LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w25 July masa. 20-25
  • Kodi ‘Munaphunzila Cinsinsi’ Cokhala Wokhutila?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi ‘Munaphunzila Cinsinsi’ Cokhala Wokhutila?
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • KULITSANI KHALIDWE LA KUYAMIKILA
  • IKANI MAGANIZO ANU PA ZINTHU ZOFUNIKA NDIPO KHALANIBE WODZICEPETSA
  • MUZISINKHASINKHA ZA CIYEMBEKEZO CANU
  • “ONSE AMENE AMAMUOPA SASOWA KANTHU”
  • Muzivomeleza Kuti Pali Zimene Simudziwa
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • Muzikumbukila Kuti Yehova ni “Mulungu Wamoyo”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
  • Zisankho Zimene Zimaonetsa Kuti Timadalila Yehova
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
  • Kodi Mumacizindikila Coonadi?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
w25 July masa. 20-25

NKHANI YOPHUNZILA 31

NYIMBO 111 Zifukwa Zokhalila Acimwemwe

Kodi ‘Munaphunzila Cinsinsi’ Cokhala Wokhutila?

“Ndaphunzila kukhala wokhutila ndi zimene ndili nazo posatengela mmene zinthu zilili pa moyo wanga.”​—AFIL. 4:11.

ZOFUNIKA KUMVETSETSA

Kuphunzila mmene tingakhalile okhutila pokulitsa khalidwe la kuyamikila, kuika maganizo athu pa zimene Mulungu amafuna ndi kukhala odzicepetsa, komanso kusinkhasinkha za ciyembekezo cathu.

1. Kodi kukhala wokhutila kumatanthauza ciyani? Nanga sikutanthauza ciyani?

KODI ndinu wokhutila ndi zimene muli nazo? Munthu wokhutila amakhala ndi cimwemwe komanso mtendele wa mumtima cifukwa coika maganizo ake pa madalitso amene ali nawo. Iye sakhala wokhumudwa kapena wokwiya cifukwa ca zimene alibe. Komabe kukhala wokhutila sikutanthauza kuti sitisamala ndi mmene zinthu zilili pa umoyo wathu. Mwacitsanzo, sikulakwa ngati Mkhristu akufunafunabe mipata kuti awonjezele utumiki wake kwa Yehova. (Aroma 12:1; 1 Tim. 3:1) Komabe, iye amakhalabe wacimwemwe ngakhale kuti sanalandile mautumiki amene anali kulakalaka pa nthawi imene anali kuwayembekezela.

2. N’cifukwa ciyani kusakhutila n’koopsa kwambili?

2 Kusakhutila ndi zimene tili nazo, kungaticititse kuti tipange zisankho zolakwika. Anthu osakhutila angamadzikhaulitse kugwila nchito maola ambili pofuna kupeza zinthu zosafunika kwenikweni. N’zacisoni kuti Akhristu ena afika ngakhale pa kuba ndalama kapena zinthu zina zimene anali kulakalaka. Pocita zimenezo, mumtima amati, ‘Sindilakwa ndikatenga cinthuci,’ ‘Ndikufuna cinthuci pompanopompano,’ kapena ‘Ndingaigwilitse nchito ndalamayi ndipo ndidzabwezelapo.’ Komabe, kuba kwa mtundu uliwonse kumakhumudwitsa Yehova ndipo kumanyozetsa dzina lake. (Miy. 30:9) Ena anakhumudwa cifukwa sanapatsidwe utumiki umene anali kufuna moti analeka kutumikila Yehova. (Agal. 6:9) N’ciyani cingapangitse mtumiki wa Yehova kufika mpaka poganiza kucita zimenezo? Vuto lingakhale lakuti munthuyo analeka kukhala wokhutila.

