LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w25 December masa. 20-25
  • Mungatani Kuti Tsiku la Ukwati Wanu Likalemekeze Yehova?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mungatani Kuti Tsiku la Ukwati Wanu Likalemekeze Yehova?
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • N’CIFUKWA CIANI MUYENELA KULEMEKEZA YEHOVA?
  • KODI MUNGAMULEMEKEZE BWANJI YEHOVA?
  • KUPEWA ZOBVUTA NDI KUZIGONJETSA
  • Pewani Kutengela Maganizo a Dziko Pokonzekela Cikwati
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2019
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
w25 December masa. 20-25

NKHANI YOPHUNZILA 51

NYIMBO 132 Lomba Ndise Thupi Limodzi

Mungatani Kuti Tsiku la Ukwati Wanu Likalemekeze Yehova?

“Zinthu zonse zizicitika moyenela komanso mwadongosolo.”​—1 AKOR. 14:40.

ZOFUNIKA KUMVETSETSA

Zimene mwamuna ndi mkazi amene akufuna kukwatilana angacite kuti tsiku la ukwati wao likakhale lolemekeza Yehova.

1-2. Kodi Yehova akufuna kuti tsiku la ukwati wanu likakhale lotani?

KODI muli pa citomelo? Ngati n’telo, tikukufunilani zabwino zonse! Mwacionekele, muli yakali-yakali kukonzekela tsiku la ukwatia wanu. Yehova akufuna kuti mukasangalale pa tsikulo komanso pambuyo pake.​—Miy. 5:18; Nyimbo 3:11.

2 Yehova ndi woyenela kulemekezedwa pa tsiku la ukwati wanu. N’cifukwa ciani tikutelo? Nanga mungatani kuti ukwati wanu ukacitike m’njila yolemekeza Yehova? Nkhani ino iyankha mafunso amenewa. Koma ngakhale kuti nkhaniyi yalembedwela amene akufuna kukwatilana, mfundo zake zingathandize tonsefe. Zingatithandize kulemekeza Yehova tikapezeka pa ukwati, kapena ngati amene akulowa m’banja atipempha malangizo a mmene angakonzekelele tsiku la ukwati wao.

N’CIFUKWA CIANI MUYENELA KULEMEKEZA YEHOVA?

3. Kodi n’ciani cimene anthu amene ali pa citomelo ayenela kuganizila akamakonzekela ukwati wao? Nanga n’cifukwa ciani?

3 Amene ali pa citomelo ayenela kukonzekela ukwati wao mogwilizana ndi mfundo za m’Baibo zimene Yehova watipatsa. Cifukwa n’cakuti Yehova ndiye anayambitsa ukwati. Iye ndiye anamanga ukwati woyamba, wa Adamu ndi Hava. (Gen. 1:28; 2:24) Conco, anthu amene afuna kulowa m’banja ayenela kuonetsetsa kuti zimene adzacite pa ukwati wao zikakhale zolemekeza Yehova.

4. N’cifukwa ciani anthu amene akufuna kukwatilana ayenela kucita zinthu zimene zingathandize kuti tsiku la ukwati wao likakhale lolemekeza Yehova?

4 Pali cifukwa cinanso cacikulu cimene ciyenela kukusonkhezelani kuganizila mfundo za Yehova pokonzekela tsiku la ukwati wanu. Cifukwaco n’cakuti Yehova ndi Atate wanu wakumwamba komanso Bwenzi lanu lapamtima. (Aheb. 12:9) Mosakaika konse, simukufuna kusokoneza ubale wanu ndi iye. Simungafune kuti pa tsikuli kapena pa tsiku lina lililonse padzacitike cinthu cimene cingakhumudwitse Bwenzi lanulo. (Sal. 25:14) Mukaganizila zonse zimene Yehova wakucitilani komanso zimene adzakucitileni, mudzaona kuti iye ndi woyeneladi kulandila ulemelelo pa tsiku la ukwati wanu.​—Sal. 116:12.

KODI MUNGAMULEMEKEZE BWANJI YEHOVA?

