PHUNZILANI KWA MABWENZI A YEHOVA
Debora
Sewenzetsani mbali ya zocita iyi kuti muphunzile kwa Debora amene anali bwenzi la Yehova.
Makolo, welengani ndi kukambilana Oweruza 4:4-10 ndi ana anu.
Citani daunilodi ndi kupulinta pepala la zocita ili.
Dulani zithunzi za anthu oonetsedwa pa tsamba loyamba, ndipo matani zithunzizo pa tsamba laciwili motsatila malangizo amene apelekedwa. Pamene mukucita izi capamodzi, kambilanani mafunso amene ali mu vidiyo. Ngati muli ndi mapepala ena a zithunzi za m’mavidiyo awa, mungawaike pamodzi ndi kupanga buku.