3. Kodi ndi mfundo yokhazika mtima pansi iti imene ili pa Afilipi 4:​11, 12?

3 N’zotheka tonsefe kukulitsa khalidwe lokhutila. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Ndaphunzila kukhala wokhutila ndi zimene ndili nazo posatengela mmene zinthu zilili pa moyo wanga.” (Welengani Afilipi 4:​11, 12.) Ngakhale kuti Paulo analemba mawuwa ali m’ndende, iye anakhalabe wacimwemwe. Iye anali ‘ataphunzila cinsinsi’ cokhala wokhutila. Ngati zimativuta kukhala wokhutila, mawu a Paulo komanso zimene zinamucitikila, zimatitsimikizila kuti nafenso tikhoza kukhala okhutila. Khalidwe lokhutila sitibadwa nalo, timacita kuliphunzila. Motani? Tiyeni tikambilane makhalidwe amene angatithandize kuphunzila cinsinsi cokhala wokhutila.

KULITSANI KHALIDWE LA KUYAMIKILA

4. Kodi mzimu woyamikila umatithandiza bwanji kukhala wokhutila? (1 Atesalonika 5:18)

4 Mzimu woyamikila umapangitsa munthu kukhala wokhutila. (Welengani 1 Atesalonika 5:18.) Mwacitsanzo, ngati timayamikila zimene tili nazo pa umoyo, timapewa kuganizila kwambili zinthu zimene tikuzifuna koma tikalibe kuzipeza. Ngati timayamikila mautumiki amene tili nawo palipano, tidzayesetsa kuwasamalila bwino kwambili mautumikiwo, m’malo mongokhalila kuganizila za mautumiki atsopano amene tikufuna. M’pake kuti Malemba amatilimbikitsa kuti tiziikamo mawu oyamikila m’mapemphelo athu. Mzimu woyamikila umatithandiza kukhala ndi “mtendele wa Mulungu umene anthu sangathe kuumvetsa.”​—Afil. 4:​6, 7.

5. Kodi Aisiraeli anali ndi zifukwa ziti zokhalila oyamikila? (Onaninso cithunzi.)

5 Ganizilani zimene zinacitikila Aisiraeli. Kangapo konse ali m’cipululu, iwo anadandaulila Yehova kuti analibe zakudya zimene anali nazo ku Iguputo. (Num. 11:​4-6) N’zoona kuti umoyo m’cipululu unali wovuta. Koma kodi n’ciyani cikanawathandiza kukhala okhutila? Iwo anayenela kuganizila zinthu zimene Yehova anali atawacitilapo kale n’kumuyamikila. Mwacitsanzo, anayenela kukumbukila kuti pamene anali kuzunzidwa ku Iguputo monga akapolo, Yehova anawapulumutsa mwa kugwetsela Aiguputo milili 10. Cina, Aisiraeli atamasulidwa, Yehova anawathandiza kuti ‘atenge zinthu zambili za Aiguputo’ monga siliva, golide, ndi zovala. (Eks. 12:​35, 36) Cinanso, pamene Aisiraeli anali kuthamangitsidwa ndi gulu la nkhondo la Farao, Yehova anawapulumutsa mozizwitsa pogawa Nyanja Yofiila. Ndipo pamene anali m’cipululu, tsiku lililonse anali kuwapatsa mana. Ndiye vuto linali pati? Aisiraeli sanali okhutila, osati cifukwa cakuti analibe cakudya, koma cifukwa cakuti sanali kuyamikila zimene anali nazo pa nthawiyo.

Aisiraeli ena akudandaulila Mose poonetsa kusakhutila ndi mana amene akutolela. Ena omwe ali pafupi akupitiliza kutolela manawo ndipo akuyang’ana zimene zikucitika.