5. Kodi Baibo ingawathandize bwanji anthu amene ali pa citomelo kukonzekela tsiku la ukwati wao?

5 M’Baibo mulibe malamulo ofotokoza mwachuchuchu mmene mwambo wa ukwati kapena phwando la ukwati liyenela kucitikila. Conco, amene akufuna kulowa m’banja ali ndi ufulu wokonzekela ukwati wao mogwilizana ndi mmene zinthu zilili pa umoyo wao, cikhalidwe cao, komanso malinga ndi zimene akonda. Olambila oona ayenelanso kutsatila zimene boma limafuna pa nkhani ya ukwati. (Mat. 22:21) Ukwati wokonzedwa mogwilizana ndi mfundo za m’Baibo umakondweletsa Yehova ndiponso umacititsa kuti iye alemekezeke. Ndiye, kodi ndi mfundo ziti za m’Baibo zimene muyenela kukumbukila?

6. N’cifukwa ciani anthu ofuna kukwatilana ayenela kutsatila malamulo a boma pa nkhani ya ukwati?

6 Tsatilani malamulo a boma. (Aroma 13:​1, 2) M’maiko ambili, anthu amafunika kutsatila malamulo enaake a boma asanakwatilane. Anthu amene afuna kulowa m’banja ayenela kudziwa kuti malamulo a m’dziko lao amati ciani pa nkhaniyi. Ngati muli ndi mafunso pa nkhaniyi, mungacite bwino kufunsila kwa akulu kuti akuthandizeni.b

7. Kodi ukwati uyenela kucitika motani? Nanga ofuna kulowa m’banja ayenela kucita ciani kuti zimenezi zikacitike?

7 Konzani kuti cocitikaco cikapeleke ulemelelo kwa Mulungu. (1 Akor. 10:​31, 32) Onetsetsani kuti zokacitika pa ukwati wanu zikaonetse kuti pali mzimu wa Mulungu, osati mzimu wa dziko. (Agal. 5:​19-26) Mogwilizana ndi mfundo ya m’Baibo yokhudza umutu, mwamuna ndiye afunika kuonetsetsa kuti tsiku la ukwati n’losangalatsa komanso lolemekezeka. N’ciani cingathandize kuti zimenezi zikatheke? Nkhani ya ukwati yocokela m’Baibo yokambidwa mwacikondi, molimbikitsa ndiponso mwaulemu imathandiza onse opezekapo kumvetsa kuti ukwati ndi mphatso yocokela kwa Mulungu. Imawathandizanso kumvetsa kuti ukwati ndi cocitika cofunika kwambili. N’cifukwa cake anthu ambili amasankha kucita mwambo wa ukwati mu Nyumba ya Ufumu ngati n’kotheka. Ngati mukufuna kugwilitsa nchito Nyumba ya Ufumu, muyenela kulemba kalata ku bungwe la akulu yopempha cilolezo kukali nthawi.

8. Kodi mungacite ciani kuti phwando la ukwati wanu likacitike m’njila yolemekeza Yehova? (Aroma 13:13)

8 Welengani Aroma 13:13. Ngati mwasankha kukhala ndi phwando la ukwati, mungatani kuti phwandolo lisakaonetse mzimu wa dziko? Mau a Cigiliki amene anamasulidwa kuti “maphwando aphokoso” pa mau a m’munsi a pa Aroma 13:13 anali kutanthauza maphwando kumene anthu anali kumwa mowa mwaucidakwa komanso kumene nyimbo zinali kulila mpaka usiku. Ngati mwasankha kuti pa ukwati wanu pakakhale mowa, citani zimene mungathe kuti anthu asakamwe kwambili.c Ngati pa ukwatiwo padzakhala nyimbo, siziyenela kulila mokweza kwambili moti anthu n’kulephela kumvana bwino akamaceza. Sankhani nyimbo mosamala, ndipo onetsetsani kuti mau a nyimbozo sangakhumudwitse munthu aliyense.

