CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Mmene Mungakhalile Bwenzi Labwino
Tonthozani na kulimbikitsa bwenzi lanu limene lapsinjika maganizo (1 Sam. 20:1, 2; w19.11 7 ¶18)
Cenjezani bwenzi lanu pakakhala zoopsa (1 Sam. 20:12, 13; w08 2/15 8 ¶7)
Bwenzi lanu likamanenezedwa na ena, muzilikhalila kumbuyo (1 Sam. 20:30-32; w09 10/15 19 ¶11)
Anthu a Yehova ali na mipata yambili yopezela mabwenzi abwino. Kuti mupeze bwenzi, muyenela kukhala waubwenzi. N’ndani amene mungakonde kupalana naye ubwenzi mumpingo?