 4) Mabwenzi abwino adzawalimbikitsa kucita zabwino.—Miy. 13:20; lff phunzilo 48.
Khalani acifundo pothandiza maphunzilo anu a Baibo kupewa mayanjano oipa. Zingakhale kuti zikuwavuta kuleka kugwilizana na mabwenzi a kudziko. Conco, muziwaonetsa cidwi ngakhale masiku amene simuphunzila nawo Baibo. Mungacite izi mwa kuwatumila meseji, foni, kapena kuwacezelako kwakanthawi. Pamene ophunzila Baibo anu akupita patsogolo, mungawaitanileko ku maceza amene anthu a Mulungu amakhala nawo nthawi zina. Mukatelo, adzaona kuti zimene akupeza n’zambili kuposa zimene akutaya. (Maliko 10:29, 30) Inunso mudzapeza cimwemwe poona kuti banja la Yehova likukula.
ONELELANI VIDIYO YAKUTI THANDIZANI MAPHUNZILO ANU A BAIBO KUPEWA MAYANJANO OIPA, KENAKO YANKHANI MAFUNSO AWA:
Kodi mayanjano oipa n’ciani?—1 Akor. 15:33
Kodi Rose anali kuganiza kuti maceza acikhristu amakhala otani?
Kodi Neeta anam’thandiza bwanji Rose kusiya mabwenzi oipa n’kupeza mabwenzi abwino?