9. Ngati amene afuna kulowa m’banja asankha kuti pa ukwati wao pakacitike zosangalatsa, kapena ngati asankha kuti wina akakambepo, n’ciani cimene ayenela kukumbukila?

9 Kodi pa phwando la ukwati wanu padzakhala mwai woti ena akakambepo? Kodi padzakhala zithunzi, mavidiyo, kapena zosangalatsa za mtundu wina? Izi zingapangitse kuti phwandolo likhale losaiwalika. Koma onetsetsani kuti zosangalatsazi zikakhale zolimbikitsa. (Afil. 4:8) Dzifunseni kuti: ‘Kodi zosangalatsazi zidzaonetsa kuti opezekapo tawalemekeza? Kodi zidzalemekeza makonzedwe a ukwati?’ Ndipo koposa zonse dzifunseni kuti: ‘Kodi zidzalemekeza Yehova?’ Ngakhale kuti kukamba zoseketsa pa phwando la ukwati si koipa, pewani nthabwala zimene zingadzutse cilakolako ca kugonana mwa anthu opezekapo. (Aef. 5:3) Ngati a m’banja mwanu kapena mabwenzi anu adzakhala ndi mwai wokambapo, auzeni zimene mufuna kuti akapewe kukamba.

10. N’cifukwa ciani amene akufuna kulowa m’banja ayenela kukhala odzicepetsa pokonzekela ukwati wao? (1 Yoh. 2:​15-17)

10 Khalani odzicepetsa. (Welengani 1 Yoh. 2:​15-17) Yehova amayamikila atumiki ake akamacita zinthu zopeleka ulemu kwa iye m’malo mocita zinthu kuti anthu awaone. Conco, Akhristu odzicepetsa amapewa kuononga ndalama zoculuka pofuna “kudzionetsela.” Kodi mungapindule bwanji mukacita phwando la ukwati losalila zambili? Zinthu zidzakuyendelani bwino. Ganizilani citsanzo ca m’bale wina wa ku Norway, dzina lake Mike. Iye anati: “Cifukwa tinacita ukwati wosalila zambili, tinapewa kukhala ndi nkhongole ndipo tinapitiliza kucita upainiya. Ukwati wathu unali wosalila zambili, koma unakhalabe wosangalatsa ndi wosaiwalika.” Mlongo wina wa ku India, dzina lake Tabitha, anakamba kuti: “Popeza kuti ukwati wathu unali wosalila zambili, panali zocepa zofunika kukonzekela kapena zoti n’kusiyanapo maganizo. Conco, tinapewa kudzibweletsela nkhawa zoculuka.”

Zithunzi: Abale ndi alongo akusangalala pa maukwati a Cikhristu kuzungulila dziko lonse. 1. Mkwati ndi mkwatibwi akhala ku pulatifomu m’Nyumba ya Ufumu moyang’ana m’bale amene akukamba nkhani ya ukwati wao. 2. Mwamuna ndi mkazi wake akuyamikila mkwati ndi mkwatibwi pa phwando la ukwati limene likucitikila panja. 3. Mkwati ndi mkwatibwi komanso ena amene apezeka pa phwando la ukwati akutenga cakudya. 4. Mkwati ndi mkwatibwi aimilila pamaso pa m’bale amene akuwakambila nkhani ya ukwati pabwalo.

Kaya timakhala kuti, n’zotheka ukwati wa Cikhristu kukhala wosalila zambili, wosangalatsa, komanso wosaiwalika (Onani ndime 10-11)


11. Kodi ofuna kulowa m’banja angaonetse bwanji kudzicepetsa pa nkhani ya kabvalidwe ndi kudzikongoletsa?(Onaninso zithunzi.)

