LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
Tulukani
Loŵani
LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Takulandilani
Ici ni cida cofufuzila m'mabuku olembewa na Mboni za Yehova mu vitundu volekana-lekana.
Ngati mufuna kucita daunilodi, yendani pa jw.org.
  • Lelo

Citatu, October 1

Nzelu yocokela kumwamba . . . ndi yokonzeka kumvela.​—Yak. 3:17.

Kodi kukhala womvela kumakuvutani? Davide nayenso, zinali kumuvuta nthawi zina. Ndiye cifukwa cake anapemphela kuti: “Ndipatseni mtima wofunitsitsa kukumvelani.” (Sal. 51:12) Davide anali kukonda Yehova. Ngakhale n’telo, nthawi zina Davide zinali kumuvuta kuonetsa mtima womvela, ndipo ni mmenenso zilili kwa ise. Cifukwa ciyani? Coyamba, cifukwa cakuti tinatengela mzimu wa kusamvela kwa makolo athu. Caciŵili, Satana amayesetsa kutinyengelela kuti tipandukile Yehova mmene iye anacitila. (2 Akor. 11:3) Cacitatu, tikukhala m’dziko mmene khalidwe la kupanduka lili paliponse, ndipo “mpweya umenewu, kapena kuti kaganizidwe kameneka, tsopano kakugwila nchito mwa ana osamvela.” (Aef. 2:2) Tiyenela kucita zonse zothekha kuti tilimbane na ucimo, Satana, komanso dziko, kuti timvele Yehova komanso aja amene wapatsa ulamulilo. w23.10 6 ¶1

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025

Cinayi, October 2

Iwe wasunga vinyo wabwino mpaka nthawi ino.​—Yoh. 2:10.

Kodi tiphunzilapo ciyani pa cozizwitsa ca Yesu cosandutsa madzi kukhala vinyo? Kukhala odzicepetsa. Yesu sanadzitame pa cozizwitsaco ayi. Ndipo sanadzitamepo pa zonse zimene anali kucita. M’malo mwake, nthawi zonse anali kudzicepetsa mwa kupeleka ulemu na ulemelelo kwa Atate wake. (Yoh. 5:19, 30; 8:28) Tikatengela citsanzo ca Yesu mwa kukhala odzicepetsa, sitidzadzitama pa zilizonse tingakwanitse kucita. Tisadzitame ayi, koma tidzitamandile kuti Mulungu wathu ni wabwino, ndipo tili na mwayi wom’tumikila. (Yer. 9:23, 24) Tizim’patsa ulemelelo wake. Ndi iko komwe, n’ciyani cabwino cimene tingakwanitse kucita popanda thandizo la Yehova? (1 Akor. 1:26-31) Ngati tikhala odzicepetsa, sitidzafuna kudzipezela ulemu pa zabwino zimene tacitila ena. Timakhutila kudziŵa kuti Yehova amaona komanso amayamikila zimene timacita. (Yelekezelani na Mateyu 6:2-4; Aheb. 13:16) Ndithudi, timakondweletsa Yehova tikamatengela Yesu poonetsa kudzicepetsa.​—1 Pet. 5:6. w23.04 4 ¶9; 5 ¶11-12

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025

Cisanu, October 3

Musamaganizile zofuna zanu zokha, koma muziganizilanso zofuna za ena.​—Afil. 2:4.

Mouzilidwa na mzimu woyela, mtumwi Paulo analimbikitsa Akhristu kuti aziganizila zofuna za ena. Kodi tingatsatile motani uphungu umenewu pa misonkhano? Mwa kukumbukila kuti nawonso abale na alongo athu amafuna kupelekapo ndemanga. Ganizilani izi. Mukamaceza na mabwenzi anu, kodi mungamalankhule kwambili moti anzanuwo n’kusoŵa mpata wakuti alankhulepo? Ayi simungatelo. Mumafuna kuti nawonso azilankhulapo. Mofananamo, pamisonkhano tiyenela kusiyilako ena mpata wopelekapo ndemanga. Ndipo njila yabwino koposa yolimbikitsila abale na alongo athu, ni kuwapatsa mpata woonetsa cikhulupililo cawo. (1 Akor. 10:24) Ndemanga zathu zizikhala zazifupi, kuti ena azikhalanso na mpata wopelekapo ndemanga. Ngakhale popeleka ndemanga yaifupi, pewani kukamba mfundo zambili. Musacite kukombelatu mfundo zonse m’ndime, moti ena n’kusoŵa ndemanga yopelekapo. w23.04 22-23 ¶11-13

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025
Takulandilani
Ici ni cida cofufuzila m'mabuku olembewa na Mboni za Yehova mu vitundu volekana-lekana.
Ngati mufuna kucita daunilodi, yendani pa jw.org.
  • Cinyanja
  • Gawilani
  • Makonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenela Kutsatila
  • Mfundo Yosunga Cisinsi
  • Kusunga Cinsinsi
  • JW.ORG
  • Loŵani
Gawilani