PHUNZILANI KWA MABWENZI A YEHOVA
Abigayeli
Sewenzetsani mbali ya zocita iyi kuti muphunzile kwa Abigayeli amene anali bwenzi la Yehova.
Makolo, welengani ndi kukambilana 1 Samueli 25:27-35 ndi ana anu.
Citani daunilodi ndi kupulinta pepala la zocita ili.
Dulani zithunzi za anthu oonetsedwa pa tsamba loyamba, ndipo matani zithunzizo pa tsamba laciwili motsatila malangizo amene apelekedwa. Pamene mukucita izi capamodzi, kambilanani mafunso amene ali mu vidiyo. Ngati muli ndi mapepala ena a zithunzi za m’mavidiyo awa, mungawaike pamodzi ndi kupanga buku.