PHUNZILANI KWA MABWENZI A YEHOVA
Yoswa ndi Kalebe
Sewenzetsani mbali ya zocita iyi kuti muphunzile kwa Yoswa ndi Kalebe amene anali mabwenzi a Yehova.
Makolo, welengani ndi kukambilana Numeri 13:30–14:10 ndi ana anu.
Citani daunilodi ndi kupulinta pepala la zocita ili.
Dulani zithunzi za anthu oonetsedwa pa tsamba loyamba, ndipo matani zithunzizo pa tsamba laciwili motsatila malangizo amene apelekedwa. Pamene mukucita izi capamodzi, kambilanani mafunso amene ali mu vidiyo. Ngati muli ndi mapepala ena a zithunzi za m’mavidiyo awa, mungawaike pamodzi ndi kupanga buku.