11 Kodi munasankha kale zimene mudzabvale pa tsiku la ukwati? Mwacionekele, mufuna kudzaoneka bwino kwambili. Ngakhale m’nthawi za m’Baibo, mkwati ndi mwatibwi anali kuyesetsa kubvala zobvala zooneka bwino kwambili. (Yes. 61:10) Zimene mungabvale pa ukwati wanu zingakhale zosiyana ndi zimene mungabvale pa zocitika zina, koma zifunika kukhalabe zaulemu. (1 Tim. 2:9) Musalole kuti kabvalidwe ndi kudzikongoletsa kwanu zikhale zinthu zofunika kwambili kuposa zina zonse pa ukwati wanu.​—1 Pet. 3:​3, 4.

12. N’cifukwa ciani anthu amene akufuna kulowa m’banja ayenela kutsimikiza mtima kupewelatu miyambo yofala m’dela lao imene sigwilizana ndi Malemba?

12 Pewani miyambo yosagwilizana ndi Malemba. (Chiv. 18:4) Masiku ano, pa maukwati nthawi zambili pamacika miyambo yacikunja komanso imene imaphatikizapo zamizimu. Yehova amaticenjeza mosapita m’mbali kuti tiyenela kupewelatu miyambo yodetsa imeneyi. (2 Akor. 6:​14-17) Ngati m’dela lanu muli miyambo yokaikitsa, fufuzani kuti mupeze ciyambi cake. Fufuzaninso mfundo za m’Baibo zimene zingakuthandizeni kupanga cisankho canzelu.

13. Kodi amene akuyembekezela kulowa m’banja angatengele bwanji citsanzo ca Yehova pa nkhani yolandila mphatso?

13 Kodi pa cikhalidwe ca kwanuko, anthu opezeka pa mwambo wa ukwati amayembekezeledwa kupeleka mphatso kwa amene akulowa m’banja? Mphatso imene angapeleke ingadalile mmene zacuma zilili kwa iwo. N’zoona kuti Akhristu amalimbikitsidwa kuti azikhala opatsa, ndipo kucita izi kumawabweletsela cimwemwe. (Miy. 11:25; Mac. 20:35) Komabe, sitiyenela kupangitsa anthu oitanidwa kukakamizika kuti apeleke mphatso. Sitiyenelanso kuwapangitsa kumva kuti sitinaiyamikile mphatso yao cifukwa si yodula. Timatengela citsanzo ca Yehova mwa kuyamikila zilizonse zimene ena atipatsa mwa kufuna kwao osati mokakamizika.​—2 Akor. 9:7.

KUPEWA ZOBVUTA NDI KUZIGONJETSA

14. Ndi zobvuta ziti zimene anthu ofuna kulowa m’banja amakumana nazo?

14 Pamene mukukonzekela ukwati umene udzalemekeza Yehova, mungakumane ndi zobvuta. Mwacitsanzo, zingakhale zobvuta kwa inu kukonzekela ukwati wosalila zambili. Mwamuna wina wa ku Solomon Islands, dzina lake Charlie, anakamba kuti: “Zinatibvuta kwambili kusankha anthu oti tiwaitanile ku phwando la ukwati. Tili ndi mabwenzi ambili ndipo pa cikhalidwe cathu, aliyense amayembekezela kuti adzaitanidwa.” Tabitha, yemwe tam’chula m’ndime 10, anati: “Kudela kwathu n’zofala kucita maphwando aukwati okhala ndi anthu ambili. Zinawatengela nthawi makolo athu kuti agwilizane ndi cisankho cathu coitanila anthu 100 okha.” Mlongo wina wa ku India, dzina lake Sarah, anakamba kuti: “Anthu ena amadela nkhawa kwambili za mmene ena adzawaonela. Safuna kuoneka ngati otsika kapena osauka. Azisuweni anga anacita maphwando aukwati apamwamba moti inenso n’nayamba kuganiza kuti ndifunika kucita phwando lapamwamba kwambili kuposa iwo.” Kodi n’ciani cingakuthandizeni kugonjetsa zobvuta ngati zimenezi?

15. N’cifukwa ciani pemphelo ndi lofunika kwambili pamene mukukonzekela ukwati wanu?

15 Muzipemphela kawili-kawili pamene mukukonzekela ukwati. Mungauze Yehova nkhani iliyonse imene yakuthetsani nzelu kapena mmene mukumvela. (Afil. 4:​6, 7) Mungam’pemphe kuti akuthandizeni kupanga zisankho zabwino komanso kuti akuthandizeni kukhala odekha pamene muli ndi nkhawa. Mungam’pemphenso kuti akuthandizeni kukhala wolimba mtima ngati mwasankha kucita zinthu mosiyana ndi ena. (1 Pet. 5:7) Mukamaona Yehova akukuthandizani, mudzayamba kum’dalila kwambili. Tabitha, yemwe tam’chulako kale, anati: “Ine ndi mwamuna wanga tisanakwatilane, tinali ndi nkhawa yakuti tizisemphana maganizo tikamakonzekela ukwati wathu. Tinalinso ndi nkhawa yakuti tizikangana ndi acibale athu. Conco, nthawi zonse tikamakambilana za ukwati wathu, tinali kuyamba ndi pemphelo. Tinaonadi thandizo la Yehova, ndipo tinakhala ndi mtendele pakati pathu komanso pocita zinthu ndi acibale athu.”

16-17. Kodi kukambilana bwino kungakuthandizeni bwanji pomwe mukukonzekela ukwati?

16 Muzikambilana mokoma mtima komanso momveka bwino. (Miy. 15:22) Pokhala kuti mukukonzekela kulowa m’banja, pali zisankho zambili zimene muyenela kupanga. Izi ziphatikizapo kusankha tsiku la ukwati, kupanga bajeti, kusankha anthu oitanila, ndi zina zotelo. Musanapange cigamulo, kambilanani malingalilo amene muli nao. Kambilananinso mfundo za m’Baibo komanso malangizo amene mwalandila kucokela kwa abale ndi alongo okhwima kuuzimu. Pofotokoza zimene mufuna, khalani okoma mtima, oganiza bwino komanso ololela. Ngati makolo anu kapena acibale apafupi akupemphani kuti pa ukwati wanu pakakhale zinazake, yesani kucita zimene apempha ngati sizikusemphana ndi mfundo za m’Baibo. Musaiwale kuti kwa iwonso tsiku la ukwati wanu ndi cocitika capadela. Ngati simungathe kucita zimene akupemphani, afotokozeleni mosamala zifukwa zimene simungacitile zimenezo. (Akol. 4:6) Afotokozeleni momveka bwino acibale anu kuti colinga canu cacikulu n’cakuti ukwati wanu ukakhale wosangalatsa komanso wolemekeza Yehova.

17 Kufotokozela makolo anu zimene mwasankha kungakhale kobvuta maka-maka ngati sali m’coonadi. Koma n’zotheka kuwathandiza kumvetsa zisankho zanu. M’bale wina wa ku India, dzina lake Santhosh, anati: “Acibale athu anali kufuna kuti pa ukwati wathu tikacite miyambo ya ci Hindu. Tinawafotokozela zimene tinasankha koma zinawatengela nthawi kuti agwilizane nazo. Tinacitako zina zimene anatipempha titaona kuti sizingakhumudwitse Yehova. Mwacitsanzo, pa phwando la ukwati tinacotsapo zakudya zimene ife tinali kufuna n’kuikapo zimene iwowo anali kufuna. Tinasankhanso kuti pasakhale kuimba kapena kubvina cifukwa sanazizolowele.”

18. N’ciani cingakuthandizeni kuti zinthu zikayende bwino pa tsiku la ukwati wanu? (1 Akorinto 14:40) (Onaninso cithunzi.)

18 Konzekelani bwino. Kucita zinthu mwadongosolo kudzakuthandizani kucepetsa nkhawa pa tsiku la ukwati wanu. (Welengani 1 Akorinto 14:40.) M’bale wina wa ku Taiwan, dzina lake Wayne, anati: “Kutatsala masiku ocepa kuti ukwati wathu ucitike, tinakumana ndi anthu amene anadzipeleka kuti atithandize pa ukwatiwo. Tinakambilana ndi kuyeseza mmene mbali zina zidzafunika kucitikila pofuna kutsimikizila kuti zonse zikayende bwino. Kuti mukaonetse ulemu kwa anthu amene mwaitana, mukayesetse kusunga nthawi.”

