Kodi Mukukumbukila?
Kodi munawelenga mosamala magazini a Nsanja ya Mlonda a caka cino? Ngati n’telo, yesani kupeza mayankho a mafunso otsatilawa:
N’ciani cimatilimbikitsa kupatsa Yehova ulemelelo?
Timam’patsa ulemelelo cifukwa timam’konda ndi kum’lemekeza kwambili. Cifukwa cinanso n’cakuti timafuna kuti ena am’dziwe.—w25.01, tsa. 3.
Kodi tingatani kuti tikulitse mtima wokhululuka, munthu wina akatikhumudwitsa?
Tisangodzipanga pofuna kuonetsa monga sitinakhumudwe. Koma tiyenela kupewa kukhala cikwiyile ndi kusunga cakukhosi. Tikatelo, tidzapewa kucita zinthu molamulidwa ndi mkwiyo.—w25.02, mas. 15-16.
N’cifukwa ciani Maliko ndi citsanzo cabwino kwa abale acinyamata?
Maliko analandila utumiki ndi mtima wonse. Ndipo sanabwelele m’mbuyo ngakhale kuti pa nthawi ina ayenela kuti anakhumudwa. Anapalana ubwenzi ndi Paulo komanso Akhristu ena okhwima.—w25.04, tsa. 27.
Kodi Yesu anatanthauza ciani pomwe anapemphela kuti: “Ine ndacititsa kuti iwo adziwe dzina lanu”? (Yoh. 17:26)
Ophunzila a Yesu anali kulidziwa kale dzina la Mulungu. Koma Yesu anawathandiza kum’dziwa bwino mwini dzinalo. Anatelo mwa kuwadziwitsa colinga cake, zocita zake, makhalidwe ake ndi zina zotelo.—w25.05, mas. 20-21.
Kodi kukhala odzicepetsa kumatithandiza kuzindikila ciani?
Timazindikila kuti pali zinthu zina zimene sitidziwa. Mwacitsanzo, sitidziwa pamene mapeto adzafika kapena mmene Yehova adzacitile zinthu pa nthawiyo. Sitidziwanso zobwela mawa. Cinanso, sitingamvetse mofikapo mmene Yehova amatidziwila.—w25.06, mas. 15-18
Tingatani kuti tizipindula tikamawelenga zofalitsa zathu kapena tikamamvetsela nkhani ya anthu onse?
Tingadzifunse kuti: ‘Ndi umboni uti umene akugwilitsa nchito pofuna kutsimikizila kuti zimene akukamba n’zoona? Kodi munkhaniyi muli fanizo limene ndingagwilitse nchito pophunzitsa ena? Kodi ndani angacite nayo cidwi mfundoyi?’—w25.07, tsa. 19.
Tingaphunzilepo ciani za kukhululuka kwa Yehova tikaona mmene anacitila zinthu ndi Davide?
Ngakhale kuti Davide anacita macimo aakulu, Yehova anam’khululukila atalapa mocokela pansi pa mtima. (1 Maf. 9:4, 5) Yehova akakhululukila munthu, samulanga cifukwa ca colakwa cake kapena kum’kumbutsanso za colakwaco.—w25.08, p. 17.
Mungatani ngati munthu amene mukuphunzitsa Baibo akubvutika kumvetsa mfundo inayake?
Ngati mwayesetsa kufotokoza bwino mfundo inayake posewenzetsa Baibo koma wophunzila wanu sakumvetsabe, pitani pena ndipo konzani zoti mudzakambilanenso mfundoyo nthawi ina.—w25.09, tsa. 24.
N’cifukwa ciani Baibo imati ucimo uli ndi “cinyengo camphamvu”? (Aheb. 3:13)
Ucimo ungatikope kuti ticite zinthu zoipa. Ungatipangitsenso kuti tizingokhalila kukaikila. Mwacitsanzo, tingamakaikile zakuti Mulungu amatikondadi.—w25.10, tsa. 16.
N’zinthu zitatu ziti zimene zingatithandize kuti mapemphelo amene timapeleka tili patokha azikhala ocokela pansi pa mtima?
(1) Tiyenela kusinkha-sinkha pa makhalidwe a Yehova. (2) Tiyenela kuganizila zimene tikulimbana nazo panopa n’kuzichula m’pemphelo. Mwacitsanzo, tingapemphe zakuti Yehova atithandize kukhululukila munthu yemwe watilakwila. (3) Tingapemphele kwa nthawi yaitali. Tikatelo m’pamene tingafotokoze bwino za mumtima mwathu.—w25.10, mas. 19-20.
Kodi tingawathandize bwanji okalamba?
Tingawayendele kapena kuwatumilako foni. Ngati n’zotheka, tingawapelekeze kucipatala. Tingacitekonso nao ulaliki m’njila zosiyana-siyana.—w25.11, mas. 6-7.
Kodi ndi mfundo ziti zimene anthu amene akulowa m’banja ayenela kutsatila kuti tsiku la ukwati wao likakhale lolemekezeka?
Tsatilani malamulo onse a boma okhudza ukwati. Onetsetsani kuti zocitika pa mwambo wa ukwati ndi pa phwando la ukwati zikuonetsa kuti pali mzimu wa Mulungu. Bvalani zobvala zaulemu, ndipo tsimikizani mtima kuti musalowetsepo miyambo yosemphana ndi Malemba. Kambilanani momveka bwino komanso mwaulemu pamene mukukonzekela ukwati wanu.—w25.12, mas. 21-24.