N’cifukwa ciyani Aisiraeli anakhala osakhutila? (Onani ndime 5)


6. Kodi ndi njila zina ziti zimene zingatithandize kukulitsa khalidwe loyamikila?

6 Ndiye mungatani kuti mukhale woyamikila? Coyamba, muzipatula nthawi tsiku lililonse yoganizila zinthu zabwino zimene muli nazo. Mungacite bwino kulemba zinthu ziwili kapena zitatu zimene mwayamikila pa tsikulo. (Maliro 3:​22, 23) Caciwili, muzionetsetsa kuti mwayamikila anthu amene akucitilani zinazake. Ndipo koposa zonse, muziyamikila Yehova tsiku lililonse. (Sal. 75:1) Cacitatu, muzisankha kukhala ndi mabwenzi amene ali ndi khalidwe loyamikila. Kuyamikila kumayambukila. Ndi mmenenso zilili ndi kusakhutila. (Deut. 1:​26-28; 2 Tim. 3:​1, 2, 5) Tikakulitsa khalidwe la kuyamikila, tidzacepetsa mzimu wosakhutila.

7. Kodi Aci anacita ciyani kuti akhalenso ndi mzimu woyamikila? Ndipo panakhala zotsatilapo zotani?

7 Ganizilani zimene zinacitikila Aci wa ku Indonesia. Ananena kuti: “Pa nthawi ya mlili wa COVID-19, ndinayamba kuyelekezela umoyo wanga ndi umoyo wa okhulupilila anzanga. Izi zinacititsa kuti ndikhale wosakhutila.” (Agal. 6:4) N’ciyani cinam’thandiza kusintha maganizo ake? Iye anati: “Ndinayamba kuwelenga madalitso amene ndinali kulandila tsiku lililonse, ndipo ndinali kusinkhasinkha zinthu zabwino zimene ndinapeza cifukwa cokhala m’gulu la Mulungu. Kenako, ndinali kumuyamikila Yehova. Izi zinandicititsa kukhaladi wokhutila.” Ngati inunso simuli wokhutila cifukwa ca mmene zinthu zilili pa umoyo, mungacite bwino kuganizila zimene Aci anacita kuti mukhalenso ndi mzimu woyamikila.

IKANI MAGANIZO ANU PA ZINTHU ZOFUNIKA NDIPO KHALANIBE WODZICEPETSA

8. Kodi Baruki anagwela mu msampha wotani?

8 Pa nthawi ina, kalembela wa mneneli Yeremiya, Baruki, anakhalapo wosakhutila. Baruki anali kucita utumiki wovuta. Utumikiwo unali wocilikiza Yeremiya pamene anali kupeleka uthenga wamphamvu kwa mtundu wosayamikila. Koma pa nthawi ina, iye anasiya kuika maganizo ake pa zinthu zofunika. M’malo moika maganizo ake pa zimene Yehova anafuna kuti acite, mwacionekele anayamba kuganizila kwambili za iyemwini komanso zimene anafuna kucita. Kudzela mwa Yeremiya, Yehova anauza Baruki kuti: “Iwe ukufunafuna zinthu zazikulu. Leka kufunafuna zinthu zimenezo.” (Yer. 45:​3-5) M’mawu ena, Yehova anali kuuza Baruki kuti: “Baruki, khala wokhutila ndi zimene uli nazo.” Baruki analandila uphunguwo ndipo anapitiliza kukhala bwenzi la Yehova.

9. Malinga ndi 1 Akorinto 4:​6, 7, kodi kudzicepetsa kudzatithandiza kuzindikila mfundo iti? (Onaninso zithunzi.)

9 Nthawi zina, Mkhristu angaganize kuti ayenela kupatsidwa utumiki winawake zivute zitani. N’kutheka kuti angakhale ndi luso lapadela, wakhama pa nchito, kapena wodziwa zinthu zambili. Mwinanso angakhale ndi zonse zitatu. Komabe zingacitike kuti ena apatsidwa udindo umene iye akuufunitsitsa. N’ciyani cingamuthandize kuwongolela maganizo ake? Angacite bwino kusinkhasinkha zimene mtumwi Paulo analemba pa 1 Akorinto 4:​6, 7. (Welengani.) Utumiki uliwonse kapena luso lililonse limene tili nalo, linacokela kwa Yehova. Yehova sanatipatse zinthu zimenezi cifukwa cakuti ndife apadela kuposa ena. Amatipatsa mwa cisomo cake.​—Aroma 12:​3, 6; Aef. 2:​8, 9.

Zithunzi: Abale ndi mlongo akucita mautumiki osiyanasiyana. 1. M’bale akuona mapaipi a madzi pa cimango. 2. Mlongo akufunsidwa mafunso ndi m’bale pa msonkhano wadela pa wacinenelo camanja. 3. M’bale akukamba nkhani pa msonkhano wa mpingo.

Mphatso iliyonse imene tili nayo imacokela kwa Yehova mwa cisomo cake (Onani ndime 9)c


10. Tingalikulitse motani khalidwe la kudzicepetsa?

10 Tingakulitse khalidwe la kudzicepetsa tikamaganizila mozama citsanzo ca Yesu. Ganizilani zinacitika usiku umene Yesu anasambika mapazi atumwi ake. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Yesu podziwa [1] kuti Atate wake anapeleka zinthu zonse m’manja mwake, ndiponso [2] kuti anacokela kwa Mulungu komanso [3] kuti anali kupita kwa Mulungu, ananyamuka, . . . n’kuyamba kusambika mapazi a ophunzila ake.” (Yoh. 13:​3-5) Izi zikanacititsa Yesu kuganiza kuti ophunzila ake ndiwo anayenela kusambika iye mapazi. Koma pa nthawi yonse imene anali pa dziko lapansi, iye sanaganizilepo kuti ayenela kukhala ndi nyumba yabwino, ndalama zambili, kapenanso kukhala umoyo wawofuwofu. (Luka 9:58) Yesu anali wodzicepetsa komanso wokhutila. Anatisiyila citsanzo cabwino.​—Yoh. 13:15.

11. Kodi kudzicepetsa kwam’thandiza bwanji Dennis kukhala wokhutila?

11 Dennis wa ku Netherlands, wakhala akuyesetsa kutsatila citsanzo ca Yesu ca kudzicepetsa. Koma sicinakhale capafupi kucita zimenezo. Iye anati: “Nthawi zina ndimaona mzimu wonyada ndi wosakhutila ukukula mwa ine makamaka ngati munthu wapatsidwa utumiki umene n’nali kuufuna. Izi zikacitika, ndimawelenga komanso kumvetsela nkhani zokamba pa kudzicepetsa. Pa JW Library®, ndinapanga tagia yokhala ndi Malemba enaake okamba za kudzicepetsa kuti ndiziwapeza mwamsanga komanso kuwawelenga. Ndipo ndinacitanso dawunilodi nkhani zina zokamba za kudzicepetsa pa foni panga ndipo ndimazimvetsela kawilikawili.b Ndaphunzila kuti nchito iliyonse imene timagwila, timaigwila kuti tipeleke ulemelelo kwa Yehova osati kwa ife. Aliyense wa ife amagwilako mbali yocepa pa zimene Yehova akukwanilitsa.” Ngati nanunso mwaona kuti mwayamba kukhala ndi mzimu wosakhutila, citam’poni kanthu kuti mukulitse khalidwe la kudzicepetsa. Izi zidzalimbitsa ubwenzi wanu ndi Yehova ndipo zidzakuthandizani kukhala wokhutila.​—Yak. 4:​6, 8.

MUZISINKHASINKHA ZA CIYEMBEKEZO CANU

12. Ndi ciyembekezo citi ca zamtsogolo cimene cimatipangitsa kukhala okhutila? (Yesaya 65:​21-25)

12 Tikamasinkhasinkha madalitso amene tidzalandila m’tsogolo, timakhala okhutila. M’buku la Yesaya, Yehova amatiuza kuti amadziwa kuti timakumana ndi mavuto ambili. Koma analonjeza kuti adzawacotsa mavuto onsewa. (Welengani Yesaya 65:​21-25.) Analonjeza kuti tizikakhala m’nyumba zabwino komanso zotetezeka. Anatilonjezanso kuti tizikagwila nchito yosangalatsa komanso kuti tizikadya zakudya zokoma zopatsa thanzi. Sitidzadanso nkhawa poganizila zoopsa zimene zingavulaze ife kapena ana athu. (Yes. 32:​17, 18; Ezek. 34:25) Tsogolo lathu ndi losangalatsa komanso lotsimikizika.

13. Ndi pa nthawi iti makamaka pamene tiyenela kuika maganizo athu pa ciyembekezo cathu?

13 N’cifukwa ciyani m’pofunika kwambili kuika maganizo athu pa ciyembekezo cathu palipano kuposa n’kale lonse? Cifukwa n’cakuti tikukhala ‘m’masiku otsiliza’ ndipo tonsefe timakumana ndi mavuto aakulu. (2 Tim. 3:1) Tsiku lililonse, Yehova amatithandiza kupilila mwa kutitsogolela, kutipatsa mphamvu, komanso kutipatsa thandizo limene tikufunikila. (Sal. 145:14) Kuwonjezela apo, ciyembekezo cathu cidzatithandiza pamene tikukumana ndi mavuto. Mwina zimakuvutani kupezela banja lanu zosowa zakuthupi. Koma kodi izi zitanthauza kuti nthawi zonse mudzakhalabe wovutika? Kutalitali! Yehova walonjeza kukupatsani zimene mukufunikila, ndipo adzakupatsaninso zoculuka, inde zoculuka zedi m’Paradaiso. (Sal. 9:18; 72:​12-14) Mwinanso mukudwala matenda aakulu, mukuvutika maganizo, kapena mukukumana ndi zovuta za ukalamba. Kodi muzivutika conci kwamuyaya, popanda ciyembekezo cakuti mudzacila? Kutalitali! M’dziko latsopano la Mulungu, matenda ndi imfa zidzathelatu. (Chiv. 21:​3, 4) Ciyembekezoci cimatithandiza kukhala okhutila palipano n’kupewa kukhala okwiya ndi okhumudwa. Tingakhalebe okhutila ngakhale pamene tacitidwa zopanda cilungamo, tataikilidwa okondedwa athu mu imfa, tikudwala, kapena pamene takumana ndi mayeso ena alionse. Zitheka bwanji? Izi zimatheka cifukwa timadziwa kuti ngakhale mavuto athu palipano atakula motani, “mavuto amene tikukumana nawo ndi akanthawi.” Ndipo dziko latsopano lidzabweletsa mpumulo wosatha posacedwapa.​—2 Akor. 4:​17, 18.

14. Kodi tingacilimbitse motani ciyembekezo cathu?

14 Popeza ciyembekezo cimatithandiza kuti tikhale okhutila, kodi tingacilimbitse motani? Munthu amavala magalasi kuti athe kuona zinthu zimene zili patali. Ifenso kuti tizitha kuona bwinobwino m’maganizo mwathu madalitso a m’Paradaiso, tiyenela kumacita zinthu zolimbitsa ciyembekezo cathu. Nkhawa ya zacuma ikatikulila, tingacite bwino kuganizila mmene umoyo udzakhalile m’Paradaiso, mmene simudzakhala ndalama, nkhongole, ndi kusauka. (1 Tim. 6:19) Popeza timakhala ndi nkhawa zambili palipano, zingakhale zovuta kwa ife kuganizila za tsogolo labwino. Komabe, m’kupita kwa nthawi, tikamaganizila za tsogolo limene Yehova watilonjeza, zidzakhala zosavuta kuganizila zimene Yehova watilonjeza m’malo moganizila kwambili nkhawa zathu.

15. Kodi mwaphunzilapo ciyani pa zimene Christa anakamba?

15 Onani mmene ciyembekezo cathandizila Christa, mkazi wa Dennis yemwe tam’chula m’ndime 11. Iye anati: “Ndili ndi matenda omwe amandifooketsa kwambili moti sindimatha kuyenda, ndipo ndimagwilitsila nchito njinga ya olumala. Nthawi zambili ndimakhala cigonele. Ndimamva ululu tsiku lililonse. Posacedwapa dokotala anandiuza kuti sindidzacila. Nthawi yomweyo ndinati camumtima: ‘Mmene ndionela tsogolo si mmene akulionela dokotalayu.’ N’naika maganizo anga pa ciyembekezo canga, ndipo zimenezi zinandipatsa mtendele wa mumtima. Palipano ndikulimbana ndi mavuto ambili, koma ndikuyembekezela umoyo wokoma m’tsogolo.”

“ONSE AMENE AMAMUOPA SASOWA KANTHU”

16. N’cifukwa ciyani Mfumu Davide analemba kuti anthu oopa Yehova “sasowa kanthu”?

16 Ngakhale titakhala okhutila, tidzakumanabe ndi mavuto. Ganizilani za Mfumu Davide. Baibo imakamba kuti iye anatayikilidwa ana ake atatu. Cina, ena anamuneneza mabodza a zinthu zimene sanacite. Kuwonjezela apo, anakanidwa ndi anzake, ndipo kangapo konse, Mfumu Sauli inafuna kumupha. Ngakhale n’telo, pamene anali kukumana ndi mavutowa, iye anati ponena za Yehova: “Onse amene amamuopa sasowa kanthu.” (Sal. 34:​9, 10) N’ciyani cinamupangitsa kukamba zimenezi? Cifukwa cinali cakuti ngakhale kuti Yehova satichinjiliza ku mavuto a m’dzikoli, amatipatsa zimene tikufunikiladi. (Sal. 145:16) Cinanso n’cakuti sitikayikila kuti Yehova adzatithandiza m’masautso athu. N’zotheka kukhala okhutila mosasamala kanthu mmene zinthu zili pa umoyo wathu.

17. N’cifukwa ciyani mwatsimikiza mtima kuphunzila cinsinsi cokhala wokhutila?

17 Yehova amafuna kuti mukhale wokhutila. (Sal. 131:​1, 2) Conco citani zonse zotheka kuti muphunzile cinsinsi cokhala okhutila. Mukacita khama kukulitsa khalidwe la kuyamikila, kuganizilabe zinthu zofunika, kukhalabe wodzicepetsa, komanso mukalimbitsa ciyembekezo canu, mudzatha kunena kuti: “Ndaphunzila kukhala wokhutila.”​—Afil. 4:11.

KODI ZINTHU ZOTSATILAZI ZINGAKUTHANDIZENI BWANJI KUKHALA WOKHUTILA?

  • Kukhala woyamikila

  • Kuika maganizo pa zinthu zofunika ndi kukhala wodzicepetsa

  • Kusinkhasinkha za ciyembekezo canu

NYIMBO 118 “Tiwonjezeleni Cikhulupililo”

a Kuti mudziwe zambili pa nkhani ya matagi, onelelani vidiyo yakuti Zimene Gulu Likukwanilitsa​—Mfundo Zothandiza Poseŵenzetsa JW Library pa jw.org.

b Mwacitsanzo, onelelani pulogilamu ya Kulambila kwa m’Mawa ya mutu wakuti Kodi Ndinu Odzicepetsa Kapena Wodzikuza? pa jw.org.

c MAWU OFOTOKOZELA CITHUNZI: M’bale akuona mapaipi a madzi pa cimango kuti aone ngati akugwila bwino nchito, mlongo amene anaphunzila cinenelo camanja akufunsidwa mafunso pa msonkhano wadela, ndipo m’bale akukamba nkhani ya anthu onse.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani