Cinayi, October 2
Iwe wasunga vinyo wabwino mpaka nthawi ino.—Yoh. 2:10.
Kodi tiphunzilapo ciyani pa cozizwitsa ca Yesu cosandutsa madzi kukhala vinyo? Kukhala odzicepetsa. Yesu sanadzitame pa cozizwitsaco ayi. Ndipo sanadzitamepo pa zonse zimene anali kucita. M’malo mwake, nthawi zonse anali kudzicepetsa mwa kupeleka ulemu na ulemelelo kwa Atate wake. (Yoh. 5:19, 30; 8:28) Tikatengela citsanzo ca Yesu mwa kukhala odzicepetsa, sitidzadzitama pa zilizonse tingakwanitse kucita. Tisadzitame ayi, koma tidzitamandile kuti Mulungu wathu ni wabwino, ndipo tili na mwayi wom’tumikila. (Yer. 9:23, 24) Tizim’patsa ulemelelo wake. Ndi iko komwe, n’ciyani cabwino cimene tingakwanitse kucita popanda thandizo la Yehova? (1 Akor. 1:26-31) Ngati tikhala odzicepetsa, sitidzafuna kudzipezela ulemu pa zabwino zimene tacitila ena. Timakhutila kudziŵa kuti Yehova amaona komanso amayamikila zimene timacita. (Yelekezelani na Mateyu 6:2-4; Aheb. 13:16) Ndithudi, timakondweletsa Yehova tikamatengela Yesu poonetsa kudzicepetsa.—1 Pet. 5:6. w23.04 4 ¶9; 5 ¶11-12
Cisanu, October 3
Musamaganizile zofuna zanu zokha, koma muziganizilanso zofuna za ena.—Afil. 2:4.
Mouzilidwa na mzimu woyela, mtumwi Paulo analimbikitsa Akhristu kuti aziganizila zofuna za ena. Kodi tingatsatile motani uphungu umenewu pa misonkhano? Mwa kukumbukila kuti nawonso abale na alongo athu amafuna kupelekapo ndemanga. Ganizilani izi. Mukamaceza na mabwenzi anu, kodi mungamalankhule kwambili moti anzanuwo n’kusoŵa mpata wakuti alankhulepo? Ayi simungatelo. Mumafuna kuti nawonso azilankhulapo. Mofananamo, pamisonkhano tiyenela kusiyilako ena mpata wopelekapo ndemanga. Ndipo njila yabwino koposa yolimbikitsila abale na alongo athu, ni kuwapatsa mpata woonetsa cikhulupililo cawo. (1 Akor. 10:24) Ndemanga zathu zizikhala zazifupi, kuti ena azikhalanso na mpata wopelekapo ndemanga. Ngakhale popeleka ndemanga yaifupi, pewani kukamba mfundo zambili. Musacite kukombelatu mfundo zonse m’ndime, moti ena n’kusoŵa ndemanga yopelekapo. w23.04 22-23 ¶11-13
Ciŵelu, October 4
Ndimacita zinthu zonse cifukwa ca uthenga wabwino, kuti ndilalikile uthengawu kwa anthu ena.—1 Akor. 9:23.
Zinthu zikasintha pa umoyo wathu, kuthandizabe ena n’kofunika kwambili, maka-maka mwa kulalikila. Tizikhala ololela pa utumiki wathu. Timakumana na anthu a zikhulupililo na maganizo osiyana-siyana, komanso ocokela kosiyana-siyana. Mtumwi Paulo anali wololela, ndipo tingatengeleko citsanzo cake. Yesu anaika Paulo kukhala ‘mtumwi wotumidwa kwa mitundu ina.’ (Aroma 11:13) Pa utumiki wake umenewo, Paulo analalikila kwa Ayuda, Agiriki, anthu ophunzila, alimi osauka, anyanchito a boma, komanso mafumu. Kuti awafike pa mtima anthu onsewo, Paulo ‘anakhala zinthu zonse kwa anthu osiyanasiyana.’ (1 Akor. 9:19-22) Poganizila cikhalidwe na zikhulupililo za anthu amene anali kuwalalikila, mtumwi Paulo anasintha njila yolalikila. Nafenso tingakhale alaliki ogwila mtima tikamakhala okonzeka kusintha ulaliki wathu kuti ugwilizane na munthu amene tapeza. w23.07 23 ¶11-12