Mwamuna ndi mkazi amene ali pa citomelo akukonzekela ukwati limodzi ndi mabwenzi ao amene adzawathandize. M’bale akuwaonetsa tabuleti lomwe lionetsa mmene anthu adzakhalile pa phwando la ukwati.

Kukonzekela bwino kungathandize kuti zinthu zikayende bwino pa tsiku la ukwati (Onani ndime 18)


19. Kodi mungatani kuti zinthu zikayende mwadongosolo pa phwando la ukwati wanu?

19 Kuganizilatu zimene zingacitike kungakuthandizeni kupewa mabvuto. (Miy. 22:3) Mwacitsanzo, ngati kumene mumakhala anthu ali ndi cizolowezi cofika pa phwando la ukwati ngakhale kuti sanaitanidwe, ganizilani zimene mungacite kuti zimenezi zisadzacitike. Uzani acibale anu amene si mboni zimene zidzacitike pa ukwati wanu, komanso afotokozeleni mmene mumaonela miyambo ina ya ukwati. Mungawaonetsenso nkhani imene ili pa jw.org ku Chichewa ya mutu wakuti “Kodi pa Ukwati wa Mboni za Yehova Pamachitika Zotani?” Pofuna kuti zinthu zisakasokonezeke pa phwando la ukwati, mungasankhe m’bale wokhwima mwauzimu kuti akakhale ‘woyang’anila phwando.’ (Yoh. 2:8) Mukamufotokozela bwino-bwino mmene mukufunila kuti zinthu zonse zikayendele pa ukwati wanu, angakuthandizeni kuti zinthu zikacitike mwaulemu komanso mmene munazikonzela.

20. Kodi amene akulowa m’banja sayenela kuiwala ciani za ukwati wao?

20 Mwina mungazizile m’nkhongono mukaganizila zonse zimene muyenela kucita pokonzekela ukwati wanu. Koma musaiwale kuti ukwati wanu udzacitika pa tsiku limodzi lokha. Tsikulo n’ciyambi cabe ca umoyo wosangalatsa wotumikila Yehova monga banja. Cotelo citani zonse zimene mungathe kuti ukwati wanu ukakhale wosalila zambili komanso wolemekezeka. Dalilani Yehova. Mwa thandizo lake, mudzatha kukonzekela ukwati umene muzidzaukumbukila ndi mtima wacimwemwe popanda kudziimba mlandu.​—Sal. 37:​3, 4.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • N’cifukwa ciani anthu amene akulowa m’banja ayenela kulemekeza Yehova pa tsiku la ukwati wao?

  • Kodi amene akulowa m’banja angacite ciani kuti tsiku la ukwati wao likakhale losangalatsa komanso lolemekezeka?

  • Kodi kucita ukwati wosalila zambili kungawathandize bwanji amene akulowa m’banja?

NYIMBO 107 Cikondi ca Umulungu

a KUFOTOKOZELA MAU ENA: M’zikhalidwe zambili, ukwati umaphatikizapo mwambo wolumbilitsa mwamuna ndi mkazi amene akukwatilana. Iwo amalumbila kuti adzakhala limodzi kwa moyo wao wonse. Pambuyo pake, pangakhale phwando la ukwati. Anthu amene amakhala m’madela amene anthu sacita mwambo wa ukwati kapena phwando la ukwati, angapindulebe mwa kutsatila mfundo za m’Baibo pa tsiku la ukwati wao.

b Kuti mudziwe mmene Mkhristu ayenela kuonela malamulo a boma pa nkhani ya ukwati, onani nkhani yakuti “Ukwati Wolemekezeka kwa Mulungu ndi kwa Anthu” mu Nsanja ya Olonda ya Chichewa ya October 15, 2006.

c Onani vidiyo yakuti Kodi Niikeponso Moŵa? pa jw.org

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2026)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani