LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w25 August masa. 20-25
  • Zimene Zingatithandize pa Nkhondo Yolimbana ndi Zilakolako Zoipa

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Zimene Zingatithandize pa Nkhondo Yolimbana ndi Zilakolako Zoipa
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • MAGANIZO AMENE “WOIPAYO” AMAFUNA KUTI TIZIKHALA NAO
  • MAGANIZO AMENE TINGAKHALE NAO CIFUKWA CAKUTI NDIFE OPANDA UNGWIRO
  • ZIMENE MUYENERA KUCITA KUTI MUPAMBANE
  • “PITIRIZANI KUDZIYESA”
  • Khalani Maso Kuti Musagonje pa Mayeselo
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
  • Pitilizani Kutsatila Yesu Pambuyo pa Ubatizo Wanu
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
  • Zimene Yehova Anacita Kuti Apulumutse Anthu ku Ucimo
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
  • Zisankho Zimene Zimaonetsa Kuti Timadalila Yehova
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
w25 August masa. 20-25

NKHANI YOPHUNZIRA 35

NYIMBO 121 Kudziletsa N’kofunika

Zimene Zingatithandize pa Nkhondo Yolimbana ndi Zilakolako Zoipa

“Musalole kuti ucimo uzilamulirabe ngati mfumu m’matupi anu oti akhoza kufawo kuti muzitsatira zilakolako zao.”​—AROMA 6:12.

ZOFUNIKA KUMVETSETSA

Zimene zingatithandize (1) kupewa maganizo oona kuti sitingapambane tikayesedwa komanso (2) kuti tisagonje tikayesedwa.

1. Kodi tonsefe timalimbana ndi ciani?

KODI pa nthawi ina munakhalapo ndi cilakolako camphamvu cofuna kucita zinthu zimene Yehova amadana nazo? Ngati n’tero, musaganize kuti mukukumana ndi mayeso aakulu kuposa amene amagwera ena onse. Baibo imati: “Palibe mayesero amene mwakumana nao osiyana ndi amene anthu ena amakumana nao.” (1 Akor. 10:13) Izi zitanthauza kuti zilakolako zilizonse zimene mukulimbana nazo, aliponso ena amene akulimbana nazo. Komabe, Yehova ali nanu, simuli nokha. Ndipo ndi thandizo lake, mukhoza kupambana.

2. Kodi ndi mayesero ati amene Akhristu ena komanso ophunzira Baibo ena akulimbana nao? (Onaninso zithunzi.)

2 Baibo imakambanso kuti: “Munthu aliyense amayesedwa ndi cilakolako cake cimene cimam’kopa ndi kumukola.” (Yak. 1:14) Izi zitanthauza kuti zimene zimakopa munthu wina, zingasiyane ndi zimene zingakope wina. Mwacitsanzo, Akhristu ena angayesedwe kuti acite ciwerewere ndi munthu amene simwamuna kapena mkazi mnzao, pomwe ena angayesedwe kuti acite zimenezo ndi mwamuna kapena mkazi mnzao. Awo amene anasiya kuonerera zolaula angakhale ndi cikhumbo camphamvu cofuna kuyambiranso cizolowezici. Izi zingacitikenso kwa ambiri amene anasiya kusewenzetsa mankhwala osokoneza bongo kapena kwa amene anali kumwa mowa mwaucidakwa. Izi ndi zina mwa zilakolako zoipa zimene Akhristu ena komanso maphunziro ena a Baibo akulimbana nazo. Pa nthawi ina, tonse tinamvapo monga mtumwi Paulo, amene analemba kuti: “Pamene ndikufuna kucita zinthu zabwino, zoipa zimakhala mkati mwangamu.”​—Aroma 7:21.

Tingayesedwe nthawi iliyonse komanso kulikonse (Onani ndime 2)c


3. Ngati munthu wakhala akulimbana ndi cilakolako coipa kwa nthawi yaitali, angayambe kuganiza ciani?

3 Ngati mwakhala mukulimbana ndi cilakolako coipa kwa nthawi yaitali, mungaganize kuti mulibe mphamvu zokwanitsa kugonjetsa cilakolakoco. N’kutheka mungaganizenso kuti mulibe ciyembekezo cifukwa coganiza kuti Yehova amangokhalira kukuimbani mlandu cifukwa cokhala ndi zilakolako zoipa. Koma dziwani kuti maganizo onse awiriwa sioona! Pofotokoza cifukwa cake tikutero, m’nkhani ino tiyankha mafunso awiriwa: (1) Kodi maganizo odziona kuti tilibe mphamvu komanso ciyembekezo amacokera kuti? (2) Kodi mungacite ciani kuti mupambane pa nkhondo yolimbana ndi zilakolako zoipa?

MAGANIZO AMENE “WOIPAYO” AMAFUNA KUTI TIZIKHALA NAO

4. (a) N’cifukwa ciani Satana amafuna kuti tiziona kuti tilibe mphamvu zokwanitsa kulimbana ndi mayesero? (b) Nanga n’cifukwa ciani tinganene kuti tili nazo mphamvu zotithandiza kulimbana ndi mayesero?

4 Satana amafuna kuti tiziganiza kuti tilibe mphamvu zokwanitsa kugonjetsera mayesero. Yesu anaonetsa bwino lomwe kuti Satana adzatiyesa pomwe anauza ophunzira ake kupemphera kuti: “Tithandizeni kuti tisagonje tikamayesedwa, koma mutiteteze kwa woipayo.” (Mat. 6:13) Pa nthawi ina, Satana anakamba kuti anthu alibe cifuno cokhalabe okhulupirika akayesedwa. (Yobu 2:​4, 5) N’cifukwa ciani Satana amaganiza conco? Satana ndi amene anayamba kukodwa m’cilakolako cake ndipo anasankha kukhala wosakhulupirika kwa Yehova. Mosakaikira, amaganiza kuti tili monga iye, kuti tikhoza kupandukira Yehova mosabvuta tikayesedwa. Satana anafika ngakhale poganiza kuti Mwana wangwiro wa Mulungu angagonje ndi mayesero. (Mat. 4:​8, 9) Koma kodi n’zoona kuti tilibedi mphamvu zotithandiza kupambana nkhondo yolimbana ndi zilakolako zoipa? Ai! Limenelo ndi bodza lamkunkhuniza! Timagwirizana ndi mau amene mtumwi Paulo analemba akuti: “Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kucokera kwa Mulungu amene amandipatsa mphamvu zimene ndikufunikira.”​—Afil. 4:13.

5. Tidziwa bwanji kuti Yehova amatidalira kuti tingathe kupambana nkhondo yolimbana ndi zilakolako zoipa?

5 Mosiyana kwambiri ndi Satana, Yehova amatidalira kuti tingathe kugonjetsa zilakolako zoipa. N’cifukwa ciani tanena conco? Yehova anakambiratu kuti khamu lalikulu la anthu okhulupirika lidzapulumuka cisautso cacikulu. Kodi mfundoyi ionetsa ciani? Yehova amene sanganame ndiye ananena kuti khamu lalikulu la anthu, osati anthu owerengeka, adzalowa m’dziko lake latsopano ali oyera, ‘atacapa mikanjo yawo n’kuiyeretsa m’magazi a Mwanawankhosa.’ (Chiv. 7:​9, 13, 14) Conco izi zionetseratu kuti Yehova sationa kuti tilibe mphamvu zokwanitsa kupambana pa nkhondo yolimbana ndi zilakolako zoipa.

6-7. N’cifukwa ciani Satana amafuna kuti tiziganiza kuti tilibe ciyembekezo cakuti tingapambane polimbana ndi mayesero?

6 Kuonjezera pa kutipangitsa kuona kuti tilibe mphamvu, Satana amafunanso kutipangitsa kuona kuti tilibe ciyembekezo poticititsa kuganiza kuti Yehova adzatiimba mlandu, cabe cifukwa cokhala ndi zilakolako zoipa. Tingacitenso bwino kuganizira cifukwa cake Satana amafuna kuti tiziganiza conco. Satana ndiye alibe ciyembekezo. Iye anaweruzidwa ndi Yehova kuti siwoyenera kulandira moyo wosatha. (Gen. 3:15; Chiv. 20:10) N’zosacita kufunsa kuti Satana amafuna kuti tiziganiza monga iye kuti tilibe ciyembekezo, makamaka cifukwa cakuti tili ndi dalitso lodzakhala ndi moyo wosatha m’tsogolo, lomwe iye alibe. Koma zoona zake n’zakuti ife tili naco ciyembekezo! Ndi iko komwe, Baibo imatitsimikizira kuti Yehova amafuna kutithandiza osati kutiimba mlandu. Iye “sakufuna kuti munthu aliyense adzaonongedwe, koma akufuna kuti anthu onse alape.”​—2 Pet. 3:9.

7 Conco tikamakhulupirira kuti tilibe mphamvu kapena ciyembekezo cakuti tingapambane polimbana ndi zilakolako zoipa, ndiye kuti m’ceniceni tikuganiza mmene Satana amafuna kuti tiziganizira. Kuzindikira mfundoyi kudzatithandiza kuti tilimbitse cikhulupiriro cathu polimbana naye.​—1 Pet. 5:​8, 9.

MAGANIZO AMENE TINGAKHALE NAO CIFUKWA CAKUTI NDIFE OPANDA UNGWIRO

8. Kuonjezera pa kucita zoipa, kodi Baibo imakambanso ciani za ucimo? (Salimo 51:5) (Onaninso mbali yakuti “Kufotokozera Mau Ena.”)

8 Kucotserako Satana, pali cinthu cina cimene cingatipangitse kuganiza kuti tilibe mphamvu komanso ciyembekezo cakuti tingapambane nkhondo yolimbana ndi zilakolako zoipa. N’ciani cimeneco? Ndi ucimo umene tinatengera kwa makolo athu oyambirira.a​—Yobu 14:4; werengani Salimo 51:5.

9-10. (a) Kodi Adamu ndi Hava anamva bwanji atacimwa? (Onaninso cithunzi.) (b) Kodi ucimo umatipangitsa kumva bwanji?

9 Onani mmene Adamu ndi Hava anamvera pambuyo pakuti acimwa. Atapandukira Yehova, iwo anapita kukabisala ndipo anaphimba matupi awo. Ponena za nkhaniyi, buku la Insight on the Scriptures, limati: “Ucimo unawacititsa kudziimba mlandu, kukhala ndi nkhawa, kudzimva osatetezeka, komanso amanyazi.” Zinali ngati Adamu ndi Hava anatsekeredwa m’nyumba imene inali ndi zipinda zinai zimenezi. Iwo akanakwanitsa kucoka m’cipinda cimodzi kupita m’cipinda cina, koma sakanakwanitsa kutulukamo m’nyumbayo. Iwo sakanakwanitsa kudziombola ku mkhalidwe wao waucimo.

10 Komabe, mkhalidwe wathu sufanana ndendende ndi mkhalidwe wa Adamu ndi Hava. Dipo limatiyeretsa ndi kutithandiza kukhala pa ubale wabwino ndi Mulungu. Koma siligwira nchito kwa makolo athuwo. (1 Akor. 6:11) Ngakhale n’tero, tinatengerabe ucimo kwa iwo. Ndiye cifukwa cake nafenso timadziimba mlandu, timakhala ndi nkhawa, komanso timadzimva osatetezeka ndi amanyazi. Ndipo Baibo imanena kuti ucimo ukupitirizabe kukhala ndi cisonkhezero camphamvu pa mtundu wa anthu kuti azicita zoipa. Ucimowo wacita zimenezo “ngakhalenso kwa anthu amene sanacimwe ngati mmene anacimwira Adamu.” (Aroma 5:14) Ngakhale kuti mfundo yoona imeneyi ingatipangitse kumva olefuka, sitiyenera kumva kuti tilibe mphamvu komanso ciyembekezo cakuti tingapambane nkhondo yolimbana ndi zilakolako zoipa. N’zotheka kugonjetsa maganizo olefula amenewa. Motani?

Adamu ndi Hava ali amanyazi ndipo akutuluka m’munda wa Edeni atavala zikumba nyama.

Chimo linacititsa Adamu ndi Hava kudziimba mlandu, kukhala ndi nkhawa, komanso kudzimva osatetezeka ndi amanyazi (Onani ndime 9)


11. Tiyenera kucita ciani tikamva kuti tilibe mphamvu zokwanitsa kulimbana ndi zilakolako zoipa? Ndipo n’cifukwa ciani? (Aroma 6:12)

11 Tikamva kuti mphamvu yotithandiza kulimbana ndi zilakolako zoipa yatithela, tingacite bwino kuona zimenezo ngati kuti ucimo ukutilankhula. Ndipo sitiyenera kuumvetsera. N’cifukwa ciani sitiyenera kuumvela? Baibo imatiuza kuti ngakhale kuti ndife ocimwa, sitiyenera kulola ucimo kupitiriza ‘kulamulira ngati mfumu’ mwa ife. (Werengani Aroma 6:12.) Izi zitanthauza kuti tikayesedwa kuti ticite coipa, zili kwa ife kaya kucita coipaco kapena kucipewa. (Agal. 5:16) Yehova sangatipemphe kucita zimene sitingakwanitse kucita. Iye amatidalira kuti tingathe kugonjetsa mayesero. (Deut. 30:​11-14; Aroma 6:6; 1 Ates. 4:3) Conco n’zoonekeratu kuti mphamvu tili nazo zokwanitsa kugonjetsa zilakolako zoipa!

12. Kodi tiyenera kucita ciani tikamva kuti tilibe ciyembekezo? Nanga n’cifukwa ciani?

12 Mofananamo, tikamva kuti tilibe ciyembekezo poganiza kuti Yehova amangokhalira kutiimba mlandu, cabe cifukwa cokhala ndi zilakolako zoipa, tingacite bwino kuona zimenezo ngati kuti ucimo ukutilankhula. Ndipo sitifunika kuumvetsera. N’cifukwa ciani sitiyenera kuumvetsera? Baibo imaphunzitsa kuti Yehova adziwa bwino kuti tinabadwa ocimwa. (Sal. 103:​13, 14) Iye “amadziwa zonse” zokhudza ife. Mwacitsanzo, amadziwa mmene ucimo umakhudzira kaganizidwe ndi zocita za aliyense wa ife. (1 Yoh. 3:​19, 20) Malinga ngati sitigonja polimbana ndi zilakolako zoipa, Yehova adzationa kuti ndife oyera. N’cifukwa ciani ndife otsimikiza za zimenezi?

13-14. Kodi kungokhala ndi zilakolako zoipa kutanthauza kuti ndife olephera? Fotokozani.

13 Baibo imaonetsa kuti pali kusiyana kwakukulu pakati pa kukhala ndi zilakolako zoipa ndi kucita zinthu zoipa. Nthawi zina, zilakolako zoipa zimabwera zokha. Koma kucita zoipa, munthu amacita kufuna. Mwacitsanzo, ena mwa anthu amene anali mu mpingo wa ku Korinto wa m’zaka za zana loyamba, anali kucita mathanyula asanakhale Akhristu. Paulo analemba kuti: “Ena a inu munali otero.” Kodi izi zitanthauza kuti iwo sanakhalenso ndi cilakolako cofuna kucita zamathanyula? Zilakolako zaconco zimakhala zozika mizu. Conco sitingakambe kuti anthuwo analekeratu kukhala ndi cilakolako cofuna kucita zamathanyula. Koma Akhristu amene anaonetsa khalidwe la kudziletsa ndi kupewa kucita zimene zilakolako zaozo zinali kufuna kuti acite, anakhala obvomerezeka kwa Yehova. Iye anali kuwaona kuti ‘asambitsidwa n’kukhala oyera.’ (1 Akor. 6:​9-11) Izi zingacitikenso kwa inu.

14 Kaya mukulimbana ndi zilakolako zotani zoipa, mungathe kuzigonjetsa. Ngakhale kuti simungazithetseretu, mungakwanitse kukhala odziletsa ndi kupewa ‘kucita zofuna za thupi ndi maganizo [anu].’ (Aef. 2:3) Kodi mungacite bwanji zimenezi ndi kupambana nkhondo yolimbana ndi zilakolako zoipa?

ZIMENE MUYENERA KUCITA KUTI MUPAMBANE

15. Kodi kubvomereza kuti tili ndi zofooka kungatithandize bwanji kupambana nkhondo yolimbana ndi zilakolako zoipa?

15 Kuti mupambane nkhondo yolimbana ndi zilakolako zoipa, muyenera kubvomereza kuti muli ndi zofooka. Khalani osamala kuti musadzipusitse ndi “maganizo abodza.” (Yak. 1:22) Mwacitsanzo, munthu amene ali ndi bvuto la kamwedwe ka mowa angapereke cifukwa codzikhululukira pokamba kuti, ‘Ine ndimamwako bwino poyerekezera ndi ena.’ Kapena mwamuna amene ali ndi bvuto loonerera zamalisece angaimbe mlandu mkazi wake ponena kuti, ‘Mkazi wanga akanakhala kuti amandionetsa cikondi cofikapo, sindikanakhala ndi bvutoli.’ Kuganiza motero kungapangitse kuti cikhale capafupi kugonja ku mayesero. Conco musamapereke zifukwa zodzikhululukira. Ndipo musamaimbe ena mlandu pa zimene mwacita.​—Agal. 6:7.

16. Muyenera kucita ciani kuti mukhale otsimikiza kucita zoyenera?

16 Kuonjezera pa kubvomereza kuti muli ndi zofooka, muyeneranso kukhala otsimikiza kuti musasunthike pa cisankho cimene munapanga cakuti musagonje pa mayesero. (1 Akor. 9:​26, 27; 1 Ates. 4:4; 1 Pet. 1:​15, 16) Dziwani mayesero amene mumalimbana nao kawiri-kawiri komanso nthawi pomwe amabwera. N’kutheka angakhale mayesero enaake, kapena nthawi inayake pa tsiku pomwe zimakhala zosabvuta kuti muyesedwe. Mwacitsanzo, kodi mumagonja mosabvuta mukayesedwa pomwe mwalema kapena kukada usiku? Muzikonzekera pasadakhale zimene mudzacita mayeserowo akabwera. Nthawi yabwino koposa imene mufunika kucita zimenezi ndi pamene mayeserowo asanabwere.​—Miy. 22:3.

17. Tiphunzirapo ciani pa citsanzo ca Yosefe? (Genesis 39:​7-9) (Onaninso cithunzi.)

17 Onani zimene Yosefe anacita pamene mkazi wa Potifara anali kumunyengerera kuti agone naye. Iye sanaganizirepo kawiri katatu, koma anamukana mwamphamvu nthawi yomweyo. (Werengani Genesis 39:​7-9.) Izi zionetsa kuti Yosefe anali kudziwa kuti kugona ndi mkazi wa mwini linali chimo ngakhale pamene mkazi wa Potifarayo asanayambe kumunyengerera kuti agone naye. Mofananamo, muyenera kutsimikiza mtima kucita zoyenera mayesero asanabwere. Kucita zimenezi kudzapangitsa kuti cikhale cosabvuta kwa inu kucita coyenera mukayesedwa cifukwa munasankhiratu zoyenera kucita.

Zithunzi: 1. Yosefe akuthawa mkazi wa Potifara yemwe wagwira malaya ake. 2. M’bale wacinyamata akukana mtsikana yemwe akumufuna.

Muzikana mayesero mwamsanga monga anacitira Yosefe! (Onani ndime 17)


“PITIRIZANI KUDZIYESA”

18. Kodi mungacite ciani kuti mupambane nkhondo yolimbana ndi zilakolako zoipa? (2 Akorinto13:5)

18 Kuti mupambane pa nkhondo yolimbana ndi zilakolako zoipa, muyenera ‘kupitiriza kudziyesa.’ Izi zitanthauza kuti muyenera kupitiriza kudzifufuza nthawi zonse kuti muone mmene mukucitira. (Werengani 2 Akorinto 13:5.) Nthawi ndi nthawi, muzisanthula kaganizidwe ndi kacitidwe kanu ka zinthu ndipo muzipanga masinthidwe ofunikira. Mwacitsanzo, ngakhale pamene mwakwanitsa kugonjetsa mayesero, dzifunseni kuti: ‘Kodi zanditengera utali wotani kuti ndikane?’ Ngati mwaona kuti zinakutengerani nthawi kuti muwapewe mayeserowo, musadziimbe mlandu. M’malomwake, citani zonse zimene mungathe kuti mukacite bwino ulendo wotsatira zikakacitikanso. Mungacite bwino kudzifunsa mafunso monga akuti: ‘Maganizo olakwika akandibwerera, kodi ndimacitapo kanthu mwamsanga kuti ndiwacotse? Kodi zosangalatsa zimene ndimasankha zimapangitsa kuti zikhale zobvuta kwa ine kugonjetsa mayesero? Kodi ndimayang’ana kumbali mwamsanga kukaonekera zithunzi zolaula? Kodi ndimamvetsa kuti kutsatira miyeso ya Yehova nthawi zonse kungandipindulire, ngakhale kuti ndingafunike kucita khama kukulitsa khalidwe la kudziletsa kuti ndiitsatire?’​—Sal. 101:3.

19. Kodi zisankho zolakwika zimene zingaoneke zing’ono-zing’ono, zingacititse bwanji kuti zikhale zobvuta kwa ife kupambana polimbana ndi zilakolako zoipa?

19 Pamene mukudzifufuza, muyenera kupewa kupereka zifukwa zodzikhululukira. Baibo imati: “Mtima ndi wopusitsa kwambiri kuposa cinthu ciliconse ndipo ungathe kucita cina ciliconse coipa.” (Yer. 17:9) Yesu anakamba kuti mu mtima mumacokera “maganizo oipa.” (Mat. 15:19) Mwacitsanzo, munthu amene analeka kuonerera zamalisece, m’kupita kwa nthawi angaganize kuti palibe bvuto kupenya zithunzi zodzutsa cilakolako cakugonana cifukwa sizamalisece kwenikweni. Kapena anagaganize kuti, ‘Palibe bvuto kuganizira kuti ndikucita zinthu zolakwika malinga sindikuzicitadi zinthuzo.’ Ngati munthu akuganiza mwanjira imeneyi, zimakhala ngati mtima wake wonyenga ‘ukumukonzekeretsa kucita zimene thupi limalakalaka.’ (Aroma 13:14) N’ciani cingakuthandizeni kuti mupewe kucita zimenezi? Muzipewa kupanga zisankho zing’ono-zing’ono zolakwika zimene zingakutsogolereni kuti mupange zisankho zikulu-zikulu zolakwika.b Muzipewanso “maganizo oipa” amene angacititse kuti muzipereka zifukwa zodzikhululukira mukalakwitsa zinazake.

20. Kodi tikuyembekezera tsogolo lotani? Ndipo n’ciani cingatithandize palipano?

20 Monga taonera, Yehova amatipatsa mphamvu zotithandiza kugonjetsa mayesero. Cina, timayamikira cifundo cake cimene cimatheketsa kuti tikhale ndi ciyembekezo cokakhala ndi moyo wosatha m’dziko latsopano! Zidzakhala zosangalatsa kwambiri kutumikira Yehova popanda kulimbana ndi zilakolako zoipa. Koma ngakhale nthawiyo isanafike, ndife otsimikiza kuti tili nazo mphamvu komanso ciyembekezo pa nkhondo yolimbana ndi zilakolako zoipa. Yehova adzatidalitsa cifukwa ca kuyesetsa kwathu ndipo tidzapambana!

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • N’ciani cingatithandize kugonjetsa maganizo odziona kuti tilibe mphamvu komanso ciyembekezo polimbana ndi zilakolako zoipa?

  • Tingacite ciani kuti tisalole ucimo ‘kulamulira ngati mfumu’ mwa ife?

  • N’cifukwa ciani tiyenera ‘kupitiriza kudziyesa’?

NYIMBO 122 Cilimikani, Musasunthike!

a KUFOTOKOZERA MAU ENA: M’Baibo, mau akuti “chimo,” nthawi zambiri amatanthauza kucita zinthu zoipa monga kuba, cigololo, kapena kupha munthu. (Eks. 20:​13-15; 1 Akor. 6:18) M’Malemba ena, mawu akuti “chimo” amakamba za kupanda ungwiro kumene tinatengera kwa makolo athu pobadwa, ngakhale kuti pa nthawiyo tinali tisanacite chimo lililonse.

b Onani kuti mnyamata wa pa Miyambo 7:​7-23 anapanga zisankho zing’ono-zing’ono zolakwika zomwe zinamutsogolera kupanga cisankho cacikulu colakwika comwe ndi kucita ciwerewere.

c MAU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Kumanzere: M’bale wacinyamata ali m’shopu yogulitsa khofi ndipo waona amuna awiri amene akuonetsana cikondi mokopana. Kulamanja: Mlongo waona mwamuna ndi mkazi akusuta.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani