Inu Okalamba, Ndinu Ofunika Kwambili Mumpingo
“Ndimadabwa ndikaganizila kuculuka kwa zinthu zimene ndinali kukwanitsa kucita ndili mtsikana. Koma popeza tsopano ndakalamba, sindikukwanitsanso kucita zinthu zimenezo.”—Connie, wa zaka 83.
Mwina inunso mukulephela kucita zinthu zina cifukwa cakuti ndinu wokalamba. Ngakhale kuti mwatumikila Yehova kwa zaka zambili, mungayambe kukhala ndi maganizo olefula cifukwa cakuti mukulephela kucita zinthu zina tsopano. Mwacitsanzo, mungayambe kuyelekezela zimene mukucita pali pano ndi zimene munali kucita m’mbuyomo. Ngati n’conco, n’ciani cimene cingakuthandizeni kupewa maganizo otelo?
ZIMENE YEHOVA AMAFUNA KUTI MUZICITA
Dzifunseni kuti, ‘Kodi Yehova amafuna kuti ndizicita ciani?’ Mau a pa Deuteronomo 6:5 angakulimbikitseni kwambili. Amati: “Muzikonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, moyo wanu wonse ndi mphamvu zanu zonse.”
Malinga ndi lembali, Yehova amafuna kuti muzim’tumikila ndi mtima wanu wonse, moyo wanu wonse, ndi mphamvu zanu zonse. Mfundoyi ingakuthandizeni kupewa kudziyelekezela ndi anthu ena. Ingakuthandizeninso kupewa kuyelekezela zimene mumacita palipano ndi zimene munali kucita kale.
Ganizilani izi: Kodi munali kum’patsa zotani Yehova muli wacinyamata? Atumiki ambili a Yehova anganene kuti anali kum’patsa zabwino koposa. Munali kum’patsa zabwino koposa malinga ndi mmene zinthu zinalili pa nthawiyo. Nanga tsopano mukutha kum’patsa zotani Yehova? Mwacionekele, panopa mukucita zonse zotheka kuti mum’patse zabwino koposa malinga ndi mmene zinthu zili kwa inu. Mukamaona zinthu mwa njila imeneyi, mudzakhala otsimikiza kuti mofanana ndi kale, mukum’patsa zabwino koposa Yehova. Kalelo munali kum’patsa zabwino koposa ndipo panopa mukupitiliza kutelo.
Mukamacita zonse zomwe mungathe potumikila Yehova mu ukalamba wanu, mumakhala kuti mukum’patsa zabwino koposa monga mmene munali kucitila pa unyamata wanu
MUNGAWATHANDIZE KWAMBILI ANTHU ENA
M’malo moganizila kwambili zinthu zimene simungathenso kucita, muziganizila zinthu zosiyana-siyana zimene mungacite pothandiza ena. Kunena zoona, pokhala Mkhristu wokalamba, pali zinthu zina zimene mungacite pali pano zimene simukanatha kucita pamene munali wacinyamata. Mwacitsanzo, mungathe kucita zotsatilazi:
Muzifotokozelako ena zimene mudziwa. Ganizilani mau otsatilawa opezeka m’Baibo:
Mfumu Davide anati: “Ndinali mwana ndipo tsopano ndakula koma sindinaonepo munthu aliyense wolungama atasiyidwa, kapena ana ake akupemphapempha cakudya.”—Sal. 37:25.
Yoswa anati: “Tsopano ine ndatsala pangʼono kufa. Inu mukudziwa bwino ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse, kuti palibe mau ngakhale amodzi pa malonjezo onse abwino amene Yehova Mulungu wanu ananena, omwe sanakwanilitsidwe. Onse akwanilitsidwa kwa inu. Palibe ngakhale mau amodzi omwe sanakwanilitsidwe.”—Yos. 23:14.
N’kutheka kuti munakambako mau ngati amenewa muli wacinyamata. Davide ndi Yoswa anakamba zimenezi cifukwa ca zimene anaona pa zaka zambili zomwe anakhala ndi moyo. Izi n’zimene zinapangitsa mau ao kukhala ogwila mtima.
Ngati mwatumikila Yehova kwa nthawi yaitali, inunso mungafotokozeleko ena mapindu amene mwapeza pocita zimenezi. Kodi mukukumbukilako nthawi pamene munaona Yehova akuthandiza anthu ake m’njila yapadela? Ngati n’telo, muziuzako ena zocitika zimenezi. Kucita zimenezo kungawatsitsimule ndipo inunso kungakutsitsimuleni. Conco, mungalimbikitse abale ndi alongo mwa kuwafotokozelako zinthu zosiyana-siyana zimene mwaona potumikila Yehova.—Aroma 1:11, 12.
Ngati n’kotheka, muzipezeka pa misonkhano ya pamaso-m’pamaso. Ndipo iyi ndi njila inanso imene mungalimbikitsile ena. Kucita zimenezi kungakulimbikitseni kwambili, ndipo mungalimbikitsenso abale ndi alongo. Connie, amene tam’chulapo kale, anati: “Kupezeka pa misonkhano kumandithandiza kuti ndisafooke. Ndimalimbikitsidwa cifukwa ku Nyumba ya Ufumu abale ndi alongo amandionetsa cikondi. Ndimapatsako ena timphatso poonetsa kuwayamikila. Conco, ndimayesetsa mmene ndingathele kuti ndiciteko zinthu zauzimu limodzi ndi abale ndi alongo anga.”
YEHOVA AMAYAMIKILA UTUMIKI WANU
M’Malemba muli zitsanzo zambili za anthu amene Yehova anali kuwakonda ngakhale kuti sanali kukwanitsa kucita zambili. Ganizilani za Simiyoni, Mwisiraeli amene anali wokalamba pa nthawi imene Yesu anabadwa. Simiyoni akapezeka pa kacisi, mwina anali kuona acinyamata akugwila nchito zofunika za pa kacisi zimene iye sakanakwanitsa. Izi zikanapangitsa Simiyoni kuona kuti sanali wofunika kweni-kweni pamaso pa Yehova. Koma Yehova sanali kumuona conco. Yehova anaona Simiyoni kuti anali “wolungama komanso wodzipeleka kwa Mulungu.” Ndipo anam’dalitsa mwa kum’patsa mwai woona Yesu ali wakhanda. Anam’patsanso mzimu woyela ndi kum’gwilitsa nchito kulosela kuti khandalo ndi limene lidzakhala Mesiya wolonjezedwa. (Luka 2:25-35) Conco, n’zoonekelatu kuti Yehova sanangoona ukalamba wa Simiyoni, koma anaonanso cikhulupililo cake colimba.
Yehova anadalitsa Simiyoni mwa kum’patsa mwai woonako Yesu ali wakhanda komanso kum’gwilitsa nchito kulosela kuti khandalo ndi limene lidzakhale Mesiya
Inunso dziwani kuti Yehova amayamikila mukamam’tumikila mokhulupilika ngakhale pamene simungathe kucita zambili. Musaiwale kuti “mphatso yocokela pansi pa mtima ndi imene Mulungu amakondwela nayo cifukwa Mulungu amafuna kuti munthu apeleke zimene angakwanitse, osati zimene sangakwanitse.”—2 Akor. 8:12.
Conco, muzingocita zimene mungakwanitse. Mwacitsanzo, ganizilani njila zocitila ulaliki zimene mungathe kutengamo mbali, ngakhale kwa nthawi yocepa. Mwina mungalimbikitseko ena mwa kuwatumilako foni kapena kuwalembelako kakalata. Kucita zinthu ngakhale zing’ono-zing’ono zoonetsa cikondi, kungawalimbikitse kwambili alambili anzathu maka-maka ngati amene wacita zinthuzo ndi munthu amene watumikila Yehova kwa nthawi yaitali.
Ena amalephela kucita zambili cifukwa ca mabvuto monga kulemala ndi kudwala. Onani citsanzo ca mlongo wina wa ku East Africa cimene cionetsa kuti anthu otelewa Yehova angawagwilitsebe nchito. Citsanzoci cili m’bokosi la mutu wakuti “Linapulumutsa Moyo Wake.”
Muzikumbukila kuti ena amalimbikitsidwa akaona zaka zimene mwakhala mukutumikila Yehova mokhulupilika. Ndinu citsanzo pa nkhani ya kupilila, ndipo khalani otsimikiza kuti “Mulungu si wosalungama kuti angaiwale nchito yanu ndiponso cikondi cimene munacisonyeza pa dzina lake, potumikila oyela ndipo mukupitiliza kuwatumikila.”—Aheb. 6:10.
KHALANI NDI ZOCITA ZAMBILI MMENE MUNGATHELE
Kafuku-fuku aonetsa kuti amuna ndi akazi ambili okalamba amene amayesetsa kuthandiza ena, amakhala ndi thanzi labwino, amakwanitsa kuganiza bwino ndiponso amakhala ndi moyo wautali.
Koma kucitila ena zabwino sikungacotseletu mabvuto a ukalamba. Ndi Ufumu wa Mulungu wokha umene udzawathetse. Udzacita izi mwa kucotsapo ucimo umene umabweletsa ukalamba ndi imfa.—Aroma 5:12.
Ngakhale n’telo, mukapitiliza kutumikila Yehova, kumene kuphatikizapo kuthandiza ena kuti am’dziwe, ciyembekezo canu cidzakhala cowala, ndipo mungakhale ndi thanzi labwino. Inu okalamba, dziwani kuti Yehova amayamikila zimene mumakwanitsa kucita pom’tumikila. Nawonso mpingo umakuyamikilani cifukwa ca cikhulupililo canu.